Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/04 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 11/04 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu November: Gaŵirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati eninyumba anena kuti alibe ana, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Pogaŵira buloshali khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba. December: Gaŵirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe gaŵirani mabuku ena, kuphatikizapo Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January: Gaŵirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Tidzagaŵira buku la Yandikirani kwa Yehova.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa December 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Akatha kuŵerengerako, mukalengeze kumpingo poŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Mipingo iyambe kufunsira mavoliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2004 pa oda yawo ya mabuku yotsatira. Mavoliyumuŵa adzakhala m’Chingelezi ndi m’Chifalansa. Kufikira pamene mavoliyumuŵa adzakhalapo ndi kutumizidwa azidzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo. Mavoliyumu ndi zinthu zofunsira mwapadera.

◼ Kuyambira mlungu wa May 23, 2005, tidzayamba kuphunzira bulosha la Dikirani! pa Phunziro la Buku la Mpingo.

◼ Ofesi ya nthambi imafunika kukhala ndi maadiresi ndi manambala a telefoni amene akugwira ntchito panopo a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse m’kaundula wake. Komiti ya Utumiki ya Mpingo iziti zimenezi zikangosintha nthaŵi ina iliyonse, izilemba fomu ya Kusintha Adiresi ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi. Zimenezi zikuphatikizapo kusintha kwa manambala a telefoni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena