Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tiyenera kusamalira motani ntchito za mpingo?
Mpingo wa anthu a Yehova umachita zinthu mwadongosolo chifukwa chakuti anthu ake ali ogwirizana. (1 Akor. 14:33, 40) Talingalirani zimene zimafunika kuti msonkhano umodzi wokha wa mpingo ukhalepo. Kupatula pa pulogalamu yeniyeniyo, pamakhala zochitika zambiri msonkhanowo usanayambe komanso ukangotha pamene abale ndi alongo amakhala akusamalira ntchito zosiyanasiyana. Ntchito zina zimene zimasamalidwa mwam’seri nazonso n’zofunika kwambiri. Kodi aliyense wa ife angathandize nawo motani?
Dziperekeni. Amene ali ndi mtima wodzipereka amakhala ndi zochita zambiri. (Sal. 110:3) Samalani odwala ndi okalamba. Thandizani kuyeretsa pa Nyumba ya Ufumu. Pali ntchito zambiri zothandiza zimene tingachite popanda wina kuchita kutipempha. Timangofunikira kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza basi.
Tumikirani modzichepetsa. Anthu odzichepetsa amakonda kutumikira anzawo. (Luka 9:48) Kudzichepetsa kudzatiteteza kuti tisadziunjikire maudindo kuposa amene tingakwanitse kuwasamalira. Kuwonjezera apo, kudzichepetsa kudzatithandiza kuti tisagwiritse ntchito udindo wathu molakwika.—Miy. 11:2.
Khalani wodalirika. Mu Israyeli wakale, Mose anamulimbikitsa kuti asankhe amuna odalirika kuti asamalire maudindo a ntchito zina. (Eks. 18:21) Khalidwe limeneli n’lofunikanso masiku ano. Samalirani udindo uliwonse umene mwapatsidwa ndi mtima wonse. (Luka 16:10) Ngati mukuona kuti simukwanitsa kusamalira ntchito inayake imene mwapatsidwa, onetsetsani kuti mwakonza zoti munthu wina adzasamalire ntchitoyo panthaŵi imene inu kulibe.
Chitani zimene mungathe. Akristu amalimbikitsidwa kugwira ntchito ndi mtima wonse ngakhale pantchito zina zolembedwa. (Akol. 3:22-24) Ndiye pali chifukwa chachikulu chochitira zimenezi pamene tikugwira ntchito yopititsa patsogolo kulambira koona. Ngakhale pamene ntchitoyo ikuoneka ngati yosafunikira kwenikweni, mpingo umadala tikaigwira bwinobwino.
Ntchito iliyonse imene tapatsidwa imatipatsa mwayi woonetsa chikondi chathu kwa Yehova ndi kwa abale anthu. (Mat. 22:37-39) Ndiyetu tiyeni tisamalire mokhulupirika ntchito iliyonse imene tapatsidwa.