Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/05 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 1/05 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu December: Gawirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe gawirani mabuku ena, kuphatikizapo Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January: Gaŵirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Tidzagawira buku la Yandikirani kwa Yehova. March: Gawirani bulosha la Dikirani! Ngati anthu aonetsa chidwi chenicheni asonyezeni buku la Chidziwitso ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. April: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu chidwi, kuphatikizanso amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo, yesetsani kuwagawira buku la Lambirani Mulungu. Cholinga chathu chikhale kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, makamaka ndi anthu amene anaphunzira kale buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji.

◼ Oyang’anira madera adzayamba kukamba nkhani ya onse yatsopano yakuti “Chitani Mwanzeru M’dziko Lopanda Nzeru.” Adzayamba tsiku lililonse kuyambira February mpaka March 6.

◼ Mipingo iyenera kukonza dongosolo loyenera lodzachita Chikumbutso chaka chino Lachinayi, pa March 24, dzuwa litalowa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumira, musayendetse zizindikiro za Chikumbutso kufikira dzuwa litalowa. Funsani odziwa za nyengo kwanuko kuti mudziwe nthawi yolowera dzuwa m’dera lanu. Ngakhale kuti ndi bwino ngati mpingo uliwonse ungamachite Chikumbutso pawokha, izi sizitheka nthawi zina. Ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mpingo umodzi kapena ingapo ingapeze malo ena odzagwiritsa ntchito madzulo amenewo. Ngati kungatheke, tikupereka malingaliro akuti mapulogalamu akatha pazipita mphindi zosachepera 40 ena asanayambe, kuti onse apindule mokwanira ndiponso kupeza nthawi yocheza ndi alendo ndi kulimbikitsa atsopano. Bungwe la akulu liyenera kukonza dongosolo lokomera mpingowo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena