Yesani Ulaliki Wosavuta Kuusintha
Kuchita chidwi ndi anthu kudzatithandiza kuti tiyesetse kuzindikira mavuto awo ndi kuwasonyeza mmene Ufumu udzathetsere mavuto onse amene akukumana nawo. (Afil. 2:4) Ulaliki wosavuta umene ofalitsa ena auona kukhala wogwira mtima ndi wom’pempha mwininyumba kufotokoza maganizo ake pa zithunzi za Paradaiso za m’mabuku athu, pamasamba osonyezedwa pamwambapa kulamanja kwa tsamba lino. Mukhoza kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito ena mwa mawu oyamba otsatirawa:
◼ “Kodi mukuganiza kuti tidzaonadi anthu akusangalala ndi moyo ngati uyu umene ausonyeza apawu?”
◼ “Tonsefe tingakonde kuti ana anthu asangalale ndi dziko ngati ili alisonyeza apali. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chikufunika kuti dziko ngati limeneli likhalepo?”
◼ “Ichi ndi chitsanzo chosonyeza mmene dziko lizidzaonekera chifuno cha Mulungu chikadzachitika pano padziko lapansi monga kumwamba. Kodi mukuonapo chilichonse chimene chikusiyana ndi moyo wamasiku anowu?”
◼ “Kodi mukufuna kudzakhala ndi moyo m’dziko ili alisonyeza apali. [Yembekezani ayankhe.] Kodi mukuganiza kuti zimenezi zidzachitika m’nthawi yathu ino?”
Mvetserani mwatcheru mayankho a munthuyo, ndipo mwaulemu m’funseni funso lina lowonjezera kapena awiri kuti mudziwe maganizo ake. Ngati ena angayankhe kuti sakufuna kudzakhala ndi moyo m’dziko limene alisonyezalo kapena kuti sakhulupirira kuti zimenezo zingatheke, musafulumire kugamula kuti alibe chidwi. Yesani kuwafunsa mwanzeru chifukwa chimene amaganizira mmene akuneneramo. Zimene angayankhe pamenepo zikhoza kuvumbula nkhawa yaikulu imene ali nayo chifukwa cha mavuto ochuluka omwe anthu akulephera kuwathetsa amene anthu onse akukumana nawo.—Ezek. 9:4.
Mukadziwa mavuto amene mwininyumba ali nawo, sinthani ulaliki wanu mogwirizana ndi mavuto akewo. M’sonyezeni mfundo yaikulu ya uthenga wa Ufumu imene ikukhudza mavuto akewo mwachindunji. Werengani lemba limodzi kapena awiri amene akukhudza vuto limene akuda nalo nkhawalo. (Onani mfundo zimene zili kudzanja lamanjazo.) Muloleni adzionere yekha zimene Mawu a Mulungu amanena. Ngati waonetsa chidwi, gawirani buku ndi kukonza zoti mudzabwerenso. Pitirizani kukulitsa chidwi chimene anachionetsa pa kukambirana kwanu koyamba.
[Bokosi patsamba 6]
Zitsanzo za Zithunzi za Paradaiso
Buku la Mphunzitsi Waluso: masamba 251 mpaka 254
Buku la Chidziŵitso: masamba 4 ndi 5, 188 ndi 189
Bulosha la Mulungu Amafunanji: masamba 11 ndi 13
Buku la Mtendere Weniweni: tsamba 98
Buku la Lambirani Mulungu: masamba 92 ndi 93
[Bokosi patsamba 6]
Zimene Anthu Amada Nazo Nkhawa
Boma losathandiza
Chinyengo, kusowa chilungamo
Imfa, kulira
Kuchitira nkhanza nyama
Kutha kwa makhalidwe abwino
Kuvutika maganizo
Kuwononga dziko
Matenda, kulumala
Njala, kusowa kwa zakudya m’thupi
Nkhondo, uchigawenga
Nyumba, mavuto a zachuma
Tsankho
Umphawi, kuponderezana
Upandu, chiwawa