Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/96 tsamba 8
  • Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Maganizo Otsimikiza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Maganizo Otsimikiza
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Kulalikira Uthenga Wabwino Mwachangu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Mmene Mungagawire Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 9/96 tsamba 8

Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Maganizo Otsimikiza

1 Ife tonse timafuna kupeza chimwemwe ndi chikhutiro pa zimene timachita, makamaka pantchito ya kupanga ophunzira. Kodi nchiyani chimene chimatipatsa chikhutiro chimenecho? Chimayamba mwa kukhala kwathu ndi maganizo otsimikiza pamene tili otanganitsidwa ndi ntchito yoyenera ya kuthandiza ena. (Miy. 11:25) Kalalikidwe kathu ka uthenga wabwino kayenera kusonyeza kuti tikukhulupiriradi zimene tikunena. Ngati tilankhula kuchokera mumtima, pamenepo kuona mtima kwathu ndi kukhulupirira kwathu zidzaonekera. (Luka 6:45) Mwa kuyeseza ulaliki wathu, tidzakhala ndi chidaliro chachikulu polankhula kwa anthu m’gawo. Zimenezi zidzakhala zofunika kwambiri m’September pamene tikugaŵira buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndi la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Malingaliro otsatirawa angakuthandizeni polalikira uthenga wabwino ndi maganizo otsimikiza.

2 Ambiri ali ndi nkhaŵa ponena za kuwonjezereka kwa vuto la upandu. Mungayambe ndi mawu oyambirira pakamutu kakuti “Upandu/Chisungiko” patsamba 14 m’buku la “Kukambitsirana”:

◼ “Tikulankhula ndi anzathu za chisungiko cha munthu aliyense. Tazingidwa ndi upandu wochuluka, ndipo umakhudza moyo wathu. Kodi muganiza nchiyani chikufunika kuti anthu monga inu ndi ine tikhale otetezereka m’makwalala usiku?” Mungaŵerenge Salmo 37:10, 11 ndi kusonyeza madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzadzetsa, mukumagwiritsira ntchito masamba 156-8 m’buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.

3 Ngati munakambitsirana za kuipiraipira kwa mikhalidwe ya dziko paulendo wanu woyamba, mungapitirize mwa kunena kuti:

◼ “Ndikhulupirira kuti mukuvomereza kuti pakufunikira kusintha kwakukulu kuti tidzakhaledi pamtendere. Baibulo limasonyeza kuti Satana ndiye wochititsa mavuto athu wamkulu. Ambiri sadziŵa chimene Mulungu wamlolera kupitiriza kwanthaŵi yaitali. Kodi mukuganiza bwanji?” [Yembekezerani yankho.] Tsegulani patsamba 20, ndime 14 ndi 15, m’buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, ndi kufotokoza chimene Satana sanawonongedwere pakali pano. Ndiyeno ŵerengani Aroma 16:20, amene amasonyeza zimene tingayembekezere patsogolopa.

4 Pogaŵira buku la “Moyo wa Banja,” munganene zotsatirazi paulendo woyamba:

◼ “Ndafika kudzakambitsirana nanu nkhani yonena za vuto lokhudza moyo wa banja. Ife tonse timafuna mabanja athu kukhala achimwemwe, koma tikudziŵa kuti lerolino mabanja ambiri saali otero. Kodi mukuganiza kuti nchiyani chimene chingathandize anthu kupeza chimwemwe chachikulu m’moyo wawo wa banja? [Yembekezerani yankho.] Kodi simukuvomereza kuti kungakhale kopindulitsa kumvetsera zimene Woyambitsa banja akunena? Amapereka malangizo ofunika m’Baibulo. Mapulinsipulo ameneŵa afotokozedwa m’bukuli Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Taonani mbali za nkhani imeneyi zimene zikufotokozedwa. [Sonyezani mpambo wa zamkati.] Bukuli limasonyezanso mankhwala achikhalire a mavuto a anthu. Mosakayikira inu mumawapempherera. Mumalidziŵa bwino Pemphero la Ambuye, si choncho kodi? [Gwirani mawu a Mateyu 6:9, 10.] Chifuniro cha Mulungu nchakuti ufumu wake uchotse kuipa konse padziko lino lapansi ndipo zimenezo zidzathandiza moyo wa banja wa anthu onse amene tsopano akusonyeza chikhulupiriro mu ufumu wa Mulungu.” Gaŵirani bukulo pa chopereka cha nthaŵi zonse.

5 Pobwerera kwa aja amene munagaŵira buku la “Moyo wa Banja,” mwina mungafune kunena motere:

◼ “Poyamba paja tinakambitsirana za nzeru ya kutsatira mapulinsipulo a Baibulo kuti tikhale ndi moyo wa banja wachimwemwe. Kodi muganiza nchiyani chimene chingathandize mabanja lerolino kukhala ogwirizana?” Yembekezerani yankho. Pitani pa ndime 31 patsamba 80, ndi kuŵerenga Akolose 3:9, 10, 12-14. Kambanipo zina zowonjezera kusonyeza mmene chikondi chenicheni chingamangirire mabanja pamodzi. Sonyezani mmene phunziro latsatanetsatane la buku la Moyo wa Banja lingathandizire kuthetsa mavuto.

6 Ngati mukufuna mafikidwe apafupi, mungagwiritsire ntchito mawu oyamba onga aja opezeka patsamba 12 la buku la “Kukambitsirana” :

◼ “Tikulimbikitsa anansi athu kulingalira za mtsogolo mokondweretsa mmene Baibulo limatilonjeza. [Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Kodi zimenezi zikumveka kukhala zabwino kwa inu? [Yembekezerani yankho.] Mutu 19 m’bukuli ukusonyeza madalitso ena amene anthu omvera adzalandira mu Ufumu wa Mulungu.” Ngati ali ndi chidwi, gaŵirani buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.

7 Ngati munakambitsirana za madalitso amene adzakhalako mu ulamuliro wa Ufumu, paulendo wanu wobwereza, munganene kuti:

◼ “Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso abwino kwambiri padziko lapansi ndi kwa anthu. Madalitso ameneŵa asonyezedwa bwino pano pamasamba 12 ndi 13. Kodi mukuona chiyani chimene chikukukondweretsani? [Yembekezerani yankho.] Taganizirani mmene kudzakhalira kukhala m’dziko longa ili.” Ŵerengani ndime 12. Ngati ali ndi chidwi, funsani funso la ndime 13, ndi kukambitsirana yankho lake. Tchulani kuti mutu umenewu ukuyankha mafunso ambiri onena za madalitso a Ufumu ndi kuti mungakonde kudzakambitsirana zimenezo paulendo wanu wotsatira.

8 Monga “antchito anzake a Mulungu,” tili ndi chifukwa chabwino chokhalira otsimikiza popereka uthenga wabwino. (1 Akor. 3:9) Kukhala kwathu ndi maganizo otere kudzadzetsa madalitso ochuluka a Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena