Mawu Oyambirira Ogwiritsira Ntchito mu Uminisitala Wakumunda
Ndemanga: Kuti muzindikire mawu oyambirira oti mugwiritsire ntchito pamene muli muuminisitala wakumunda, zinthu zitatu zifunikira kulingaliridwa mosamalitsa: (1) Uthenga umene tatumidwa kupereka ndiwo “mbiri yabwino yaufumu.” (Mat. 24:14, NW) Ngakhale pamene sitiri kuukambitsirana mwachindunji, tiyenera kukhala tikulingalira kuthandiza anthu kuwona kufunika kwake, kapena mwinamwake kuwachotsera zopinga za kufunitsitsa kwawo kuulingalira. (2) Kudera nkhaŵa kowona mtima ndi ubwino wa anthu amene timakumana nawo kudzatithandiza, monga momwe kunachitira kwa Yesu, kufika mitima. (Marko 6:34) Chikondwerero chowona mtima chotero chingasonyezedwe mwa mkhalidwe wa kumwetulira kwachikondi ndi kwaubwenzi, kufunitsitsa kumvetsera pamene akulankhula ndiyeno kusintha makambitsirano athu kuti agwirizane ndi zimenezo, ndiponso mwa kugwiritsira ntchito kwathu mafunso amene amawalimbikitsa kulankhula momasuka kotero kuti tikhoze kuzindikira bwinopo lingaliro lawo. Akorinto Woyamba 9:19-23 amasonyeza kuti mtumwi Paulo anasintha maperekedwe ake a mbiri yabwino kuti agwirizane ndi mikhalidwe ya anthu amene analankhula nawo. (3) M’mbali zina za dziko, alendo amayembekezeredwa kutsatira machitidwe ena a mwambo asanalongosole chifuno cha kucheza kwawo. Kumaiko ena mwininyumba angayembekezere mlendo wosaitanidwa kunena mofulumira chimene wadzera.—Yerekezerani ndi Luka 10:5.
Mawu oyambirira otsatirapowa amasonyeza mmene Mboni zina zachidziŵitso zimayambira makambitsirano. Ngati mawu oyambirira amene mukuwagwiritsira ntchito tsopano samayambitsa bwino lomwe makambitsirano, yesani ena a malingaliro amenewa. Pamene mutero, inu mosakaikira mudzafuna kuwakamba m’mawu a inumwini. Ndiponso, mudzakupeza kukhala kothandiza kupeza malingaliro kuchokera ku Mboni zina zimene zakhala ndi chipambano chabwino m’kufikira anthu mu mpingo mwanu.
ARMAGEDO
● ‘Anthu ambiri akudera nkhaŵa ndi Armagedo. Iwo amva atsogoleri a dziko akumagwiritsira ntchito dzina limenelo kusonya kunkhondo yotheratu yanyukliya. Kodi inu mukhulupirira kuti Armagedo idzatathauzanji kwa anthu? . . . Ndithudi, dzina lakuti Armagedo latengedwa m’Baibulo, ndipo limatanthauza kanthu kena kosiyana kwambiri ndi zimene liwulo limagwiritsiridwa ntchito mofala kuti limatanthauza. (Chiv. 16:14, 16) Baibulo limasonyezanso kuti pali zinthu zimene ife eni tingachite tiri ncholinga cha kupulumuka. (Zef. 2:2, 3)’ (Wonaninso tsamba 37-42, pamutu wankhani waukulu wakuti “Armagedo.”)
BAIBULO/MULUNGU
● ‘Moni. Mwachidule chabe ndakufikirani kuti ndigawane nanu uthenga wofunika. Chonde imvani zimene ukunena pano m’Baibulo. (Ŵerengani lemba, monga Chivumbulutso 21:3, 4.) Kodi muganizanji za zimenezo? Kodi zikumvekera bwino kwa inu?’
● ‘Tikulankhula ndi anansi athu za kumene kungapezeke chithandizo chogwira ntchito cholakira mavuto a moyo. M’nthaŵi zakale, anthu ambiri ankafunsira ku Baibulo. Koma ife tikukhala m’nthaŵi pamene mikhalidwe iri kusintha. Kodi mukulingalira bwanji? Kodi mukhulupirira kuti Baibulo ndiro Mawu a Mulungu kapena kodi mumalingalira kuti liri bukhu wamba labwino lolembedwa ndi anthu? . . . Ngati liri lochokera kwa Mulungu, kodi muganiza kuti munthu angatsimikizire motani zimenezo?’ (Wonani tsamba 52-62, pamutu waukulu wakuti “Baibulo.”)
● ‘Ndakondwera kukupezani muli panyumba. Ndikugaŵana ndi anansi anga mfundo yolimbikitsa yochokera m’Baibulo (kapena, Malemba Opatulika). Kodi munayamba mwadabwa kuti: . . . ? (Funsani funso limene limatsogolera kumutu wanu wa nkhani wokambitsirana.)’
● ‘Tikulimbikitsa anthu kuŵerenga Baibulo lawo. Kaŵirikaŵiri mayankho a mafunso ofunika amene limapereka amadabwitsa anthu. Mwachitsanzo: . . . (Sal. 104:5; kapena Dan. 2:44; kapena linalake).’
● ‘Tikufikira mwachidule chabe anansi athu lero. Anthu ena amene timalankhula nawo amakhulupirira Mulungu. Ena amakupeza kukhala kovuta kumkhulupirira. Kodi inu mulingalira bwanji? . . . Baibulo limatilimbikitsa kusinkhasinkha tanthauzo lachilengedwe chowoneka. (Sal. 19:1) Uyo amene malamulo ake amalamulira makamu a kumwamba amenewa waperekanso chitsogozo chopindulitsa kwa ife. (Sal. 19:7-9)’ (Wonaninso tsamba 306-313, 74-78, pamitu yaikuluyi “Mulungu” ndi “Chilengedwe.”)
BANJA/ANA
● ‘Tikulankhula kwa anthu amene ali okondweretsedwa ndi mmene tingalakire bwino kwambiri mavuto a moyo wabanja. Tonsefe timayesa kuchita zonse zothekera kwa ife, koma ngati pali kanthu kena kamene kangatithandize kuti tikhale ndi chipambano chokulirapo, tingakakondwerere, kodi sichoncho? . . . (Akol. 3:12, 18-21) Baibulo limaika pamaso pathu chiyembekezo chimene chimalonjeza mtsogolo mwenimweni kaamba ka mabanja athu. (Chiv. 21:3, 4)’
● ‘Tonsefe timafuna kuti ana athu akhale ndi moyo wachimwemwe. Koma kodi muganiza kuti pali chifukwa chabwino choyembekezerera chotulukapo chachimwemwe kaamba ka vuto limene dziko lirimo lerolino? . . . Chotero, kodi ndimtundu wanji wa dziko limene muganiza kuti ana athu adzakhalamo pamene asinkhuka? . . . Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzapanga dziko lapansi lino kukhala malo okongola okhalamo. (Sal. 37:10, 11) Koma kuti kaya ana athu adzakhalamo ndi phande pamlingo waukulu kumadalira pachosankha chimene ife tipanga. (Deut. 30:19)’
CHIKONDI/KUKOMA MTIMA
● ‘Tapeza kuti anthu ambiri ngodera nkhaŵa kwambiri ndi kusoŵeka kwa chikondi m’dziko. Kodi nanunso mumalingalira motero? . . . Kodi nchifukwa ninji muganiza kuti mkhalidwe uli wotero? . . . Kodi mumadziŵa kuti Baibulo lidaneneratu mkhalidwe umenewu? (2 Tim. 3:1-4) Limalongosolanso chifukwa chake. (1 Yoh. 4:8)’
● ‘Dzina langa ndine——. Ndiri mmodzi wa anansi anu. Ndikucheza mwachidule chabe kulankhula ndi anansi anga ponena za kanthu kena kondidetsa nkhaŵa kwambiri, ndipo ndiri wotsimikiza kuti nanunso mwakawona. Kukoma mtima sikuli kokwera mtengo kwambiri, koma kukuwonekera kukhala kosoŵeka kwambiri lerolino. Kodi munayamba mwadabwa chifukwa chake mkhalidwewo ulipo? . . . (Mat. 24:12; 1 Yoh. 4:8)’
CHISALUNGAMO/KUVUTIKA
● ‘Kodi munayamba mwadabwa kuti: Kodi Mulungu amasamaladi za chisalungamo ndi kuvutika zimene anthu akukomana nazo? . . . (Mlal. 4:1; Sal. 72:12-14)’ (Wonaninso mitu yaikulu yakuti “Kuvutika” ndi “Chilimbikitso.”)
MASIKU OTSIRIZA
● ‘Tafika kuti tikambitsirane tanthauzo la zimene zikuchitika motizungulira m’dziko lerolino. Pakati pa anthu ambiri pakhala kuchepachepa kwa chikondwerero mwa Mulungu ndi m’miyezo yake ya moyo yolembedwa m’Baibulo. Zimenezi zasonkhezera kwambiri maganizo a anthu kwa wina ndi mnzake. Chonde tandilolani kugaŵana nanu malongosoledwe awa olembedwa pa 2 Timoteo 3:1-5 ndipo ndiuzeni ngati muganiza kuti ndimo mmene uliridi mkhalidwe wadziko lerolino. (Ŵerengani) . . . Kodi pali chifukwa chirichonse cha kuyembekezerera mikhalidwe yabwinopo mtsogolo? (2 Pet. 3:13)’
● ‘Anthu ambiri amakhulupirira kuti nthaŵi ikuthera dziko lino mofulumira. Amalankhula za nthaŵi yathu kukhala “masiku otsiriza.” Koma kodi munazindikira kuti Baibulo limatiuza mmene tingapulumukire mapeto a dziko lamakono ndi kukhala ndi moyo padziko lapansi limene lidzapangidwa kukhala paradaiso? (Zef. 2:2, 3)’ (Wonaninso tsamba 261-270, pamutu waukulu wakuti “Masiku Otsiriza.”)
Wonaninso “Zochitika Zatsopano” m’mpambo uno wa mawu oyambirira ovomerezedwa.
MOYO/CHIMWEMWE
● ‘Tikuchezera anansi athu kufunafuna anthu amene ali odera nkhaŵa kwambiri ndi tanthauzo la moyo. Anthu ambiri amakhala achimwemwe pang’ono. Koma amakumananso ndi mavuto ambiri. Pamene tikalamba, timazindikira kuti moyo ngwaufupi kwambiri. Kodi nzokhazi zimene moyo walinganizidwira kukhala? Kodi inu mulingaliranji za iwo? . . . (Lankhulani za chifuno choyambirira cha Mulungu monga momwe chinasonyezedwera mu Edene; ndiyeno Yohane 17:3 ndi Chivumbulutso 21:3, 4.)’ (Wonaninso tsamba 289-294, pamutu wankhani waukulu wakuti “Moyo (Life).”)
● ‘Lerolino tikufunsa anansi athu zimene akuganiza pamene aŵerenga m’Mabaibulo awo mawu akuti “moyo wosatha.” Ali okondweretsa mwapadera chifukwa chakuti mawu amenewo amawonekera m’Baibulo nthaŵi zokwanira 40. Kodi moyo wotero ungatanthauzenji kwa ife? . . . Kodi tingaupeze motani? (Yoh. 17:3; Chiv. 21:4)’
● ‘Tikulankhula ndi anthu amene alidi odera nkhaŵa ndi mkhalidwe wa moyo lerolino. Ambirife tiri okondwera kukhala ndi moyo, koma ambiri amadabwa kuti, Kodi moyo wachimwemwe mowonadi ngwotheka? Kodi muganiza bwanji za zimenezo? . . . Kodi mukanati nchiyani chimene chiri chimodzi cha zopinga zazikulu koposa za chimwemwe lerolino? . . . (Sal. 1:1, 2; malemba ena oyenerera ndi zimene mwininyumba akudera nazo nkhaŵa)’
MTSOGOLO/CHISUNGIKO
● ‘Moni. Muli bwanji? . . . Tikuyesayesa kugaŵana ndi anansi athu lingaliro lotsimikizirika lamtsogolo. Kodi mumayesayesa kuwona moyo motero? . . . Kodi mumapeza kuti mikhalidwe ina imapangitsa zimenezi kukhala zovuta kuzichita? . . . Ndapeza kuti Baibulo liri lothandiza kwambiri pa mfundoyi. Iro limalongosola mosabisa mikhalidwe imene iri m’tsiku lathu, koma limafotokozanso tanthauzo lake ndi kutiuza chimene chidzakhala chotulukapo. (Luka 21:28, 31)’
● ‘Moni. Dzina langa ndine——. Kodi lanu ndinu yani? . . . Ndikulimbikitsa achichepere onga inu kulingalira mtsogolo mokondweretsa mmene Baibulo limatilonjeza. (Werengani lemba, longa Chivumbulutso 21:3, 4.) Kodi zimenezo zikumvekera bwino kwa inu?’
NKHONDO/MTENDERE
● ‘Pafupifupi aliyense masiku ano ngwodera nkhaŵa ndi chiwopsezo cha nkhondo yanyukliya. Kodi muganiza kuti tidzawonapo mtendere weniweni padziko lino lapansi? . . . (Sal. 46:8, 9; Yes. 9:6, 7)’
● ‘Ndikufunafuna anthu amene akanakonda kukhala ndi moyo m’dziko lopanda nkhondo. M’zaka za zana lino lokha kwachitika nkhondo mazana ambiri, kuphatikizapo nkhondo zadziko ziŵiri. Tsopano tikuyang’anizana ndi chiwopsezo cha nkhondo yanyukliya. Kodi muganiza kuti chofunika nchiyani ngati nkhondo imeneyi iti ipeŵedwe? . . . (Mika 4:2-4)’
● ‘Tikupeza kuti pafupifupi munthu aliyense akunena kuti akufuna mtendere wadziko. Atsogoleri adziko ambiri amanenanso chomwecho. Nangano, nchifukwa ninji, kuli kovuta kwambiri kuupeza? . . . (Chiv. 12:7-12)’
NTCHITO/KUPEZEKA KWA NYUMBA
● ‘Tinali kulankhula ndi anansi anu za zimene zingachitidwe kutsimikizira kuti padzakhale ntchito ndi nyumba kaamba ka aliyense. Kodi mukhulupirira kuti kuli koyenera kuyembekezera kuti maboma a anthu adzakwaniritsa zimenezi? . . . Koma pali munthu wina amene amadziŵa mmene angathetsere mavuto amenewa; ndiye Mlengi wa anthu. (Yes. 65:21-23)’
● ‘Tikugaŵana ndi anansi athu mfundo yonena za boma labwino. Anthu ambiri akakonda kukhala ndi boma lopanda chinyengo, limene limagawira ntchito ndi nyumba zabwino kwa aliyense. Kodi ndi boma liti limene muganiza kuti lingachite zonsezo? . . . (Sal. 97:1, 2; Yes. 65:21-23)’ (Wonaninso tsamba 62-66, pamutu waukulu wakuti “Boma.”)
PHUNZIRO LABAIBULO LAPANYUMBA
● ‘Ndafika kudzakusonyezani kosi yaulere ya phunziro Labaibulo lapanyumba. Ngati ndingathe, ndingakonde kutenga mphindi zochepa kusonyeza mmene anthu m’maiko okwanira 200 amaphunzirira Baibulo monga timagulu tabanja. Tingagwiritsire ntchito uli onse wa mitu yokambitsirana imeneyi. (Sonyezani mpambo wa zamkatimo kuchokera m’bukhu la phunzirolo.) Kodi ndiuti umene umakukondweretsani mwapadera?’
● ‘Tikusonyeza chothandizira phunziro Labaibulo ichi kwa anansi athu. (Sonyezani bukhulo.) Kodi munayamba mwaliwonapo kale? . . . Ngati muli ndi mphindi zoŵerengeka chabe, ndingakonde kusonyeza mmene lingagwiritsidwire ntchito limodzi ndi kope lanu la Baibulo.’
UFUMU
● ‘Polankhula ndi anansi anga, ndawona kuti ochuluka amalakalaka kukhala ndi moyo pansi pa boma limene lingathetsedi mavuto aakulu amene timayang’anizana nawo lerolino—upandu ndi kukwera mtengo kwa zinthu (kapena chirichonse chimene chiri m’maganizo mwa anthu ambiri panthaŵiyo). Limenelo likakhala lofunika, kodi simukuvomereza? . . . Kodi liripo boma lotero lerolino? . . . Anthu ambiri kwenikweni apempherera boma limene lingachite zinthu zimenezo. Mosakaikira inu mwalipempherera, koma sianthu ambiri amene amaganiza za iro kukhala boma. (Dan. 2:44; Sal. 67:6, 7; Mika 4:4)’ (Wonaninso tsamba 374-382 ndi 62-66, pamitu yankhani yaikulu yakuti “Ufumu” ndi “Boma.”)
● ‘Tikufunsa anansi athu funso. Tikayamikira ndemanga yanu pa iro. Mudziŵa, Yesu anatiphunzitsa kupempherera kuti Ufumu wa Mulungu udze ndi kuti chifuniro Chake chichitidwe padziko lapansi monga kumwamba. Kodi muganiza kuti pemphero limeneli lidzayankhidwa konse kotero kuti chifuniro cha Mulungu chidzachitikadi pano padziko lapansi? . . . (Yes. 55:10, 11; Chiv. 21:3-5)’
● ‘Ndikukambitsirana ndi anansi anga za nkhani imene tonsefe tiyenera kuyang’angizana nayo: Kodi timayanja boma la Mulungu kapena kodi timakonda ulamuliro wa anthu? Chifukwa cha mikhalidwe m’dziko lerolino, kodi muganiza kuti tifunikira kanthu kena koposa zimene anthu atulutsa? . . . (Mat. 6:9, 10; Sal. 146:3-5)’
UKALAMBA/IMFA
● ‘Kodi munayamba mwadabwa chifukwa chake timakalamba ndi kufa? Akamba ena a m’nyanja amakhala ndi moyo zaka mazana angapo. Mitengo ina imakhala zaka zikwi zambiri. Koma anthu amakhala kokha zaka 70 kapena 80 ndiyeno nkufa. Kodi munayamba mwadabwa chifukwa chake? . . . (Aroma 5:12) Kodi mkhalidwe umenewo udzasintha? . . . (Chiv. 21:3, 4)’
● ‘Kodi munayamba mwafunsa kuti: Kodi imfa ndiwo mapeto a zonse? Kapena kodi pali kanthu kena pambuyo pa imfa? . . . Baibulo limayankha bwino lomwe funso lirilonse limene tingakhale nalo ponena za imfa. (Mlal. 9:5, 10) Limasonyezanso kuti pali chiyembekezo chenicheni kaamba ka anthu amene ali ndi chikhulupiriro. (Yoh. 11:25)’ (Wonaninso tsamba 151-157 ndi 80, pamutu wankhani waukulu wakuti “Imfa” ndi “Chilimbikitso.”)
UPANDU/CHISUNGIKO
● ‘Moni. Tikulankhula ndi anthu za nkhani yonena za chisungiko cha munthu aliyense payekha. Pali upandu wochuluka motizinga, ndipo umayambukira miyoyo yathu. Kodi muganiza kuti nthaŵi idzafika pamene anthu onga inu ndi ine adzakhoza kuyenda m’makwalala pausiku ndi kudziwona kukhala osungika? (Kapena, kodi muganiza kuti aliyense ali ndi njira yeniyeni yothetsera vutoli?) . . . (Miy. 15:3; Sal. 37:10, 11)’
● ‘Dzina langa ndine——. Ndimakhala mommuno. Pamene ndinali kudza mamaŵa uno, ndawona kuti aliyense akulankhula za (tchulani upandu waposachedwapa wochitikira m’malowo kapena nkhani ina yodetsa nkhaŵa m’malowo). Kodi inu mukuganizanji nawo? . . . Kodi pali kanthu kalikonse kamene mulingalira kuti kangathandize kupangitsa miyoyo yathu kukhala yosungikadi? . . . (Miy. 1:33; 3:5, 6)’
ZOCHITIKA ZATSOPANO
● ‘Moni. Dzina langa ndine——. Ndine mnansi wanu wochokera (tchulani dzina lakhwalala kapena chigawo). Kodi munawona nkhani pa TV usiku wathawu? . . . Lipoti lija losimba za (tchulani nkhani ina yochitika chatsopano yodetsa nkhaŵa)—kodi mukuiganiza bwanji? . . . Sikuli kwachilendo kumva anthu akufunsa kuti, Kodi dziko lino likumka kuti? Ife monga Mboni za Yehova tikhulupirira kuti tiri mu amene Baibulo limawatcha “masiku otsiriza.” Tawonani malongosoledwe atsatanetsatane awa pa 2 Timoteo 3:1-5.’ (Wonaninso tsamba 261-270.)
● ‘Kodi munaŵerenga izi m’nyuzipepala mlungu uno? (Sonyezani kachigawo koyenelera kodulidwa ka nyuzipepalayo.) Kodi muganiza bwanji . . . ?’
● ‘Ndikakonda kukufunsani funso. Ngati mukasankha, kodi ndi ati a mavuto ambiriwo amene tsopano ali m’dziko amene mukanakonda kuti athetsedwe choyamba? (Pambuyo pa kumva chimene chiri nkhaŵa yaikulu koposa kwa mwininyumbayo, gwiritsirani ntchito chimenecho monga maziko a kukambitsirana kwanu.)’
PAMENE ANTHU AMBIRI ANENA KUTI: ‘NDIRI NDI CHIPEMBEDZO CHANGA’
● ‘Moni, Tikuchezera mabanja onse m’laeni lanu lino (kapena, m’chigawo chino), ndipo tikupeza kuti ambiri a iwo ali ndi chipembedzo chawo. Mosakaikira inunso muli nacho. . . . Koma, mosasamala kanthu za chimene chiri chipembedzo chathu, timayambukiridwa ndi mavuto ambiri ofanana—kukwera mitengo kwa zinthu, upandu, matenda—kodi sichoncho? . . . Kodi mukulingalira kuti pali njira yeniyeni yothetsera zinthu zimenezi? . . . (2 Pet. 3:13; ndi ena otero.)’
PAMENE ANTHU AMBIRI ANENA KUTI: ‘NDIRI WOTANGANITSIDWA’
● ‘Moni. Tikuchezera munthu aliyense m’chigawo chino ndi uthenga wofunika. Mosakaikira inu muli munthu wotanganitsidwa, chotero ndidzalankhula mwachidule.’
● ‘Moni. Dzina langa ndine——. Chifuno cha kufika kwanga ndicho kukambitsirana nanu madalitso a Ufumu wa Mulungu ndi mmene tingawalandirire. Koma ndingathe kuwona kuti muli wotanganitsidwa (kapena, muli pafupi kuchoka). Kodi ndingakusiireni mfundo yachidule chabe?’
M’GAWO LOFOLEDWA KAŴIRIKAŴIRI
● ‘Ndiri wokondwa kukupezani panyumba. Tikuchita kucheza kwathu kwamlungu ndi mlungu m’chitaganya chino, ndipo tiri ndi kanthu kena koti tigaŵane nanu ponena za zinthu zabwino kwambiri zimene Ufumu wa Mulungu udzachitira anthu.’
● ‘Moni. Nkokondweretsa kukuwonaninso. . . . Kodi aliyense m’banja ali bwino? . . . Ndaima pano kugaŵana nanu mfundo yonena za . . . ’
● ‘Moni. Muli bwanji? . . . Ndakhala ndikufunafuna mpata wina wa kulankhula nanu. (Ndiyeno tchulani nkhani yeniyeni imene mukufuna kulankhula.)’