Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera
1 Ambiri a ife takhala ndi chipambano m’kugaŵira magazini ndi kupeza masabusikripishoni. Nkofunika kuti tibwerere ndi kukayesa kusonkhezera chikondwerero chowonjezereka. Chipambano chathu m’kuchita motero chingadalire pa kukonzekera kwathu bwino tisanapange ulendo wobwereza.
2 Kumbukirani kuti anthu ochuluka amalingalira kuti zipembedzo zonse ndi timagulu tachipembedzo zimatsogolera ku chipulumutso. Kope la Nsanja ya Olonda la May 1, 1994, lili ndi nkhani zimene zikufotokoza kaya ngati chipembedzo china chilichonsecho chingakondweretse Mulungu. Nkhani zimenezi zikupereka chidziŵitso chimene chingathandize anthu kudziŵa miyezo ya kulambira ya Mlengi.
3 Ngati munagaŵira kope limeneli la “Nsanja ya Olonda,” mungalinganize za kubwereranso mwa kukagaŵira sabusikripishoni. Munganene kuti:
◼ “Kope lija limene ndinakusiyirani linali ndi nkhani zonena za chipembedzo.” Ndiyeno funsani kuti: “Kodi ndi njira iti imene ili yoyenerera kulambirira Mulungu? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limatiphunzitsa kuti kulambira koona kwazikidwa pa chidziŵitso cholongosoka. Kodi mumadziŵa zimene mneneri wamkulu Yesu Kristu panthaŵi ina anauza mkazi Wachisamariya ponena za kulambira Mulungu?” [Ŵerengani Yohane 4:22.] Mwininyumbayo atayankha funsani mafunso otsatirawa: “Kodi mwinamwake zimenezi zingakhalenso choncho kwa inu? Kodi mwaphunzitsidwa kuti Mulungu Wamphamvuyonse ali ndi dzina la iye mwini, Yehova? (Sal. 83:18) Ndipo ngati mukudzilingalira kukhala Mkristu, kodi mungafotokoze zikhulupiriro zanu kuchokera m’Malemba? Mwa kulandira magazini a Nsanja ya Olonda nthaŵi zonse, mudzathandizidwa kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu.” Ndiyeno gaŵirani sabusikripishoni.
4 Mungafune kugwiritsira ntchito njira ina yogaŵirira masabusikripishoni mwa njira iyi:
◼ “Ndinasangala pakukambitsirana kwathu papitapo ponena za mtsogolo mwa dziko lapansili. Kodi mungayerekezere mmene moyo ukakhalira pano pamene Mulungu athetsa kuipa ndi kuvutika? Taonani mmene Salmo 37:9-11 limanenera za chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi. [Ŵerengani.] Kwazaka zambiri, Nsanja ya Olonda yasonyeza oŵerenga ake chimene Ufumu wa Mulungu udzachitira mtundu wa anthu.” Ndiyeno, mutasonyeza mfundo yakutiyakuti ya m’kope latsopano, gaŵirani sabusikripishoni.
5 Pamene mubwererako, mwinamwake mudzapeza kuti mwininyumbayo amalandira mabuku achipembedzo chake ndipo akukhulupirira kuti zimenezo nzokwanira. Munganene kuti:
◼ “Mosasamala kanthu za chipembedzo chathu, tonsefe timakhudzidwa ndi nkhaŵa zambiri zofanana—upandu, matenda owopsa, nkhaŵa za malo okhala—kodi si choncho? [Mloleni akambepo.] Kodi mulingalira kuti pali chothetsera chenicheni cha mavuto ameneŵa? [Ŵerengani 2 Petro 3:13.] Chifuno cha magazini athu chalembedwa pa tsamba 2 la Nsanja ya Olonda. [Ŵerengani chiganizo chimodzi kapena ziŵiri zosankhidwa.] Anthu ambiri amene sali Mboni za Yehova amakondwa kuŵerenga zofalitsidwa zathu chifukwa cha uthenga wa chiyembekezo umene zili nawo, umene wazikidwa pa Baibulo.” Ngati mwininyumba akuyankha mokondweretsedwa, fotokozani programu yathu ya phunziro la Baibulo.
6 Munganene mwanjira iyi:
◼ “Pamene ndinali pano ulendo wapitawo, tinakambitsirana za ziyembekezo zamtsogolo za dziko lathuli. Kodi mukulingalira motani pa lipoti ili? [Tchulani nkhani zochititsa nkhawa zimene zangochitika kumene.] Pamene anthu amva zinthu zonga zimenezo, zimawachititsa kudabwa za kumene dzikoli likupita, kodi si choncho? Timakhulupirira kuti zinthu zotero zimasonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ onenedweratu m’Baibulo pa 2 Timoteo 3:1-5.” Mutaŵerenga mfundo zazikulu, mungafunse ngati iye waona anthu amene amayenererana ndi mafotokozedwe amenewo. Pitirizani kukambitsiranako pa umodzi wa mitu yaing’ono pa masamba 261-5 a buku la Kukambitsirana.
7 Ngati tikonzekezera bwino ndi kusonyeza chikhumbo chenicheni cha kufuna kuthandiza, tingakhale ndi chidaliro chakuti anthu oona mtima adzamvetsera.—Yoh. 10:27. 28.