Bwererani Kumene Munagaŵira Magazini
1 Yesu analimbikitsa otsatira ake kuchita ntchito yopanga ophunzira. (Mat. 28:19) Zimenezo zimatanthauza zoposa kugaŵira magazini chabe; timafuna kuthandiza anthu kupita patsogolo mwauzimu. Kuti tichite zimenezo tiyenera kubwerera kukapereka chithandizo chowonjezereka kwa awo amene anasonyeza chikondwerero.
2 Ngati munasonyeza nkhani imodzi ya m’magazini paulendo wanu woyamba, kungakhale bwino kukambitsirana nkhani imodzimodziyo pamene mubwerera:
◼ “Pamene ndinafika pano ulendo woyamba, ndinakusonyezani nkhani ya mu Nsanja ya Olonda (kapena Galamukani!) imene inatithandiza kuzindikira kufunika kwa kufufuza m’Baibulo. Chifuno cha Mulungu cha mtsogolo mwabwinopo kwa anthu chazikidwa pa boma lake la Ufumu. Lemba la Mika 4:3, 4 limanena za lonjezo lake lakuti Ufumu umenewu udzathetsa nkhondo zonse.” Pambuyo poŵerenga lembalo, gaŵirani sabusikripishoni.
3 Ngati chikondwerero cha mwininyumba chionekera kukhala chochepa kapena alibe nthaŵi yokambitsirana, mungangosankha kuwonjezera dzina lake pa mpambo wa njira yanu ya magazini:
◼ “Popeza kuti munasonyeza chikondwerero m’magazini amene ndinakusiyirani poyamba paja, ndinaganiza kuti mungakondwere ndi makope atsopano. Ndikhulupirira kuti mudzapeza nkhani iyi kukhala yosangalatsa kwambiri.” Sonyezani nkhani imene mukuganiza kuti idzamsangalatsa. Pemphani kubwereranso ndi makope otsatira.
4 Ngati mwininyumba anaŵerenga magaziniwo ndipo asonyeza chiyamikiro kaamba ka iwo, mungagaŵire sabusikripishoni:
◼ “Popeza mukuonekera kukhala mukusangalala ndi Nsanja ya Olonda, ndakhala wokondwera kukubweretserani makope atsopano pamene angotuluka kumene. Ngati mungakonde, ndingapange makonzedwe kuti adzitumizidwa kwa inu mokhazikika kudzera pa positi kotero kuti mudzilandira kope lililonse.” Kapena mungangonena kuti: “Nsanja ya Olonda idzakuthandizani kuyang’anira zochitika za dziko pamene zikukwaniritsa ulosi wa Baibulo. Imabweretsa uthenga wotonthoza wakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzasintha dziko lapansili kukhala paradaiso wabwino koposa. Mungalandire makope aŵiri a magazini iliyonse pa mwezi kwa chaka chimodzi pa chopereka cha . . . (Tchulani chopereka cha nthaŵi zonse.).”
5 Ngati munagaŵira magazini koma simunapeze mpata wogaŵira sabusikripishoni, konzekerani kuchita zimenezo pa ulendo wobwereza.
Mwachitsanzo, ngati munasiyira magazini munthu wachipembedzo, mungayambe mwa kunena kuti:
◼ “Nkokondweretsa kupeza anthu amene adakali okondweretsedwa ndi Baibulo. Kukuonekera kuti ambiri amaona Baibulo kukhala buku lina chabe. Monga munthu woŵerenga Mawu a Mulungu, kodi ndi mapindu othandiza otani amene uthenga wake wabweretsa m’moyo wanu?” (Pamene mwininyumba ayankha, mvetserani mosamalitsa ndi kupereka ndemanga zolimbikitsa.) Ndiyeno mungapereke ndemanga yakuti ngakhale kuti anthu ambiri amaŵerenga Baibulo, iwo amalephera kupindula chifukwa chakuti samamvetsetsa zimene akuŵerenga, ndipo wonjezerani kuti: “Nsanja ya Olonda yandithandiza kumvetsetsa bwinopo Mawu a Mulungu. Kwenikweni, mamiliyoni apeza kuti yawonjezera mokulira kumvetsetsa kwawo Baibulo.” Ndiyeno sonyezani mwininyumbayo mfundo yosangalatsa m’magaziniwo. Malizani mwa kunena kuti: “Ndili wosangalala kukugaŵirani sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda, imene idzaphatikizapo makope 24 pa chopereka cha . . . (Tchulani chopereka cha nthaŵi zonse.).”
6 Tili ndi magazini osiyanasiyana. Pezani mfundo zosangalatsa m’kope limene mufuna kugwiritsira ntchito. Zidzakuthandizani kulimbikitsa anthu owona mtima kuphunzira zochuluka ponena za zinthu zimene Yesu analamulira.—Mat. 28:20.