Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/05 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira February 14
  • Mlungu Woyambira February 21
  • Mlungu Woyambira February 28
  • Mlungu Woyambira March 7
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 2/05 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira February 14

Nyimbo Na. 174

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kusonyezera chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya February 15 ndi Galamukani! ya March 8. Mwachidule fotokozani mmene tingasinthire zitsanzozo kuti zigwirizane ndi zochitika za m’gawo lanu.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005 pa tsamba 8. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 35: “Nyengo ya Chikumbutso Ndi Nthawi Yochita Zambiri.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Pokambirana ndime 6, phatikizanipo ndemanga zochokera mu Galamukani! ya September 8, 2004, tsamba 12 ndi 13. Lengezani amene alembetsa kuchita upainiya wothandiza. Fotokozani za misonkhano yowonjezera imene yakonzedwa yokonzekera utumiki wakumunda. Limbikitsani onse kuwonjezera zochita zawo zauzimu m’njira zosiyanasiyana m’nyengo ya Chikumbutso imeneyi.

Nyimbo Na. 14 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 21

Nyimbo Na. 31

Mph. 5: Zilengezo za pampingo.

Mph. 20: “Yamikani Yehova Chifukwa cha Chifundo Chake.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Lengezani nthawi ndi malo amene kukachitikire Chikumbutso limodzi ndi dzina la amene adzakambe nkhani ndi mfundo zina zimene zingakhale zofunikira. Pokambirana ndime 4, phatikizanipo chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akuitanira ku Chikumbutso munthu amene amakam’patsira magazini. Perekani timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso pambuyo pa msonkhanowu, ngati munali musanapereke.

Mph. 20: “Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Tchulani deti la msonkhano wadera wotsatira ngati laperekedwa. Amene akufuna kubatizidwa ayenera kudziwitsa woyang’anira wotsogolera pasadakhale. Pendaninso nkhani ya pa tsamba 4 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2004, ya mutu wakuti: “Njira Yatsopano Yobwerezera Zophunziridwa pa Misonkhano Yadera.”

Nyimbo Na. 21 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 28

Nyimbo Na. 42

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a February. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu), sonyezani chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi Galamukani! ya March 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena. Pamapeto pa chitsanzocho, wofalitsayo amuitanire mwini nyumbayo ku Chikumbutso pogwiritsa ntchito tsamba lomaliza la Galamukani! ya March 8.

Mph. 20: Adereni Nkhawa Amene Ali Ofooka. (Mac. 20:35) Pambuyo pokamba mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, kambiranani mwa mafunso ndi mayankho kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2004, tsamba 17 ndi 18, ndime 12 mpaka 16, ngati mmene timachitira pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Uzani mbale amene amatha kuwerenga bwino kuti aziwerenga ndimezo. Cholinga chake chikhale kufuna kuona mmene tingagwiritsire ntchito nkhaniyo mogwirizana ndi Chikumbutso chimene chikubwerachi limodzinso ndi nkhani yapadera ya onse.

Mph. 10: Kodi Chofunika N’chiyani Kuti Munthu Akhale Wofalitsa Wabwino Pampingo? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Sikuti zimachita kufuna kuti mukhale ndi luso linalake la pamwamba; m’malo mwake, tonsefe timangofunika kukhala ndi mtima wofunitsitsa umene umasonyeza chikondi, kudzichepetsa, changu, ndiponso kuyamikira. Pemphani omvera kufotokoza chifukwa chake zinthu zotsatirazi zili zofunika: (1) mtima wansangala, (2) kupezeka pamisonkhano nthawi zonse ndi kutenga nawo mbali, (3) kufunitsitsa kulandira ntchito ndi kuzichita, (4) kugwirizana ndi akulu ndi zimene iwo akonza zokhudza mpingo, (5) mtima wofunitsitsa kuthandiza ena, ndi (6) kutenga nawo mbali mu utumiki wa kumunda nthawi zonse ndiponso kupereka maola mofulumira mwezi uliwonse.

Nyimbo Na. 72 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 7

Nyimbo Na. 12

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kambani mfundo zazikulu zomwe zili m’bokosi lakuti “Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso.”

Mph. 15: Zosowa za pampingo.

Mph. 20: “Ntchito Yapadera Yogawira Bulosha Latsopano.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Sonyezani zitsanzo zimene zaperekedwazo. M’chitsanzo chimodzi, mwininyumba asonyeze kuti alibe chidwi kwenikweni ndi nkhani za m’Malemba ndipo amugawire thirakiti m’malo mwa bulosha.

Nyimbo Na. 192 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena