Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira May 9
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kuchitira chitsanzo choonetsa mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya May 15 ndi Galamukani! ya June 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chimodzi, onetsani akugawira magazini mu ulaliki wa mwamwayi m’basi kapena minibasi. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Gwiritsani Ntchito Mawu a Mulungu Kuwafika Ena Pamtima. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2005, tsamba 28 mpaka 31. Fotokozani mmene Yesu anagwiritsira ntchito Malemba pothandiza Petro. Fotokozani mmene tingatengere chitsanzo cha Yesu ngati pakufunika kuthandiza ana athu kuti asinthe kaganizidwe kawo ndi mmene amaonera zinthu, kapena kuthandiza ophunzira Baibulo athu, ndiponso ngakhale ife amene.
Mph. 20: “Konzani Ndandanda ya Banja Yotheka Kuitsatira.” M’mawu anu oyamba osapitirira mphindi ziwiri, fotokozani ubwino wa ndandanda yochita kulemba ndiponso fotokozani mmene angalembere ndandanda imene ili patsamba 6. Kenako kambiranani mwa mafunso ndi mayankho nkhani yakuti “Ndandanda ya Banja ya Misonkhano ya Mpingo.” Pemphani omvera kuti afotokoze mmene amachitira ntchito zina kuti zisasokonezane ndi misonkhano ya mpingo. Mbali zina zokhudza ndandanda ya banja zidzafotokozedwa m’milungu ikubwerayi.
Nyimbo Na. 176 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 16
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 20: “Ndandanda ya Banja Yolowera mu Utumiki wa Kumunda.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kupereka ndemanga zosonyeza phindu lopitira limodzi mu utumiki nthawi zonse monga banja.
Mph. 20: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 8.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Sonyezani chitsanzo chachidule cha ofalitsa akupereka kwa wophunzira Baibulo wake watsopano bulosha lakuti Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? Wofalitsayo asonyeze chithunzi chimene chili patsamba 20 la buloshalo ndipo mwachidule afotokoze za Msonkhano wa Onse. Atchule mutu wa nkhani ya onse ya mlungu umenewo ndi kupempha wophunzirayo kudzapezekapo.
Nyimbo Na. 134 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 23
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti limodzi ndi makalata oyamikira zopereka ochokera ku nthambi. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) sonyezani chitsanzo choonetsa mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya June 1 ndi Galamukani! ya June 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 18: “Tsiku la Yehova Lili Pafupi.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokonzekera nkhani imeneyi, onani m’buku la Samalani Ulosi wa Danieli, tsamba 59, ndime 28.
Mph. 15: “Ndandanda ya Banja Yochitira Phunziro la Banja.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzani nthawi idakalipo zoti munthu mmodzi kapena awiri adzafotokoze kuti amachita zotani kuti azikhala ndi phunziro la banja ndiponso kuti asamaphonye phunzirolo.
Nyimbo Na. 152 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 30
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa May. Tchulani mabuku ogawira mu June. Sonyezani chitsanzo cha mmene tingagawire mabukuwo pogwiritsa ntchito chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zimene zili mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu). Mungathe kugwiritsanso ntchito zitsanzo zina zimene zingakhale zothandiza.
Mph. 20: “Ndandanda ya Banja Yochitira Lemba la Tsiku.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kupereka ndemanga za mmene banja lawo lapindulira chifukwa chochitira pamodzi lemba la tsiku ndiponso za ndandanda imene aiona kukhala yothandiza kuchitira zimenezi.
Mph. 15: Simbani kapena chitani zitsanzo za zokumana nazo zosangalatsa za mu utumiki wa kumunda zimene zinachitika m’mwezi wa March, April ndi May. Konzani nthawi idakalipo zoti munthu mmodzi kapena awiri adzafotokoze zimene anachita kuti alalikire nawo kwambiri pa nyengo ya Chikumbutso ndiponso madalitso amene anapeza chifukwa chochita zimenezi.
Nyimbo Na. 115 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 6
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Zosowa za pampingo.
Mph. 25: “Kulitsani Chidwi cha Amene Mumakawapatsira Magazini.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 3, pitani m’buku la Kukambitsirana, tsamba 376 mpaka 380. Mungagwiritse ntchito mfundo zimenezo pokonza makambirano a lemba limodzi okhudza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite. Sonyezani chitsanzo cha zimene wofalitsa angachite pokambirana ndi amene amakam’patsira magazini pogwiritsa ntchito lemba limodzi. Wofalitsayo afotokoze mwachidule ndiponso kuchitira fanizo zimene lembalo likutanthauza kuti am’thandize mwininyumbayo kulimvetsetsa molondola ndiponso kuona mmene lilili lofunika pa moyo wake.
Nyimbo Na. 107 ndi pemphero lomaliza.