Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/05 tsamba 7
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 6/05 tsamba 7

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 27, 2005. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya May 2 mpaka June 27, 2005. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. N’chifukwa chiyani mawu oyerekeza zinthu ndi ofananitsa zinthu amathandiza kwambiri pophunzitsa? (Gen. 22:17; Sal. 1:3; Yak. 3:6) [be-CN tsa. 240 ndime 2-4, bokosi]

2. Kodi tingapeze kuti zitsanzo zimene zimakhala zophunzitsadi, koma tiyenera kusamala chiyani pankhani imeneyi? [be-CN tsa. 242 ndime 1-2]

3. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani posankha mafanizo ogwira mtima kwambiri? [be-CN tsa. 244 ndime 1-2]

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito zinthu zooneka pophunzitsa, ndipo kodi Yehova wachita motani zimenezi? [be-CN tsa. 247 ndime 1-2, bokosi]

5. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji zinthu zooneka mu utumiki wakumunda? [be-CN tsa. 248 ndime 1-tsa. 249 ndime 2]

NKHANI NA. 1

6. Kodi m’Mawu a Mulungu muli malangizo otani okhudza maphunziro a ana? [w03-CN 3/15 tsa. 12 ndime 2; tsa. 14 ndime 3]

7. Kodi Yehova anasonyeza motani kuti anali kuganizira Davide ali wachinyamata, ndipo Davide anasonyeza bwanji kukonda Yehova? [w03-CN 4/15 tsa. 29 ndime 4; tsa. 30 ndime 3]

8. N’chifukwa chiyani Yehova anaona, kapena kuti anasangalala ndi nsembe ya Abele, ndipo kodi zimenezi zikutitsimikizira chiyani? (Gen. 4:4) [w03-CN 5/1 tsa. 28 ndime 4–tsa. 29 ndime 1]

9. Kodi “mwambo wa Yehova” umene lemba la Miyambo 3:11 limatilangiza kuti tisakane n’chiyani? [w03-CN 10/1 tsa. 20 ndime 2-4]

10. Kodi mawu akuti ‘kukwanitsidwa’ amene agwiritsidwa ntchito pa 1 Timoteo 6:6-8 amatanthauza chiyani? [w03-CN 6/1 tsa. 9 ndime 1-2; tsa. 10 ndime 1]

KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. Kodi kukondana kwambiri kwa Jonatani ndi Davide kunachitira chithunzi chiyani? (2 Sam. 1:26) [w89-CN 1/1 tsa. 26 ndime 13]

12. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitika nthawi yoyamba imene Davide anafuna kupititsa likasa la chipangano ku Yerusalemu? (2 Sam. 6:2-9)

13. Davide ndi Bateseba atachimwa, n’chifukwa chiyani mwana wawo anafa, pamene lemba la Deuteronomo 24:16 ndi Ezekieli 18:20 limanena kuti mwana sayenera kufa chifukwa cha machimo a atate ake? (2 Sam. 12:14; 22:31)

14. Kodi tikudziwa bwanji kuti zimene Ziba ananeneza Mefiboseti zinali zabodza? (2 Sam. 16:1-4)

15. Kodi n’chifukwa chiyani zimene Mefiboseti anachita pa vuto lake ndi Ziba zili chitsanzo chabwino kwa ife? (2 Sam. 19:24-30)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena