Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, ndipo ngati anthuwo anena kuti alibe ana, gawirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Gawirani lililonse la mabulosha awa: Buku la Anthu Onse, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! September: Gawirani buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha. Mipingo imene ili ndi mabuku kapena mabulosha ambiri akale ingathe kugawira amenewo. Tikukumbutsanso mipingo kumaitanitsiratu mabuku okwanira pasadakhale kaamba ka utumiki monga mmene amasonyezera mu Utumiki Wathu wa Ufumu uliwonse.
◼ Nyimbo zotsatirazi n’zimene zidzaimbidwa pa msonkhano wachigawo: 4, 8, 13, 34, 38, 40, 69, 123, 139, 158, 162, 170, 174, 181, 192, 205, 207 ndi 221. Tikulimbikitsa mipingo yonse kuziphunzira mwina imodzi kapena ziwiri pambuyo pa misonkhano n’cholinga chakuti aliyense athe kuzizolowera.
◼ M’pofunika kuti buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova mukaliike mu laibulale yanu ya mpingo ku Nyumba ya Ufumu. Mukafuna kudziwa zambiri zokhudza malaibulale a pa Nyumba ya Ufumu, mukhoza kuzipeza mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2003 tsamba 5, ndi wa April 1997 m’Bokosi la Mafunso.
◼ Posachedwapa mipingo iyamba kulandira mafomu a Kuwerengera Mabuku (S-18). Mafomu amenewa ndi ogwiritsa ntchito kuwerengera mabuku amene mpingo uli nawo, osati amene unagawira m’munda. Mtumiki wa mabuku kapena abale ena amene angalembe fomu imeneyi ayenera kuwerenga malangizo ake mosamala asanayambe kulemba.
◼ Mipingo ingayambe kuitanitsa buku la Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse, limene linatulutsidwa pa msonkhano wachigawo wa chaka chatha. Buku limeneli lilipo m’Chichewa, Chifalansa, Chingelezi, Chipwitikizi, ndi Chitumbuka. Koma chonde kumbukirani kuti m’madera ambiri m’Malawi muno, bukuli silingagwiritsidwe ntchito kwenikweni mu utumiki. Poganizira zimenezi, mipingo yambiri imene inaitanitsa mabuku amenewa ambiri iona kuti nambala yake taichepetsa. Ngati zimenezi zachitikira mpingo wanu, yesetsani kugawa mabuku mwalandirawo moyenerera monga mmene mungathere.