Mabulosha Ogawira Anthu Amene Sali M’chipembedzo cha Chikristu
“Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
Kwa munthu wachikulire amene ndi Mbudha munganene kuti:
“Mwinamwake inu muli ndi nkhawa ngati ine chifukwa cha kuchuluka kwa malingaliro oipa komanso mmene zimenezi zikukhudzira ana athu. N’chifukwa chiyani makhalidwe oipa akuwonjezereka chonchi kwa achinyamata? [Yembekezani ayankhe.] Kodi mukudziwa kuti zimenezi zinanenedwa m’buku limene linalembedwa kale kwambiri zipembedzo za Chisilamu, Chikristu, ndi Chihindu zisanayambe? [Werengani 2 Timoteo 3:1-3.] Koma choti mudziwe n’chakuti zinthu zimenezi zipitirizabe kuwonjezeka ngakhale kuti maphunziro apita patsogolo. [Werengani vesi 7.] Kabuku aka kandithandiza kumvetsa bwino choonadi chimene anthu ambiri sanachiphunzirepo. Kodi mungakonde kukawerenga?”—km-CN 8/99 tsa. 8.
Chitsanzo ichi chingakhale bwino kwa Mhindu amene ali ndi banja:
“Ndikuchezera anthu amene akuda nkhawa kwambiri ndi mmene moyo m’mabanja ulili m’mayiko ambiri masiku ano. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimene chingathandize kuti banja likhale logwirizana? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ena amadziwa zimene malemba a Chihindu amanena pa nkhani ya banja, koma sanapezepo mwayi wofananiza zimenezo ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi. Ndikufuna ndikambirane nanu izi. [Werengani Akolose 3:12-14.] Gawirani bulosha lakuti: Why Should We Worship God in Love and Truth? limene lili m’Chingelezi basi, ndipo m’sonyezeni tsamba 8 ndi 9 ndiponso tsamba 20 ndi 21. Kabuku aka kakufotokoza malemba opatulika a ku India komanso a m’Baibulo.”—km-CN 9/99 tsa. 8.
Kwa Mhindu wachinyamata, munganene kuti:
“Ndikudziwa kuti umakhulupirira Mulungu. Kodi ukuganiza kuti cholinga cha Mulungu n’chotani kwa ifeyo? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Genesis 1:28.] M’malo ambiri muli anthu ochuluka zedi ndipo akukumana ndi mavuto adzaoneni. Kodi ukuganiza kuti Mlengi amafunadi kutithandiza kuthetsa mavuto athu?” Yembekezani ayankhe. Kenako gawirani bulosha lakuti Our Problems—Who Will Help Us Solve Them? limene lili m’Chingelezi basi, kapena gawirani buku lililonse limene lingakhale loyenerera.—km-CN 9/99 tsa. 8.
Polalikira kwa Myuda, munganene kuti:
“Ambirife takumanapo ndi zinthu zomvetsa chisoni monga kufa kwa okondedwa athu. Kodi mukuganiza kuti chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?” Yembekezani ayankhe. Ndiyeno gawirani bulosha lakuti: Will There Ever Be a World Without War? limene lili m’Chingelezi basi. Mukatero m’sonyezeni bokosi lakuti “Death and the Soul—What Are They?” patsamba 22 m’buloshalo. Werengani ndime 17 patsamba 23 pa nkhani yonena za kuuka kwa akufa. Fotokozani kuti kholo lakale Yobu anali ndi chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Gawirani buloshalo, ndipo konzani zodzabweranso kudzakambirana malemba osagwidwa mawu amene ali kumapeto kwa ndime 17.—km-CN 10/99 tsa. 8.
Ngati mukulankhula ndi Msilamu, munganene kuti:
“Ndikuyesetsa kuti ndilankhulane ndi Asilamu. Ndinamva kuti Asilamu amakhulupirira Mulungu mmodzi ndi aneneri onse. Kodi zimenezi n’zoona? [Yembekezani ayankhe.] Ndikufuna ndikambirane nanu za ulosi wakale kwambiri umene unaneneratu za kusintha kwa dzikoli kukhala paradaiso. Kodi ndingakuwerengereni zimene mneneri analemba? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Yesaya 11:6-9.] Ulosi umenewu umandichititsa kuganiza zimene zinalembedwa mu Korani zimene zikupezeka m’kabuku aka.” Gawirani bulosha lakuti: The Guidance of God—Our Way to Paradise, limene lili m’Chingelezi basi. Tsegulani patsamba 9 ndi kuwerenga mawu amene ali m’zilembo zakuda kwambiriwo. Ngati akuonetsa chidwi, pitirizani kukambirana naye ndime 7 mpaka 9 patsamba la kumanzerelo.—km-CN 11/99 tsa. 8.