Zitsanzo za Mmene Mungagawire Bulosha la Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani?—Kodi Mungachipeze Motani?
Mutatha kulonjerana ndi mwininyumba munganene kuti:
“Moyo wa masiku ano ndi wamavuto komanso uli ndi zambiri zokhumudwitsa. Kodi mukuganiza kuti mmenemu ndi mmene moyo unafunika kukhalira? [Yembekezani ayankhe.] Kabuku aka kakusonyeza kuti cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga anthu ndi dziko lapansili chidzakwaniritsidwa. [Kambiranani chithunzi cha patsamba 20 ndi 21. Ndiyeno werengani ndime 9, ndi kugogomezera Yesaya 14:24 ndi 46:11.] Paulendo wotsatira ndikakabweranso, ndikufuna ndidzakusonyezeni kuchokera m’Baibulo pamene limanena kuti Mulungu adzakhazikitsanso Paradaiso padziko lapansi.” Gawirani buloshalo, ndipo konzani zodzabweranso.
Mutabwererako, mungakanene kuti:
“Paulendo woyamba uja, ndinafotokoza kuti cholinga cha Mulungu n’chakuti anthu akhale ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi. [M’sonyezeninso chithunzi cha patsamba 20 ndi 21 chija.] Taonani kuti Yesu, Petro, ndi Davide analankhula za Paradaiso.” Muuzeni kuti atenge kabuku kake kaja. Ndiyeno tsegulani patsamba 21 ndi 22, ndi kukambirana ndime 10 mpaka 13. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo, kapena konzani zoti paulendo wotsatira mudzakambirane kamodzi mwa timitu tating’ono ta patsamba 29 mpaka 30.
Wofalitsa wachinyamata akhoza kunena kuti:
“Anthu ambiri a msinkhu wanga uno sakudziwa mmene moyo udzakhalire kutsogolo kuno. Kodi mukuganiza kuti moyo udzakhala wabwino kwa anthu a mibadwo ya kutsogolo? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limanena kuti tsogolo la anthu onse n’labwino kwambiri. [Tsegulani pachithunzi cha patsamba 31, ndi kuwerenga timawu timene tili pamenepo. Kenako werengani 2 Petro 3:13.] Kabuku aka kali ndi nkhani zofotokoza madalitso amene Mulungu wasungira anthu. [M’sonyezeni timitu ta m’kati timene tili patsamba 29 ndi 30, ndipo gawirani buloshalo.] Ndikufuna ndidzabwerenso kuti ndidzakufotokozereni za lonjezo la Mulungu lothetsa nkhondo.” Konzani zodzabweranso.
Mutabwererako, mungakanene kuti:
“Nditabwera nthawi yoyamba ija, ndinafotokoza mwachidule kuti cholinga cha Mulungu n’choti akhazikitsenso paradaiso padziko lapansi. [M’sonyezeninso chithunzi cha patsamba 31 chija.] Ndikufuna ndimve maganizo anu pa nkhani imene Mulungu walonjezayi yakuti adzathetsa nkhondo.” Muuzeni kuti atenge kabuku kake kaja. Mukatero werengani ndi kukambirana ndime 3 mpaka 6 patsamba 29. Konzani zoti mudzakambirane ndime 7 ndi 8 paulendo wotsatira.
Ngati mukulalikira limodzi ndi mwana, mungatchule dzina lanu ndi la mwanayo ndiyeno n’kunena kuti:
“Ngati mungakonde, ________ akufuna kukuonetsani chithunzi ndiponso kukuwerengerani lemba limodzi la m’Baibulo. [Mwanayo asonyeze chithunzi cha patsamba 31 ndi kuwerenga timawu timene tili pamenepo, ndipo kenako awerenge Chivumbulutso 21:4.] Kabuku aka kakufotokoza zimene Mulungu adzachite ndi mavuto amene tikukumana nawo masiku anowa. [M’sonyezeni mwachidule timitu ta m’kati ta patsamba 29 ndi 30 ndi kugawira buloshalo.] Tikadzabweranso, ndikufuna ndidzakusonyezeni zimene Baibulo limanena pa nkhani yoti matenda onse adzatha.”
Paulendo wobwereza, munganene kuti:
“Titakambirana poyamba paja, ndinanena kuti ndikufuna ndidzakusonyezeni zimene Baibulo limanena zoti matenda onse adzatha. Taonani zimene zalembedwa apa.” Muuzeni kuti atenge kabuku kake kaja. Mukatero kambiranani ndime 9 mpaka 14 patsamba 29. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo, kapena konzani zoti mudzakambirane ndime 15 mpaka 17 paulendo wotsatira.