Zitsanzo za Mmene Mungagawire Bulosha la Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
Mutamaliza kufotokoza nkhani inayake yochititsa mantha imene munamva, munganene kuti:
“Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola anthu kuti azivutika ngati iyeyo amatisamaliradi? [Yembekezani ayankhe.] Kabuku aka kakupereka yankho lokhutiritsa pa funso limeneli ndiponso kakufotokoza zimene Mulungu akuyembekezera kuchita posachedwapa. [M’sonyezeni zithunzi patsamba 27, ndi kuwerenga Salmo 145:16 patsamba 22.] Kodi Mulungu adzathetsa bwanji mavuto onse amene anthu akhala akukumana nawo? Ndidzabweranso kuti ndidzakufotokozereni zimenezi.” Gawirani buloshalo, ndipo konzani zodzabweranso.
Paulendo wobwereza, munganene kuti:
“Nditabwera ulendo woyamba uja, tinawerenga lemba ili. [Werengani Salmo 145:16 kapena ingonenani mawu ake.] Ndiyeno ndinafunsa kuti: Kodi Mulungu adzathetsa bwanji mavuto onse amene anthu akhala akukumana nawo?” Muuzeni kuti atenge kabuku kake kaja. Ndiyeno tsegulani patsamba 27 ndi 28, ndi kukambirana ndime 23 mpaka 25. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo, kapena konzani zoti mudzakambirane ndime 26 ndi 27 pa ulendo wotsatira.
Wofalitsa wachinyamata anganene kuti:
“Anthu a msinkhu wanga uno akuda nkhawa ndi mmene dzikoli lidzakhalire zaka 10 kapena 15 zikubwerazi. Kodi mukuganiza kuti moyo udzakhala bwanji panthawi imeneyo? [Yembekezani ayankhe.] Mavuto amene tikuwaona lerowa akusonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza. [Werengani 2 Timoteo 3:1-3.] Kabuku aka kakuyankha mafunso awa. [Werengani mafunso amene ali pachikutowo, ndi kugawira buloshalo.] Ndikadzabweranso, ngati mudzakhale ndi mphindi zowerengeka, ndikufuna ndidzakambirane nanu nkhani yolimbikitsa yokhudza mmene matenda ndi ukalamba zidzathere.” Konzani zodzabweranso.
Mutapitakonso mungakanene kuti:
“Titakambirana koyamba kaja, ndinanena kuti ndikufuna kudzakambirana nanu nkhani yolimbikitsa yokhudza mmene matenda ndi ukalamba zidzathere. Nkhani imeneyi ikupezeka apa.” Muuzeni kuti atenge kabuku kake kaja. Kenako werengani ndi kukambirana ndime 6 ndi 7 patsamba 23 ndi 24. Konzani zoti mudzakambirane ndime 8 ndi 9 paulendo wotsatira.
Ngati mukulalikira ndi mwana, mungatchule dzina lanu ndi la mwanayo ndiyeno n’kunena kuti:
“Ngati mungakonde, ________ akufuna kukuwerengerani lemba. [Mwanayo awerenge Salmo 37:29 ndi kupereka ndemanga yachidule.] Kabuku aka kakufotokoza mmene Mulungu adzakwaniritsire zolinga zake kwa anthu ndi dziko lapansi. [Muonetseni zithunzi za patsamba 24 mpaka 27.] Tikadzabweranso, ndikufuna ndidzakusonyezeni lonjezo labwino kwambiri la m’Baibulo lonena za kuuka kwa akufa.” Gawirani buloshalo ndipo konzani zodzabweranso.
Paulendo wobwereza, munganene kuti:
“Paulendo woyamba uja, tinawerenga lemba la Salmo 37:29 ndipo ndinafotokoza kuti ndikufuna kudzakusonyezani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kuuka kwa akufa. Taonani zimene zinalembedwa apazi.” Muuzeni kuti atenge kabuku kake kaja. Mukatero kambiranani ndime 12 mpaka 14 patsamba 24 ndi 25. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo, kapena konzani zoti mudzakambirane ndime 15 ndi 16 paulendo wotsatira.