Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/05 tsamba 3
  • Zitsanzo za Mmeme Mungagawire Mabulosha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zitsanzo za Mmeme Mungagawire Mabulosha
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Timitu
  • Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso
  • Buku la Anthu Onse
  • Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?
  • Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
  • Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 6/05 tsamba 3

Sungani

Zitsanzo za Mmeme Mungagawire Mabulosha

Mu mphatika ino muli zitsanzo zosiyanasiyana zokuthandizani kukonzekera maulaliki a mmene mungagawire mabulosha. Zitsanzo zimenezi mungathe kuzisintha kuti zigwirizane ndi zochitika za kwanuko. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena. Mabulosha ena amene zitsanzo zake sizinaikidwe mu mphatika ino, mungazikonze potengera zitsanzo zimene taperekazi.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, tsa. 8.

Chitsanzo chilichonse chimene chili patsamba lino chili ndi (1) funso lopangitsa munthu kuganiza loyambira kukambirana, (2) malo kumene mfundo zimene zikunenedwazo mungazipeze m’buloshalo, ndi (3) lemba loyenerera limene mungawerenge pamene mukukambirana. Ndiyeno mogwirizana ndi mmene munthuyo akuyankhira, mungapitirize kukambirana naye m’mawu anuanu.

Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso

“Anthu ambiri akufunafuna njira yothetsera mavuto amene tikukumana nawo masiku ano. Kodi mukuganiza kuti lidzakhalapodi boma limene lidzathetse mavuto amenewa?”—tsa. 3, ndime 1; Mat. 6:9, 10.

Buku la Anthu Onse

“Kodi mukuganiza kuti Baibulo lili ndi malangizo amene akhoza kukhala othandiza masiku athu ano?”—tsa. 22, mawu oyamba; tsa. 23, ndime 3 ya bokosi; Miy. 25:11.

Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha

“Anthu ambiri timalidziwa pemphero limene limayamba ndi mawu akuti “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Koma kodi mumadziwa kuti chipulumutso chathu chimadalira kudziwa dzina limenelo?”—tsa. 28, ndime 1; Aroma 10:13.

Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?

“Anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana okhudza mmenedi Mulungu alili. Kodi mukuganiza kuti zimene timakhulupirira pa nkhani imeneyi n’zofunika kuziona bwinobwino?”—tsa. 3, ndime 3, 7 ndi 8; Yoh. 17:3.

Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira

“Lero tikugawira kabuku aka kamene katonthoza ndi kupatsa chiyembekezo anthu ambiri amene okondedwa awo anamwalira. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti kodi anthu amene anamwalira ali ndi chiyembekezo chotani?”—tsa. 27, ndime 3; Yoh. 5:28, 29.

Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!

“Anthu ambiri amaganiza kuti afunika kupita kumwamba kuti akasangalale ndi moyo wosatha, koma kodi maganizo anu ndi otani pa nkhani yokhala ndi moyo padziko lapansi kosatha?”—Chithunzi cha pachikuto; Chiv. 21:4.

“Kodi munayamba mwaganizapo mmene mungam’tonthozere munthu amene wokondedwa wake wamwalira?”—tsa. 20, ndime 1; Miy. 17:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena