Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira June 13
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kuchitira chitsanzo choonetsa mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya June 15 ndi Galamukani! ya July 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chimodzi, onetsani wofalitsa akugawira magazini mu ulaliki wa mwamwayi. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Thandizani Ena Kukhala Ofalitsa Osabatizidwa. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yokambidwa ndi mkulu kuchokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 79 mpaka 81. Kambiranani dongosolo limene lilipo lodziwira ngati wophunzira Baibulo akukwanitsa zoyenereza za m’Malemba zosonyeza kuti angathe kuyamba kupita nawo mu utumiki wa kumunda limodzi ndi mpingo. Mlungu wamawa tidzakambirana mmene tingaphunzitsire wophunzira Baibulo amene wayenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa kuti ayambe kupita nawo mu utumiki wa nyumba ndi nyumba.
Mph. 20: “Kulalikira Kumatithandiza Kupirira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kupereka ndemanga pa malemba osagwidwa mawu ngati nthawi ilipo.
Nyimbo 149 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 20
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mungaitanitse mabuku a chinenero chakunja polembetsa kwa mtumiki wa mabuku, ngakhale litakhala kuti ndi buku limodzi lokha, n’cholinga choti mabuku amene mukufunawo muwapeze mofulumira popanda zododometsa.
Mph. 15: Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu. (Aheb. 4:12) Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2003, tsamba 11, ndime 13 mpaka 17. Fotokozani zitsanzo zosonyeza mmene malangizo a m’Baibulo amathandizira anthu kusintha moyo wawo. (w00-CN 1/1 tsa. 3 mpaka 5) Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito Baibulo m’mbali zonse za utumiki.
Mph. 20: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 9.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 2, fotokozani mfundo imodzi kapena ziwiri kuchokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2004 tsamba 8. Sonyezani chitsanzo chachidule cha phunziro la Baibulo. Atamaliza phunziro 2 m’bulosha la Mulungu Amafunanji, wochititsa phunziroyo afunse wophunzirayo kuti: “Kodi mnzanu mungam’fotokozere bwanji za dzina la Mulungu?” Wophunzirayo afotokoze mmene angagwiritsire ntchito Salmo 83:18, ndipo atamaliza kufotokoza wochititsa phunziroyo am’yamikire.
Nyimbo Na. 208 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 27
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa June. Werengani lipoti la maakaunti ndi makalata oyamikira zopereka ochokera ku nthambi. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu), sonyezani chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito ulaliki wina umene ungakhale wothandiza. Akamaliza chitsanzocho, bwerezani mawu oyamba amene anagwiritsa ntchito kuti am’pangitse mwininyumba uja kukhala ndi chidwi. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Zosowa za pampingo.
Mph. 20: Kugawira Mabulosha M’mwezi wa July ndi August. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera mu mphatika. Fotokozani mwachidule mmene angagwiritsire ntchito mphatikayo, ndipo fotokozani zimene zili m’bokosi limene lili patsamba 3 limodzi ndi mfundo zikuluzikulu za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, tsamba 8. Kambiranani zitsanzo za maulaliki zimene zili zoyenera mogwirizana ndi gawo lanu zomwe mungazigwiritse ntchito kugawira mabulosha pa maulendo oyamba. Sonyezani zitsanzo ziwiri kapena zitatu za maulalikiwo. Chitsanzo chimodzi achite wofalitsa amene ndi mwana.
Nyimbo Na. 196 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 4
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Kodi Ndandanda Yanu ya Banja Ikukuthandizani? Kambani mfundo za m’mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2005, ndi kupempha omvera kupereka ndemanga pa zimene achita kuti athe kugwiritsa ntchito mfundozo ndiponso madalitso amene apeza chifukwa chochita zimenezi.
Mph. 20: “Kulalikira Mogwira Mtima M’malo Opezeka Anthu Ambiri.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambeni mogwirizana ndi mmene lilili gawo lanu. Kumbutsani ofalitsa kubwereranso kwa anthu amene anasonyeza chidwi.
Nyimbo Na. 120 ndi pemphero lomaliza.