Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kwa amene aonetsa chidwi, asonyezeni bulosha la Mulungu Amafunanji. November: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati eninyumba akuoneka kuti alibe ana, gawirani buku la Chidziŵitso kapena thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? December: Gawirani buku la Munthu Wamkulu Koposa Onse Amene Anakhalako. January: Gawirani bulosha la Dikirani!
◼ Mwezi wa October ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza, chifukwa uli ndi mawikendi asanu.
◼ Mphatika imene ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno ndi “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2006.” Isungeni kuti mudzaigwiritse ntchito chaka chonse cha 2006.
◼ Kuyambira mlungu wa April 17, 2006, tidzayamba kuphunzira buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pa Phunziro la Buku la Mpingo. Mipingo iyenera kukhala ndi mabuku okwanira a zilembo za nthawi zonse ndi a zilembo zazikulu.
◼ Tikukumbutsa mipingo kuti Mabaibulo amene sasindikizidwa ndi gulu monga a Chichewa ndi Chitumbuka, asamagawidwe mwachisawawa. Zinthu zodula ngati zimenezi zizikhala m’gulu la zoodetsa zapadera ndipo muzizioda pokhapokha ngati wina wake waitanitsa. Kupatula pa ofalitsa, muzioderanso Baibulo ophunzira amene akupita patsogolo. Mipingo isaode Mabaibulo ambiri ndi kumangowasunga ndipo ofalitsa asagawire Baibulo kumunda pachifukwa chakuti wina wake wawapempha.
◼ Mipingo ina ikumaitanitsa zikwama zoikamo ndalama za zopereka za ntchito ya padziko lonse, zimene ofesi ya nthambi ili nazo zochepa chabe. Popeza kuti zikwama zimenezi zinapangidwa ndi kampani ya kunja osati gulu, siziyenera kuyendera dongosolo la zopereka. Mpingo uliwonse umene ukufuna kuitanitsa tizikwama timeneti ta ntchito ya padziko lonse iyenera kutumiza K40 pa chikwama chilichonse pamodzi ndi fomu ya S-20. Ngati zikwamazi zilipo, zidzatumizidwa ku mipingo pokhapokha titalandira ndalamazi.
◼ Mipingo iyenera kuitanitsa Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso cha 2006 pamene akutumiza oda yawo yotsatira ya mabuku. Timapepala timeneti tidzakhalako m’Chichewa, Chifalansa, Chingelezi, ndi Chitumbuka. Chonde odani mwanzeru poona kuti timapepala timeneti timakonzedwa kuti mugawire anthu achidwi okha, osati aliyense.