Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2006
Malangizo
Dongosolo lotsatirali ndilo lidzagwiritsidwe ntchito pochititsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu mu 2006.
MABUKU OPHUNZIRA: Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu [bi53-CN], Nsanja ya Olonda [w-CN], Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu [be-CN], Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova [od-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN].
Sukulu iyenera kuyamba PANTHAWI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno n’kupitiriza motere:
LUSO LA KULANKHULA: Mphindi 5. Woyang’anira sukulu, mlangizi wothandiza, kapena mkulu wina woyenerera adzafotokoza luso la kulankhula kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki. (Mipingo imene ili ndi akulu ochepa ingagwiritse ntchito mtumiki wothandiza woyenerera.)
NKHANI NA. 1: Mphindi 10. Mkulu woyenerera kapena mtumiki wothandiza woyenerera ndi amene ayenera kukamba nkhani imeneyi, ndipo izitengedwa mu Nsanja ya Olonda, m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kapena m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. Imeneyi ndi nkhani yolangiza imene ayenera kuikamba kwa mphindi khumi popanda mafunso obwereza. Cholinga chake chisakhale kufotokoza chisawawa mfundo za m’nkhaniyo koma kusonyeza phindu la mfundozo, ndi kutsindika mfundo zomwe zingathandize kwambiri mpingowo. Agwiritse ntchito mutu wosonyezedwa. Abale amene apatsidwa nkhani imeneyi azionetsetsa kuti akusunga nthawi. Malangizo am’seri angaperekedwe ngati pakufunika kutero.
MFUNDO ZAZIKULU ZA KUWERENGA BAIBULO: Mphindi 10. Kwa mphindi zisanu zoyambirira, mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera afotokoze mmene machaputala omwe awerengedwa mlunguwo angathandizire mpingowo. Angafotokoze mbali ina iliyonse ya chigawo cha kuwerenga Baibulo cha mlunguwo. Isakhale chidule chabe cha gawo lowerenga mlunguwo. Cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvera kuzindikira chifukwa chake komanso mmene mfundozo zilili zaphindu. Wokamba nkhaniyo ayenera kuonetsetsa kuti asapitirire mphindi zisanu zoperekedwa pa mbali yoyambirira imeneyi. Aonetsetse kuti wagwiritsa ntchito mphindi zisanu zomalizira kuti omvera alankhulepo. Apemphe omvera kulankhulapo mwachidule (kwa masekondi 30 kapena kucheperapo) pa mfundo za m’Baibulo zimene zinawasangalatsa powerenga ndiponso phindu lake. Ndiyeno woyang’anira sukulu apemphe ophunzira amene ali m’makalasi ena kupita ku makalasi awo.
NKHANI NA. 2: Mphindi 4 kapena mphindi zosakwana 4. Iyi ndi nkhani yoti mbale awerenge. Wophunzira awerenge nkhani imene wapatsidwa popanda kukamba mawu oyamba kapena omaliza. Ngati akuwerenga nkhani yake kuchokera mu Masalmo, afunika kuwerenganso timawu tapamwamba. Woyang’anira sukulu makamaka adzaonetsetsa kuti akuthandiza wophunzira kuwerenga mosonyeza kuti akumvetsa zimene akuwerengazo, kuwerenga mosadodoma, kutsindika ganizo moyenera, kusinthasintha mawu, kupuma moyenera, ndiponso kuwerenga mwachibadwa.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhani imeneyi azikamba ndi mlongo. Wophunzira amene wapatsidwa nkhani imeneyi angasankhe yekha kapena azipatsidwa mtundu wa makambirano kuchokera pa mndandanda umene uli patsamba 82 m’buku la Sukulu ya Utumiki. Wophunzira agwiritse ntchito mutu wa nkhani umene wapatsidwa ndipo agwirizanitse ndi mbali ya utumiki wakumunda yomwe ndi yotheka ndiponso yothandiza m’gawo la mpingowo. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyo mwa kufufuza m’mabuku athu. Ophunzira atsopano azipatsidwa nkhani zimene tasonyeza buku limene nkhaniyo yachokera. Woyang’anira sukulu adzaonetsetsa makamaka mmene wophunzira akufotokozera nkhaniyo ndiponso mmene akuthandizira mwininyumba kulingalira pa Malemba ndi kumvetsa mfundo zazikulu za nkhaniyo. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi.
NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Wophunzira akambe nkhani pa mutu umene wapatsidwa. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyo mwa kufufuza m’mabuku athu. Akapatsidwa mbale, aziikamba monga nkhani yokambira omvera amene asonkhana m’Nyumba ya Ufumuyo. Mlongo akapatsidwa nkhani imeneyi, nthawi zonse aziikamba mofanana ndi Nkhani Na. 3. Woyang’anira sukulu angapereke nkhani Na. 4 kwa mbale nthawi ina iliyonse imene akuona kuti m’poyenera kupatsa mbale. Dziwani kuti nkhani zimene zili ndi nyenyezi ziyenera kuperekedwa kwa abale basi kuti akambe ngati nkhani.
KUSUNGA NTHAWI: Nkhani iliyonse isadye nthawi. Chimodzimodzinso ndi ndemanga za mlangizi. Nkhani Na. 2 mpaka Na. 4 ziziimitsidwa mwaluso nthawi yake ikatha. Ngati abale amene akamba nkhani yotsegulira ya luso la kulankhula, Nkhani Na. 1, kapena mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo adya nthawi, azilangizidwa m’seri. Aliyense ayenera kusamala kwambiri nthawi. Pulogalamu yonse izitenga mphindi 45, osaphatikizapo nthawi ya nyimbo ndi pemphero.
MALANGIZO: Mphindi imodzi. Wophunzira aliyense akamaliza nkhani Na. 2, Na. 3, ndi Na. 4, woyang’anira sukulu adzanena mfundo zolimbikitsa za mbali ya nkhaniyo zimene wophunzirayo wachita bwino. Asapitirire mphindi imodzi pofotokoza zimenezi. Cholinga chake sindicho kungonena kuti “mwachita bwino” koma kutchula zifukwa zenizeni zimene zachititsa kuti mbali za nkhaniyo zikhale zogwira mtima. Malinga ndi zimene wophunzira aliyense akufunikira, malangizo ena othandiza angaperekedwe m’seri misonkhano itatha kapena panthawi ina.
MLANGIZI WOTHANDIZA: Bungwe la akulu lingasankhe mkulu waluso, ngati alipo, kuphatikiza pa woyang’anira sukulu, kuti akhale mlangizi wothandiza. Ngati pali akulu angapo pa mpingo, ndiye kuti chaka chilichonse mkulu wina woyenerera angasamalire udindo umenewu. Ntchito yake idzakhala yopereka malangizo am’seri, ngati angafunike, kwa abale amene akamba Nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu za Baibulo. N’kosafunika kuti azipereka malangizo kwa akulu anzake kapena atumiki othandiza nthawi iliyonse yomwe akamba nkhani zimenezi.
FOMU YOLANGIZIRA: Ili m’buku momwemo.
KUBWEREZA KWA PAKAMWA: Mphindi 30. M’miyezi iwiri iliyonse, woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza kwa pakamwa. Kudzatsatira pambuyo pa kukambirana luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo monga mmene tafotokozera pamwambapa. Kubwereza kwa pakamwaku kudzakhala kwa nkhani zimene zinakambidwa m’sukulu m’miyezi iwiri yapita, kuphatikizapo mlungu wa kubwerezaku. Ngati mpingo wanu udzakhala ndi msonkhano wadera mlungu umene muyenera kukhala ndi kubwereza kwa pakamwa, ndiye kuti kubwerezako (limodzinso ndi pulogalamu ya mlungu ndi mlungu ya mlungu umenewo) ziyenera kudzachitika mlungu wotsatira ndipo pulogalamu ya mlungu wotsatirawo iyenera kuchitidwa mlungu wamsonkhanowo. Ngati woyang’anira dera adzachezera mpingo wanu mlungu umene muyenera kukhala ndi kubwereza kwa pakamwa, ndiye kuti nyimbo, luso la kulankhula, ndiponso mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo ziyenera kuchitika mogwirizana ndi ndandanda ya mlungu umenewo. Ndiyeno nkhani yachilangizo (yokambidwa pambuyo pa luso la kulankhula) iyenera kutengedwa ku ndandanda ya mlungu wotsatira. Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu wotsatira idzakhala ndi luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo mogwirizana ndi mmene zilili pa ndandanda ya mlunguwo, ndipo kupenda kwa pakamwa kudzatsatira pambuyo pake.
NDANDANDA
Jan. 2 Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 29-32 Nyimbo 91
Luso la Kulankhula: Pindulani Mokwanira ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (be-CN tsa. 5 ndime 1–tsa. 8 ndime 1)
Na. 1: Kondwerani ndi Mawu a Mulungu (be-CN tsa. 9 ndime 1–tsa. 10 ndime 1)
Na . 2: 2 Mbiri 30:1-12
Na . 3: Chifukwa Chake Akristu Enieni Amapewa Kutukwana
Na . 4: Mmene Uchimo Umakhudzira Unansi Wathu ndi Mulungu (rs-CN tsa. 361 ndime 1-4)
Jan. 9 Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 33-36 Nyimbo 144
Luso la Kulankhula: Kuwerenga Molondola (be-CN tsa. 83 ndime 1-5)
Na . 1: Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova (od-CN tsa. 5 ndime 1–tsa. 7 ndime 1)
Na . 2: 2 Mbiri 34:1-11
Na . 3: Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Moyo (rs-CN tsa. 295 ndime 1-5)
Na . 4: Musamachite Manyazi Kutsatira Mfundo Zamakhalidwe Abwino za M’Baibulo
Jan. 16 Kuwerenga Baibulo: Ezara 1-5 Nyimbo 137
Luso la Kulankhula: Mmene Mungawerengere Molondola (be-CN tsa. 84 ndime 1–tsa. 85 ndime 3)
Na . 1: Mbali ya Kumwamba ya Gulu la Yehova (od-CN tsa 7 ndime 2–tsa. 9 ndime 1)
Na . 2: Ezara 1:1-11
Na . 3: Phindu Lokhala ndi Chikumbumtima Chokoma
Na . 4: Nyama Ndizo Miyoyo (rs-CN tsa. 295 ndime 6–tsa. 296 ndime 5)
Jan. 23 Kuwerenga Baibulo: Ezara 6-10 Nyimbo 106
Luso la Kulankhula: Kulankhula Momveka Bwino (be-CN tsa. 86 ndime 1-6)
Na . 1: Gulu la Yehova Likupita Patsogolo (od-CN tsa. 9 ndime 2–tsa. 10 ndime 1)
Na . 2: Ezara 6:1-12
Na . 3: Pa Imfa, Moyo Ndiponso Mzimu Sizipitiriza Kukhalabe ndi Moyo (rs-CN tsa. 297 ndime 1–tsa. 299 ndime 3)
Na . 4: aMmene Mulungu Amaonera Ukwati
Jan. 30 Kuwerenga Baibulo: Nehemiya 1-4 Nyimbo 161
Luso la Kulankhula: Mmene Mungalankhulire Momveka Bwino (be-CN tsa. 87 ndime 1–tsa. 88 ndime 3)
Na . 1: Kodi Kristu Ali ndi Udindo Wotani pa Makonzedwe a Mulungu? (od-CN tsa. 10 ndime 2–tsa. 13 ndime 1)
Na . 2: Nehemiya 2:1-10
Na . 3: Chitetezo Chimene Chili Chofunika Kwambiri
Na . 4: Kodi Mzimu Woyera N’chiyani? (rs-CN tsa. 319 ndime 2–tsa. 320 ndime 1)
Feb. 6 Kuwerenga Baibulo: Nehemiya 5-8 Nyimbo 40
Luso la Kulankhula: Kutchula Mawu Molondola—Mfundo Zofunika Kuzidziwa (be-CN tsa. 89 ndime 1–tsa. 90 ndime 2)
Na . 1: Werengani Baibulo Tsiku ndi Tsiku (be-CN tsa. 10 ndime 2–tsa. 12 ndime 3)
Na . 2: Nehemiya 5:1-13
Na . 3: Umboni Wakuti Munthu Ali ndi Mzimu Woyera (rs-CN tsa. 320 ndime 3–tsa. 321 ndime 2)
Na . 4: “Tchinjiriza Mtima Wako” (Miy. 4:23)
Feb. 13 Kuwerenga Baibulo: Nehemiya 9-11 Nyimbo 159
Luso la Kulankhula: Njira Zothetsera Vuto Lotchula Mawu Mosalondola (be-CN tsa. 90 ndime 4–tsa. 92)
Na . 1: Kuphunzira Mtendere M’malo mwa Nkhondo (w04-CN 1/1 tsa. 6 ndime 8–tsa. 7 ndime 5)
Na . 2: Nehemiya 10:28-37
Na . 3: Umboni Wosonyeza Kuti Yehova Amatikonda
Na . 4: Palibe Mbali Yauzimu ya Munthu Imene Imapulumuka Imfa (rs-CN tsa. 321 ndime 6–tsa. 322 ndime 3)
Feb. 20 Kuwerenga Baibulo: Nehemiya 12-13 Nyimbo 118
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mosadodoma (be-CN tsa. 93 ndime 1–tsa. 94 ndime 3)
Na . 1: Kuzindikira Udindo wa Kristu M’makonzedwe a Mulungu (od-CN tsa. 14 ndime 1-4)
Na . 2: Nehemiya 13:1-14
Na . 3: Chifukwa Chake Zili Zosatheka Kulankhulana ndi Anthu Akufa (rs-CN tsa. 190 ndime 4–tsa. 191 ndime 4)
Na . 4: bAkristu Sayenera Kusewera Masewera Achiwawa a pa Vidiyo
Feb. 27 Kuwerenga Baibulo: Estere 1-5 Nyimbo 215
Luso la Kulankhula: Mmene Mungathetsere Vuto Lolankhula Mododoma (be-CN tsa. 94 ndime 4–tsa. 96 ndime 2 kupatula bokosi patsamba 95)
Kubwereza kwa Pakamwa
Mar. 6 Kuwerenga Baibulo: Estere 6-10 Nyimbo 74
Luso la Kulankhula: Kuthana ndi Chibwibwi (be-CN tsa. 95 bokosi)
Na . 1: Kudziwa “Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru” (od-CN tsa. 15 ndime 1–tsa. 16 ndime 2)
Na . 2: Estere 6:1-10
Na . 3: Kuyankha Mofatsa Kungathe Kubweza Mkwiyo
Na . 4: Chifukwa Chake Akristu Amakana Kuchita Chilichonse Chokhudza za Mizimu (rs-CN tsa. 191 ndime 5–tsa. 193 ndime 4)
Mar. 13 Kuwerenga Baibulo: Yobu 1-5 Nyimbo 160
Luso la Kulankhula: Kupuma pa Zizindikiro Zopumira Ndiponso Posintha Ganizo (be-CN tsa. 97 ndime 1–tsa. 98 ndime 5)
Na . 1: Udindo wa Bungwe Lolamulira (od-CN tsa. 17 ndime 1–tsa. 18 ndime 2)
Na . 2: Yobu 2:1-13
Na . 3: Pewani Kufunafuna Kudziwa Zinthu Zokhudza Mphamvu za Ziwanda (rs-CN tsa. 193 ndime 5–tsa. 194 ndime 3)
Na . 4: Chifukwa Chake Akristu Oona Amapewa Kung’ung’udza
Mar. 20 Kuwerenga Baibulo: Yobu 6-10 Nyimbo 214
Luso la Kulankhula: Kupuma Kuti Mutsindike Ndiponso Kupuma Kuti Mumvetsere (be-CN tsa. 99 ndime 1–tsa. 100 ndime 3)
Na . 1: Kupambana kwa Zinthu Zauzimu (w04-CN 10/15 tsa. 4 ndime 2–tsa. 5 ndime 3)
Na . 2: Yobu 7:1-21
Na . 3: Zimene Kukhala Woyera Mtima Kumatanthauza
Na . 4: Mmene Munthu Angamasukire ku Kukhulupirira Mizimu (rs-CN tsa. 195 ndime 1-5)
Mar. 27 Kuwerenga Baibulo: Yobu 11-15 Nyimbo 8
Luso la Kulankhula: Kutsindika Ganizo Moyenerera (be-CN tsa. 101 ndime 1–tsa. 102 ndime 3)
Na . 1: “Yang’anirani Mamvedwe Anu” (be-CN tsa. 13 ndime 1–tsa. 14 ndime 5)
Na . 2: Yobu 12:1-25
Na . 3: Pewani Mzimu Wodziimira (rs-CN tsa. 323 ndime 3–tsa. 324 ndime 3)
Na . 4: Chifukwa Chake Utumiki Umatipatsa Chimwemwe
Apr. 3 Kuwerenga Baibulo: Yobu 16-20 Nyimbo 50
Luso la Kulankhula: Kuthetsa Vuto la Kusatsindika Ganizo (be-CN tsa. 102 ndime 4–tsa. 104 ndime 3)
Na . 1: Mmene Timasonyezera Kuti Timakonda Mulungu (w04-CN 3/1 mas. 19-21)
Na . 2: Yobu 16:1-22
Na . 3: Mmene Yehova Amakokera Anthu Kuti Am’lambire
Na . 4: cKuipa kwa Kunyada Ndiponso Mkhalidwe Wopanduka (rs-CN tsa. 325 ndime 1-2)
Apr. 10 Kuwerenga Baibulo: Yobu 21-27 Nyimbo 119
Luso la Kulankhula: Kutsindika Malingaliro Ofunika Kwambiri (be-CN tsa 105 ndime 1–tsa. 106 ndime 1)
Na . 1: Zinthu Zauzimu Zimapindulitsa (w04-CN 10/15 tsa. 5 ndime 4–tsa. 7 ndime 2)
Na . 2: Yobu 24:1-20
Na . 3: Yehova Amapereka Mphamvu Yoposa Yachibadwa
Na. 4: dPewani Zikhumbo za Thupi (rs-CN tsa. 325 ndime 3)
Apr. 17 Kuwerenga Baibulo: Yobu 28-32 Nyimbo 100
Luso la Kulankhula: Mphamvu ya Mawu Yoyenerera kwa Omvera (be-CN tsa. 107 ndime 1–tsa. 108 ndime 4)
Na . 1: Kumvetsera pa Misonkhano ya Mpingo ndi pa Misonkhano Ikuluikulu (be-CN tsa. 15 ndime 1–tsa. 16 ndime 5)
Na . 2: Yobu 29:1-25
Na . 3: Musalamulidwe ndi Chikhumbo cha Maso (rs-CN tsa. 326 ndime 1-2)
Na . 4: Chifukwa Chake Makamu Anadabwa ndi Mmene Yesu Anali Kuphunzitsira
Apr. 24 Kuwerenga Baibulo: Yobu 33-37 Nyimbo 94
Luso la Kulankhula: Mmene Mungakulitsire Luso Lolankhula ndi Mphamvu Yoyenerera (be-CN tsa. 108 ndime 5–tsa. 110 ndime 2)
Kubwereza kwa Pakamwa
May 1 Kuwerenga Baibulo: Yobu 38-42 Nyimbo 154
Luso la Kulankhula: Kusinthasintha Mphamvu ya Mawu Anu (be-CN tsa. 111 ndime 1–tsa. 112 ndime 2)
Na . 1: Zifukwa Zimene Tiyenera Kukhulupirira “Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru” (od-CN tsa. 19 ndime 1–tsa. 21 ndime 1)
Na . 2: Yobu 38:1-24
Na . 3: Kodi Lemba la Yesaya 60:22 Likukwaniritsidwa Bwanji Masiku Ano?
Na . 4: eKulankhula Konyansa Ndiponso Chiwawa Ndi Ntchito za Thupi (rs-CN tsa. 326 ndime 3)
May 8 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 1-10 Nyimbo 168
Luso la Kulankhula: Kusinthasintha Liwiro la Mawu Anu (be-CN tsa. 112 ndime 3–tsa. 113 ndime 1)
Na . 1: Kakonzedwe ndi Kayendetsedwe ka Mpingo (od-CN tsa. 21 ndime 2–tsa. 24 ndime 3)
Na . 2: Salmo 4:1–5:12
Na . 3: Khulupirirani Mulungu Osati Anthu (rs-CN tsa. 326 ndime 4–tsa. 327 ndime 1)
Na . 4: Kutsatira Chitsanzo cha Mawu a Moyo
May 15 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 11-18 Nyimbo 217
Luso la Kulankhula: Kusiyanitsa Mamvekedwe a Mawu Anu (be-CN tsa. 113 ndime 2–tsa. 114 ndime 3)
Na . 1: Mpingo wa Masiku Ano Umatengera Chitsanzo cha Atumwi (od-CN tsa. 25 ndime 1–tsa. 27 ndime 1)
Na . 2: Salmo 14:1–16:6
Na . 3: Kodi Akristu Oona Siali a Dziko Lapansi mu Njira Ziti?
Na . 4: Kodi Ndani Amene Kwenikweni Amachititsa Kuti Anthu Tizivutika? (rs-CN tsa. 222 ndime 3–tsa. 223 ndime 1)
May 22 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 19-25 Nyimbo 23
Luso la Kulankhula: Lankhulani ndi Mzimu wa Nkhaniyo (be-CN tsa. 115 ndime 1–tsa. 116 ndime 4)
Na . 1: Nzeru Yabwino Imapatsa Chisomo (w04-CN 7/15 tsa. 27 ndime 4–tsa. 28 ndime 4)
Na . 2: Salmo 22:1-22
Na . 3: Kodi Kuvutika Kunayamba Motani? (rs-CN tsa. 223 ndime 2-3)
Na . 4: fKodi Zikumbutso za Mulungu N’chiyani, Ndipo N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuzimvera?
May 29 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 26-33 Nyimbo 203
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwaumoyo Koyenerana ndi Nkhani (be-CN tsa. 116 ndime 5–tsa. 117 ndime 4)
Na . 1: Mukhoza Kunola Luso Lanu Lokumbukira Zinthu (be-CN tsa. 17 ndime 1–tsa. 19 ndime 1)
Na . 2: Salmo 30:1–31:8
Na . 3: Kodi Choonadi Chimamasula Munthu M’njira Zotani?
Na . 4: Mmene Tingapewere Kuvutika Kwambiri (rs-CN tsa. 223 ndime 4–tsa. 224 ndime 1)
June 5 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 34-37 Nyimbo 167
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Mzimu Waubwenzi (be-CN tsa. 118 ndime 1–tsa. 119 ndime 5)
Na . 1: Mphamvu Imene Pemphero Lili Nayo (w04-CN 8/15 tsa. 18 ndime 6–tsa. 19 ndime 10)
Na . 2: Salmo 34:1-22
Na . 3: Chifukwa Chake Mulungu Wachikondi Walola Kuvutika Kupitirizabe kwa Nthawi Yaitali Motere (rs-CN tsa. 224 ndime 3)
Na . 4: Kodi Tiyenera Kuthawa Mitundu Iti ya Mafano?
June 12 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 38-44 Nyimbo 216
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Mmene Tikumvera (be-CN tsa. 119 ndime 6–tsa. 120 ndime 5)
Na . 1: Mmene Mzimu Woyera Umatithandizira Kukumbukira (be-CN tsa. 19 ndime 2–tsa. 20 ndime 3)
Na . 2: Salmo 40:1-17
Na . 3: Sayansi Yoona Siitsutsana ndi Baibulo
Na . 4: Mulungu Adzathetsa Mavuto Onse Amene Atumiki Ake Avutika Nawo (rs-CN tsa. 225 ndime 1-4)
June 19 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 45-51 Nyimbo 104
Luso la Kulankhula: Kufunika kwa Manja ndi Nkhope Polankhula (be-CN tsa. 121 ndime 1-4)
Na . 1: Kodi Kudza kwa Yesu Kunachitika Liti? (w04-CN 3/1 tsa. 16, bokosi)
Na . 2: Masalmo 46:1–47:9
Na . 3: Chifukwa Chake Mulungu Sanafune Kungonyalanyaza Tchimo la Adamu (rs-CN tsa. 225 ndime 5-6)
Na . 4: Kodi Mkristu Angakhale Bwanji Wofooka Koma Wamphamvu? (2 Akor. 12:10)
June 26 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 52-59 Nyimbo 103
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Manja ndi Nkhope Polankhula (be-CN tsa. 121 ndime 5–tsa. 123 ndime 2)
Kubwereza kwa Pakamwa
July 3 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 60-68 Nyimbo 45
Luso la Kulankhula: Kuyang’ana Omvera mu Utumiki (be-CN tsa. 124 ndime 1–tsa. 125 ndime 4)
Na . 1: Mmene Kudzichepetsa kwa Yehova Kumatikhudzira (w04-CN 11/1 mas. 29-30)
Na . 2: Salmo 60:1–61:8
Na . 3: Kodi Kutenga Nawo Mbali mu Zochitika Zachikristu Kumatipatsa Ufulu Wophwanya Malamulo a Mulungu?
Na . 4: Mulungu Sindiye Amachititsa Nthenda za M’thupi ndi za Maganizo (rs-CN tsa. 226 ndime 1-3)
July 10 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 69-73 Nyimbo 225
Luso la Kulankhula: Kuyang’ana Omvera Pokamba Nkhani (be-CN tsa. 125 ndime 5–tsa. 127 ndime 1)
Na . 1: N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuchita Khama pa Kuwerenga? (be-CN tsa. 21 ndime 1–tsa. 23 ndime 3)
Na . 2: Salmo 71:1-18
Na . 3: Yehova Mwachikondi Wapatsa Ana Mwayi Wopindula ndi Nsembe ya Dipo ya Kristu (rs-CN tsa. 226 ndime 4)
Na . 4: gChifukwa Chake Akristu Ayenera Kukhala Opanda Tsankho
July 17 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 74-78 Nyimbo 28
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwachibadwa mu Utumiki wa Kumunda (be-CN tsa. 128 ndime 1–tsa. 129 ndime 1)
Na . 1: Kulitsani Kudzichepetsa Kuti Muyanjidwe ndi Mulungu (w04-CN 8/1 tsa. 11 ndime 15–tsa. 13 ndime 18 )
Na . 2: Salmo 75:1–76:12
Na . 3: Kodi Kufunafuna Yehova Kumaphatikizapo Chiyani? (Zef. 2:3)
Na . 4: Mulungu Sakugwiritsa Ntchito Masoka Achilengedwe Kuti Alange Anthu (rs-CN tsa. 227 ndime 1-3)
July 24 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 79-86 Nyimbo 112
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwachibadwa Papulatifomu (be-CN tsa. 129 ndime 2–tsa. 130 ndime 1)
Na . 1: “Hema wa Oongoka Mtima Adzakula” (w04-CN 11/15 tsa. 26 ndime 1–tsa. 28 ndime 2)
Na . 2: Salmo 82:1–83:18
Na . 3: Mavuto Sayenera Kutengedwa Monga Umboni Woti Mulungu Sakusangalatsidwa Nafe (rs-CN tsa. 227 ndime 4–tsa. 228 ndime 1)
Na . 4: Kodi Anthu Opanda Ungwiro Angakondweretsedi Mulungu?
July 31 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 87-91 Nyimbo 57
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwachibadwa Powerenga Pamaso pa Anthu (be-CN tsa. 130 ndime 2-4)
Na . 1: “Kuphunzira Kukakhala Kosavuta” Ndiponso Nzeru Ikamatitsogolera (w04-CN 11/15 tsa. 28 ndime 3–tsa. 29 ndime 7)
Na . 2: Salmo 89:1-21
Na . 3: Kuphunzira Baibulo Ndi Mbali ya Kulambira Kwathu
Na . 4: Kulemera si Kuyenera Kutengedwa Monga Umboni wa Madalitso a Mulungu (rs-CN tsa. 228 ndime 2-3)
Aug. 7 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 92-101 Nyimbo 190
Luso la Kulankhula: Ukhondo Umakometsera Uthenga Wathu (be-CN tsa. 131 ndime 1-3)
Na . 1: Kaphunziridwe Koyenera (be-CN tsa. 27 ndime 1–tsa. 31 ndime 2)
Na . 2: Salmo 92:1–93:5
Na . 3: Kodi Kulankhula Malirime ndi Umboni Wakuti Munthu ali ndi Mzimu wa Mulungu? (rs-CN tsa. 285 ndime 1-5)
Na . 4: Kufunika kwa Makhalidwe Abwino
Aug. 14 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 102-105 Nyimbo 1
Luso la Kulankhula: Mmene Kudzichepetsa ndi Kudziletsa Kumakhudzira Kavalidwe ndi Kudzikongoletsa kwa Munthu (be-CN tsa. 131 ndime 4–tsa. 132 ndime 3)
Na . 1: “Ntchito Zanu Zichulukadi, Yehova!” (w04-CN 11/15 mas. 8-9)
Na . 2: Salmo 104:1-24
Na . 3: Chifukwa Chake Tiyenera Kukhala Odikira
Na . 4: N’chifukwa Chiyani Kulankhula M’malirime Kumene Kumachitika Masiku ano Kuli Kosiyana ndi Kumene Ankachita Akristu Oyambirira? (rs-CN tsa. 286 ndime 1-4)
Aug. 21 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 106-109 Nyimbo 201
Luso la Kulankhula: Phindu Lovala Moyenera (be-CN tsa. 132 ndime 4–tsa. 133 ndime 1)
Na . 1: Achinyamata—Pewani Kutsatira Anzanu M’chimbulimbuli (w04-CN 10/15 tsa. 22 ndime 4–tsa. 24 ndime 5)
Na . 2: Salmo 107:20-43
Na . 3: Mawu a Mulungu Amatithandiza Kudziwa Zoona Zake Zenizeni Ena Akamanena Kuti ali ndi Mzimu wa Mulungu (rs-CN tsa. 286 ndime 6–tsa. 287 ndime 2)
Na . 4: Kodi Mulungu Tingam’tsanzire M’njira Ziti?
Aug. 28 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 110-118 Nyimbo 125
Luso la Kulankhula: Kuoneka Bwino Kumathandiza Kuti Ena Asakhumudwe (be-CN tsa. 133 ndime 2-4)
Kubwereza kwa Pakamwa
Sept. 4 Kuwerenga Baibulo: Salmo 119 Nyimbo 59
Luso la Kulankhula: Kaimidwe Kabwino ndi Zida za Ntchito Zosamalika (be-CN tsa. 133 ndime 5–tsa. 134 ndime 4)
Na . 1: Kuphunzira Kumapindulitsa (be-CN tsa. 31 ndime 3–tsa. 32 ndime 4)
Na . 2: Salmo 119:25-48
Na . 3: Chifukwa Chake Timamvera Akuluakulu a Boma
Na . 4: Kulankhula M’malirime si Kumene Kumadziwikitsa Akristu Oona Masiku Ano (rs-CN tsa. 287 ndime 3-5)
Sept. 11 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 120-134 Nyimbo 65
Luso la Kulankhula: Mmene Mungachepetsere Nkhawa Polankhula (be-CN tsa. 135 ndime 1–tsa. 137 ndime 2)
Na . 1: Malonjezo Amene Mungadalire (w04-CN 1/15 mas. 4-7)
Na . 2: Salmo 121:1–123:4
Na . 3: Kodi Mphatso ya Malirime Inayenera Kutenga Nthawi Yaitali Bwanji? (rs-CN tsa. 287 ndime 6–tsa. 288 ndime 1)
Na . 4: Kodi Mafanizo Okokomeza Zinthu ndi Otani, Ndipo Kodi Yesu Anawagwiritsa Ntchito Bwanji?
Sept. 18 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 135-141 Nyimbo 97
Luso la Kulankhula: Zimene Mungachite Kuti Mukhale Wodekha (be-CN tsa. 137 ndime 3–tsa. 138 ndime 4)
Na . 1: Oyang’anira Oweta Gulu la Nkhosa (od-CN tsa. 27 ndime 2–tsa. 28 ndime 3)
Na . 2: Salmo 136:1-26
Na . 3: Kodi Chikumbutso Ndi Chakudya Chogawana M’njira Yotani?
Na . 4: hUtatu si Chiphunzitso cha M’Baibulo (rs-CN tsa. 392 ndime 1–tsa. 398 ndime 2)
Sept. 25 Kuwerenga Baibulo: Masalmo 142-150 Nyimbo 5
Luso la Kulankhula: Ubwino Wokuza Mawu (be-CN tsa. 139 ndime 1–tsa. 140 ndime 1)
Na . 1: Zoyenereza Oyang’anira—Mbali Yoyamba (od-CN tsa. 29 ndime 1–tsa. 31 ndime 1)
Na . 2: Salmo 142:1–143:12
Na . 3: iNgati Wina Afunsa Kuti, ‘Kodi Mumakhulupirira Utatu?’ (rs-CN tsa. 412 ndime 3–tsa. 413 ndime 4)
Na . 4: Kodi Tingaike Zofuna za Ena Patsogolo pa Zofuna Zathu M’njira Ziti?
Oct. 2 Kuwerenga Baibulo: Miyambo 1-6 Nyimbo 111
Luso la Kulankhula: Gwiritsani Ntchito Bwino Maikolofoni (be-CN tsa. 140 ndime 2–tsa. 142 ndime 1)
Na . 1: Zoyenereza Oyang’anira—Mbali Yachiwiri (od-CN tsa. 31 ndime 2–tsa. 33 ndime 1)
Na . 2: Miyambo 5:1-23
Na . 3: Kodi N’chifukwa Chiyani Pali Kuipa Kochuluka (rs-CN tsa. 183 ndime 2–tsa. 184 ndime 1)
Na . 4: jMusamafalitse Nkhani Zonama (2 Tim. 4:4)
Oct. 9 Kuwerenga Baibulo: Miyambo 7-11 Nyimbo 73
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Baibulo Popereka Mayankho (be-CN tsa. 143 ndime 1-3)
Na . 1: Zoyenereza Oyang’anira—Mbali Yachitatu (od-CN tsa. 33 ndime 2–tsa. 35 ndime 1)
Na . 2: Miyambo 7:1-27
Na . 3: Kusalowerera M’zochitika Zadzikoli Monga Akristu Kumathandizira Kuti Tikhale Ogwirizana Monga Abale
Na . 4: N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuipa? (rs-CN tsa. 184 ndime 2–tsa. 185 ndime 3)
Oct. 16 Kuwerenga Baibulo: Miyambo 12-16 Nyimbo 180
Luso la Kulankhula: Zomwe Mungachite Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Baibulo (be-CN tsa. 144 ndime 1-4)
Na . 1: Kuphunzira Kugwiritsa Ntchito Zida Zina Zofufuzira (be-CN tsa. 35 ndime 3–tsa. 38 ndime 4)
Na . 2: Miyambo 14:1-21
Na . 3: Chifukwa Chakuti Mulungu Walola Kuipa, Kodi Ifeyo Tapindula Bwanji? (rs-CN tsa. 186 ndime 1-2)
Na . 4: Kodi N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizimvetsera Mwatcheru pa Misonkhano?
Oct. 23 Kuwerenga Baibulo: Miyambo 17-21 Nyimbo 131
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Omvera Kuwerenga Baibulo (be-CN mas. 145-146)
Na . 1: Zoyenereza Oyang’anira—Mbali Yachinayi (od-CN tsa. 35 ndime 2–tsa. 36 ndime 2)
Na . 2: Miyambo 17:1-20
Na . 3: Mmene Akristu Amaonera Anthu Okalamba
Na . 4: kKodi Baibulo Limalimbikitsa Kuti Tiyenera Kuwaona Motani Akazi (rs-CN tsa. 27 ndime 3–tsa. 28 ndime 1)
Oct. 30 Kuwerenga Baibulo: Miyambo 22-26 Nyimbo 9
Luso la Kulankhula: Ubwino Wotchula Malemba Moyenerera (be-CN tsa. 147 ndime 1–tsa. 148 ndime 2)
Kubwereza kwa Pakamwa
Nov. 6 Kuwerenga Baibulo: Miyambo 27-31 Nyimbo 51
Luso la Kulankhula: Kusankha Mawu Oyambira Abwino Potchula Malemba (be-CN tsa. 148 ndime 3–tsa. 149 ndime 2)
Na . 1: Zoyenereza Oyang’anira—Mbali Yachisanu (od-CN tsa. 37 ndime 1–tsa. 39 ndime 3)
Na . 2: Miyambo 28:1-18
Na . 3: Kodi Kupatsidwa Umutu kwa Amuna Kumachepetsa Akazi? (rs-CN tsa. 28 ndime 2–tsa. 29 ndime 1)
Na . 4: Chifukwa Chake Sitiyenera Kuweruza Anthu Amene Timakumana Nawo mu Utumiki Poona Mmene Akuonekera
Nov. 13 Kuwerenga Baibulo: Mlaliki 1-6 Nyimbo 25
Luso la Kulankhula: Kutsindika Koyenera Kumaphatikizapo Mmene Mukumvera (be-CN tsa. 150 ndime 1-2)
Na . 1: Maudindo mu Mpingo—Mbali Yoyamba (od-CN tsa. 40 ndime 1–tsa. 42 ndime 1)
Na . 2: Mlaliki 5:1-15
Na . 3: Kodi Choonadi cha Baibulo N’chobisika Bwanji kwa Anthu Anzeru? (Mat. 11:25)
Na . 4: Kodi Akazi Ayenera Kutsogolera mu Mpingo? (rs-CN tsa. 29 ndime 2-3)
Nov. 20 Kuwerenga Baibulo: Mlaliki 7-12 Nyimbo 37
Luso la Kulankhula: Tsindikani Mawu Oyenera (be-CN tsa. 150 ndime 3–tsa. 151 ndime 2)
Na . 1: Maudindo mu Mpingo—Mbali Yachiwiri (od-CN tsa. 42 ndime 2–tsa. 45 ndime 1)
Na . 2: Mlaliki 9:1-12
Na . 3: N’chifukwa Chiyani Akazi Achikristu Amavala Chophimba Kumutu pa Zochitika Zina? (rs-CN tsa. 29 ndime 4–tsa. 30 ndime 1)
Na . 4: Kodi Cholakwika N’chiyani ndi Kuchita Nsanje?
Nov. 27 Kuwerenga Baibulo: Nyimbo ya Solomo 1-8 Nyimbo 11
Luso la Kulankhula: Njira Zotsindikira (be-CN tsa. 151 ndime 3–tsa. 152 ndime 5)
Na . 1: Maudindo Ena M’gulu la Yehova—Mbali Yoyamba (od-CN tsa. 45 ndime 2–tsa. 49 ndime 2)
Na . 2: Nyimbo ya Solomo 7:1–8:4
Na . 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Ayenera Kuvala Zovala Zoyenera, Zoyera, ndi Zaulemu?
Na . 4: Kodi N’zoyenera Kuti Akazi Azidzola Mafuta Osalalitsa Khungu Kapena Kuvala Zodzikongoletsera? (rs-CN tsa. 31 ndime 1-3)
Dec. 4 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 1-5 Nyimbo 90
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Malemba Moyenerera (be-CN tsa. 153 ndime 1–tsa. 154 ndime 2)
Na . 1: Maudindo Ena M’gulu la Yehova—Mbali Yachiwiri (od-CN tsa. 50 ndime 1–tsa. 53 ndime 3)
Na . 2: Yesaya 3:1-15
Na . 3: Kodi Dziko Lidzaonongedwa ndi Moto? (rs-CN tsa. 128 ndime 1-2)
Na . 4: lChifukwa Chake Akristu Ayenera Kukhala ‘Odekha pa Kupsa Mtima’ (Yak. 1:19)
Dec. 11 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 6-10 Nyimbo 204
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Malemba Momveka Bwino (be-CN tsa. 154 ndime 3–tsa. 155 ndime 3)
Na . 1: Kukonza Autilaini (be-CN mas. 39-42)
Na . 2: Yesaya 10:1-14
Na . 3: N’chifukwa Chiyani Kukhululuka Kuli Kofunika Kwambiri?
Na . 4: Kodi Ndani Amene Amalamulira Dzikoli—Mulungu Kapena Satana? (rs-CN tsa. 128 ndime 3–tsa. 129 ndime 3)
Dec. 18 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 11-16 Nyimbo 47
Luso la Kulankhula: Lingalirani Nawo Kuchokera M’malemba (be-CN tsa. 155 ndime 4–tsa. 156 ndime 4)
Na . 1: Achinyamata Lolani Kuti Makolo Anu Akuthandizeni Kuteteza Mtima Wanu (w04-CN 10/15 tsa. 20 ndime 1–tsa. 22 ndime 3)
Na . 2: Yesaya 11:1-12
Na . 3: Kodi Akristu Amaliona Motani Dziko Ndiponso Anthu Amene ali Mbali ya Dziko? (rs-CN tsa. 130 ndime 1-5)
Na . 4: Akristu Oona Sadzamenya Nawo Nkhondo ya Armagedo
Dec. 25 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 17-23 Nyimbo 53
Luso la Kulankhula: Kumveketsa Phindu la Nkhani Yanu (be-CN tsa. 157 ndime 1-5)
Kubwereza kwa Pakamwa
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
b Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
c Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
d Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
e Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
f Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
g Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
h Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
i Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
j Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
k Sankhani mfundo zingapo zazikulu kuchokera pa nkhani imene mwapatsidwa zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
l Sankhani mfundo zingapo zazikulu kuchokera pa nkhani imene mwapatsidwa zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.