PHUNZIRO 3
Kutchula Mawu Molondola
SI AKRISTU onse amene anaphunzira kwambiri kusukulu. Ngakhale atumwiwo, Petro ndi Yohane, akuti anali “osaphunzira ndi opulukira.” (Mac. 4:13) Ngakhale ndi choncho, tiyenera kupeŵa kusukulutsa mphamvu ya choonadi cha m’Baibulo mwa kutchula mawu molakwitsa.
Mfundo Zofunika Kuzidziŵa. Palibe malamulo a katchulidwe ka mawu amene amagwira ntchito m’zinenero zonse. Zinenero zambiri zimalembedwa m’malembo a alifabeti. Kuwonjezera pa alifabeti ya Chilatini, palinso ma alifabeti ngati a Chiarabu, Chisililiki, Chigiriki, ndi Chiheberi. M’malo mwa malembo a pamndandanda wa alifabeti, Chitchaina amachilemba ndi malembo a mitundu yosiyanasiyana. Malembowo kaŵirikaŵiri amaimira liwu kapena gawo la liwu. Ngakhale kuti polemba Chijapani ndi Chikoreya amabwerekera malembo achitchaina, malembowo angaimire matchulidwe ndi matanthauzo osiyana kotheratu.
M’zinenero zogwiritsa ntchito alifabeti, matchulidwe oyenera amatanthauza kutchula moyenerera lembo kapena maphatikizo a malembo. Pamene chinenerocho chitsatira bwino malamulo ake, monga Chicheŵa, Chigiriki, Chisipanya, ndi Chizulu, matchulidwe oyenera sakhala ovuta. Komabe, mawu ochokera m’zinenero zina amabweretsa matchulidwe achilendo. Chifukwa cha zimenezo, lembo kapena silabo lingatchulidwe m’njira zosiyanasiyana, ndipo nthaŵi zina, silingatchulidwe n’komwe. Mungafunikire kuloŵeza pamtima mbali zoterozo ndi kuzigwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri polankhula. M’Chitchaina, kutchula mawu moyenerera kumalira kuloŵeza pamtima mazanamazana a malembo. M’zinenero zina, kusintha katchulidwe ka liwu kumasinthanso tanthauzo lake. Kulephera kusamalira mbali imeneyi m’chinenero kungapereke malingaliro olakwika.
Ngati mawu a chinenero amapangidwa ndi masilabo (kutanthauza mavawelo kapena maphatikizo a malembo), m’pofunika kutsindika kwambiri silabo yoyenera. M’zinenero zambiri zogwiritsa ntchito kalembedwe kotero, mofunikira kutsindika mumakhala mofanana nthaŵi zambiri. Ngati muli mofunikira matchulidwe ena, m’mawuwo amalembamonso mingoli. Zimenezi zimathandiza kutchula mawuwo moyenerera. Komabe, ngati matchulidwe amafuna kusinthasintha nthaŵi zonse, zimakhala zovutirapo. Kuti munthu adziŵe matchulidwe oyenerera, pamafunikira kuloŵeza zambiri.
M’zinenero zina, mingoliyo ndi zinthu zofunika kwambiri kuzidziŵa. Mingoli imeneyi ndi zizindikiro zomwe zimalembedwa pamwamba ndi pansi pa mawu ena a pamndandanda wa alifabeti, ngati zotere: è, é, ô, ñ, ō, ŭ, č, ö, ç. Mingoli imeneyi nthaŵi zina imalembedwa, koma nthaŵi zina woŵerengayo amatha kungoitchula malinga ndi nkhaniyo. Mbali yachiŵiriyi imafuna kukonzekera bwino ngati mwapatsidwa gawo loŵerenga pamaso pa anthu.
Kunena za katchulidwe ka mawu, pali mbuna zina zofunika kuzileŵa. Kukhala wolondola monyanyira kumaonetsa mzimu wodzikweza kapena kuyerekedwa. N’chimodzimodzinso kukonda matchulidwe amene ambiri sakuwagwiritsanso ntchito. Amachititsa omvera kumangoganiza za wolankhulayo. Komanso si bwino kungotayirira matchulidwe. Zina mwa mfundo zimenezi zafotokozedwa kale pamutu wakuti “Kulankhula Momveka Bwino.”
Matchulidwe oyenera a mawu m’chinenero chimodzi angakhale osiyana m’mayiko osiyanasiyana, ngakhalenso m’madera osiyanasiyana a dziko limodzi. Munthu wochokera ku dziko lina angamalankhule chinenero chofananacho koma akumatchula mawu mosiyanako. Amtanthauzira mawu angasonyeze matchulidwe ololeka osiyanasiyana a liwu limodzi. Munthu amene akuphunzira kulankhula chinenero china, angapindule kwambiri mwa kumvetsera amene amalankhula bwino chinenerocho ndi kutsatira matchulidwe awo. Monga Mboni za Yehova, timafuna kulankhula m’njira imene imalemekeza uthenga umene timalalikira komanso imene anthu a m’dera la kwathu angamve mosavuta.
M’kalankhulidwe kanu ka tsiku ndi tsiku, ndi bwino kugwiritsa ntchito mawu amene mumawadziŵa bwino. Kutchula mawu sikukhala vuto kwenikweni polankhula. Koma pamene muŵerenga mokweza, mumapeza mawu amene simugwiritsa ntchito m’kalankhulidwe kanu ka tsiku ndi tsiku. Ndipo Ife a Mboni za Yehova timaŵerenga mokweza nthaŵi zambiri. Timaŵerengera anthu Baibulo powalalikira. Abale ena amapatsidwa mbali zoŵerenga ndime pa Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi pa Phunziro la Buku la Mpingo. M’pofunika kuti tiziŵerenga molondola kuti tisasokoneze uthengawo mwa kutchula mawu molakwitsa.
Kodi mawu otsatiraŵa amakuvutani kuwatchula molondola posiyanitsa matanthauzo ake: Kutseka ndi kuseka; tsankho ndi sankha; tsoka ndi soka; kutchedwa ndi kuchedwa; kutsatsa ndi kusasa; m’thengo ndi mtengo; khama ndi kama; kukonza ndi kukhoza ndi kukodza; khoka ndi kokha ndi koka; kola ndi khola; thanzi ndi thadzi; kudzaza ndi kuzaza. Nanga mawu otsatiraŵa, kodi amakuvutani kutchula molondola: opsa; zizwitsa; psompsona; bakha; bala; banika; bola (nkhasako); bavu; madzi; tsika; patsa; tsitsi; pokhapokhapo; yang’ana (osati yangana).
Njira Zothetsera Vutolo. Ambiri amene ali ndi vuto la katchulidwe ka mawu sadziŵa kuti ali ndi vutolo. Ngati woyang’anira sukulu wanu atchula mbali za katchulidwe zimene muyenera kuwongolera, yamikirani kukoma mtima kwakeko. Mutadziŵa vuto lanu, kodi mungawongolere motani?
Choyamba, mukapatsidwa mbali yoŵerenga, patulani nthaŵi yoyang’ana mu mtanthauzira mawu. Yang’anani mawu amene simuwadziŵa. Ngati simudziŵa bwino kugwiritsa ntchito mtanthauzira mawu, yang’anani pamasamba ake oyambirira omwe amafotokoza zizindikiro zimene agwiritsa ntchito, kapena ngati kuli kofunikira, funsani munthu wina kuti akutanthauzireni mawuwo. Mtanthauzira mawuyo adzakusonyezani masilabo amene muyenera kukweza ndi amene muyenera kutsitsa. Nthaŵi zina, liwu limodzi lingatchulidwe m’njira zosiyanasiyana, malinga ndi mmene aligwiritsira ntchito. Liwu lililonse limene muyang’ana mu mtanthauzira mawu, litchuleni kangapo musanatseke mtanthauzira mawuyo.
Njira yachiŵiri imene mungawongolere katchulidwe ka mawu ndiyo kuŵerengera munthu wina, amene amatchula mawu molondola. M’pempheni kuti aziwongolera zimene mukulakwitsa.
Njira yachitatu yowongolera katchulidwe ka mawu ndiyo kumvetsera odziŵa kulankhula bwino. Ngati makaseti a New World Translation kapena Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! alipo m’chinenero chanu, agwiritseni ntchito mwakhama. Pamene muwamvetsera, zindikirani mawu amene amatchulidwa mosiyana ndi mmene mumatchulira. Alembeni ndi kumawayeseza. M’kupita kwa nthaŵi, muzitchula mawu molondola, ndipo malankhulidwe anu azimveka okoma.