PHUNZIRO 6
Kutsindika Ganizo Moyenerera
PAMENE mulankhula kapena kuŵerenga, m’pofunika kutchula bwino mawu komanso kutsindika mawu ofunika kwambiri okhala ndi ganizo lofunikira. Tsindikani mawu m’njira yomveketsa bwino ganizo.
Kutsindika ganizo moyenerera si kugogomeza mawu aliwonse, oŵerengeka kapena ambiri ayi. Ndi kugogomeza mawu oyenerera. Ngati mutsindika mawu osayenerera, tanthauzo la zimene mukunena silingamveke bwino kwa omvera, ndipo zimenezo zingachititse maganizo awo kuyamba kupita ku zinthu zina. Ngakhale nkhaniyo itakhala yosangalatsa, ngati ikambidwa mosatsindika bwino maganizo, imakhala yosagwira mtima ndi yosalimbikitsa omvera.
Tingagogomeze mawu mowonjezera m’njira zosiyanasiyana, kaŵirikaŵiri mwa kugwiritsa ntchito njirazo pamodzi: mwa kuwonjezera mphamvu ya mawu, mwa kuonetsa kukhudzidwa mtima kwathu, mwa kutchula mawu pang’onopang’ono ndi mwachifatse, mwa kupuma patsogolo kapena pambuyo pa ndemanga (kapena zonse ziŵiri), komanso kugogomeza ndi manja kapena nkhope. M’zinenero zina, kugogomeza kumachitidwanso mwa kutsitsa kapena kukweza mawu. Onani nkhaniyo ndi mikhalidwe kuti mudziŵe njira yabwino koposa imene mungagogomeze nayo.
Posankha zofunika kugogomeza, ganizirani zotsatirazi. (1) M’sentensi iliyonse, mawu oyenera kuwatsindika kwambiri sadziŵika ndi sentensi yokha komanso ndi mfundo zowazungulira. (2) Kutsindika ganizo kuyenera kuchitidwa poonetsa chiyambi cha mfundo yatsopano, kaya mfundo yaikulu kapena kungosintha lingaliro. Kungasonyezenso mapeto a lingaliro. (3) Wokamba nkhani angatsindike ganizo poonetsa maganizo ake pankhaniyo. (4) Kutsindika ganizo koyenera kungaunikenso mfundo zazikulu m’nkhani.
Kuti wokamba nkhani, kaya woŵerenga pamaso pa anthu, atsindike ganizo m’njira zimenezi, ayenera kumvetsa bwino nkhani yake ndi kukhala wofunitsitsa kuti omvera ake aimvetse. Kunena za malangizo omwe anaperekedwa m’masiku a Ezara, Nehemiya 8:8 amati: “Naŵerenga iwo m’buku m’chilamulo cha Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa choŵerengedwacho.” N’kwachidziŵikire kuti amene anaŵerenga ndi kutanthauzira Chilamulo cha Mulungu panthaŵiyo anazindikira kufunika kothandiza omvera awo kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuŵerenga, kuzikumbukira, ndi kuzigwiritsa ntchito.
Chimene Chingachititse Vuto. Anthu ochuluka amatha kumveketsa zimene akunena m’kulankhula kwawo kwa tsiku ndi tsiku. Koma pamene akuŵerenga nkhani yolembedwa ndi munthu wina, kumakhala kovuta kuti adziŵe mawu oyenera kuwatsindika. Chinsinsi chagona pakuimvetsa bwino nkhaniyo. Chofunika ndicho kuŵerenga ndi kumvetsa zolembedwazo. Choncho, ngati mwapemphedwa kuŵerenga nkhani kumpingo, konzekerani mwakhama.
Anthu ena amagwiritsa ntchito “kutsindika nthaŵi” m’malo mwa kutsindika ganizo. Iwo amagogomeza mawu m’mipata yofanana ya nthaŵi, kaya kugogomezako kukhale kotanthauza kanthu kapena ayi. Ena amagogomeza kwambiri aperekezi (prepositions) ndi alumikizi (conjunctions). Pamene kugogomezako sikuthandiza kumveketsa ganizo, kumakhala chizoloŵezi chongosokoneza.
Pofuna kutsindika ganizo, okamba nkhani ena amakweza mawu kwambiri moti omvera amaona ngati akuwakalipira. Zimenezo sizinunkha kanthu. Ngati kutsindika ganizo sikumveka kwachibadwa, zimaoneka ngati wokambayo akuderera omvera ake. Kodi chinthu chanzeru si ndicho kuwakopa mwa kulankhula mwachikondi ndi kuwathandiza kuona kuti zimene mukunenazo ndi za m’Malemba ndiponso zanzeru?
Mmene Mungathetsere Vutolo. Kaŵirikaŵiri, munthu amene amalephera kutsindika ganizo moyenerera amakhala asakudziŵa za vutolo. Angafunikire munthu wina kumuuza zimenezo. Ngati mukufuna kuthetsa vuto limeneli, woyang’anira sukulu wanu adzakuthandizani. Ndiponso, khalani womasuka kupempha thandizo kwa aliyense amene amalankhula bwino. M’pempheni kuti azimvetsera poŵerenga ndi polankhula ndipo azikulangizani mmene muyenera kuwongolera.
Monga poyambira, mlangizi wanu angakulangizeni kugwiritsa ntchito nkhani ya mu Nsanja ya Olonda monga poyesezera. Mosakayika adzakuuzani kuti muzipenda masentensi imodzi ndi imodzi kuti muone mawu ofunikira kuwagogomeza kuti tanthauzo lake limveke mosavuta. Angakukumbutseni kusamalira mawu ena olembedwa mopendamitsa. Kumbukirani kuti mawu amagwira ntchito mothandizana m’sentensi. Kaŵirikaŵiri, muyenera kugogomeza gulu la mawu, osati liwu limodzi. M’zinenero zina, ophunzira angalimbikitsidwe kusamalira kwambiri zizindikiro za mingoli ya mawu pofuna kutsindika moyenerera.
Monga sitepe lotsatira pophunzira zoyenera kugogomeza, mlangizi wanu angakulimbikitseni kuganiziranso mfundo zozungulira, m’malo mwa sentensi yokha. Kodi ndi mfundo yaikulu yotani imene akufotokoza m’ndime yonseyo? Kodi kudziŵa zimenezi kungakuthandizeni bwanji kugogomeza mawu ofunikira m’masentensi? Onani mutu wa nkhaniyo ndi mitu yaing’ono ya m’malembo aakulu akuda pamene pali mfundo zanu. Kodi zimenezi zikukhudzana bwanji ndi kusankha mawu oyenera kugogomeza? Zonsezi ndi mbali zofunika kuzilingalira. Koma samalani kuti musagogomeze mawu ochuluka kwambiri.
Kaya mudzalankhula kuchokera mumtima kapena mudzaŵerenga, mlangizi wanu angakulimbikitseninso kufotokoza maganizo m’njira yolimbikitsa kutsindika ganizo. Muyenera kuzindikira pothera lingaliro lofunika kapena posinthira kupita ku lina. Omvera adzayamikira ngati muwathandiza kuzindikira malo ameneŵa. Mungachite zimenezi mwa kutsindika mawu ngati choyambirira, tikachoka apo, potsirizira pake, choncho, ndi akuti n’zomveka.
Mlangizi wanu adzakusonyezaninso mfundo zimene muyenera kuonetsa kuti zikukhudza mtima wanu. Kuti muchite zimenezo mungagogomeze mawu ngati kwambiri, kwenikweni, kutalitali, n’zosatheka, n’zofunika kwabasi, ndi akuti nthaŵi zonse. Kuteroko kumalimbikitsa omvera kukhudzidwa mtima ndi zimene mukunena. Tidzafotokoza zambiri pankhaniyi mu Phunziro 11, lakuti “Mzimu Waubwenzi ndi Mmene Mukumvera.”
Kuti mudziŵe kutsindika bwino ganizo, mufunikira kuzindikira bwino lomwe mfundo zazikulu zimene mukufuna kuti omvera anu akazikumbukire. Zimenezi zidzaunikidwa mwapadera pofotokoza mbali za kuŵerengera anthu m’Phunziro 7 lakuti: “Kutsindika Malingaliro Ofunika Kwambiri,” ndiponso pofotokoza mbali ya kulankhula m’Phunziro 37 lakuti, “Kuunika Mfundo Zazikulu.”
Ngati mukuyesetsa kupita patsogolo mu utumiki wa kumunda, samalirani kwambiri mmene mumaŵerengera malemba. Khalani ndi chizoloŵezi chomadzifunsa kuti, ‘Kodi chimene ndikuŵerengera lembali n’chiyani?’ Kwa mphunzitsi, kungotchula bwino mawu sikokwanira. Ngakhale kuŵerenga mawuwo ndi mzimu wachifundo kungakhale kosakwanira. Ngati mukuyankha funso la wina kapena ngati mukuphunzitsa chiphunzitso choyambirapo cha choonadi, ndi bwino kutsindika palembalo mawu ounika zimene mukukambirana. Mukapanda kutero, amene mukumuŵerengerayo adzaphonya mfundo yanu.
Popeza kuti kutsindika ganizo kumatanthauza kugogomeza kwambiri mawu ena ndi magulu a mawu, wokamba nkhani wosazoloŵera angagogomeze mopambanitsa mawuwo. Potero, angamveke ngati munthu amene wangoyamba kumene kuphunzira kuimba chipangizo choimbira. Komabe, poyeseza mobwerezabwereza, amadzafika pakuimba mwachibadwa “manoti” oimbira, komanso mokoma kwambiri.
Mukaphunzira zoyambirira, mudzatha kupindula mwa kuyang’ana kwa okamba nkhani aluso. Posapita nthaŵi, mudzaona zimene mungathe kuchita mwa kutsindika mawu mosiyanasiyana. Ndipo mudzazindikira phindu lake lotsindikira mawu m’njira zosiyanasiyana pofuna kumveketsa zimene mukunena. Kukulitsa luso la kutsindika mawu moyenera kudzakuthandizani kumaŵerenga ndi kulankhula mogwira mtima.
Musachite ulesi kuphunzira zonse zofunika pa kutsindika ganizo. Kuti mukathe kulankhula mogwira mtima, limbikirani mwakhama kufikira mutadziŵa bwino kutsindika ganizo m’njira yomveka yachibadwa m’makutu mwa ena.