PHUNZIRO 37
Kuunika Mfundo Zazikulu
KODI mfundo zazikulu za nkhani ndiye chiyani? Zimenezi si mbali zosangalatsa chabe zimene mumangotchula modutsa m’kati mwa nkhani yanu. Ndi mfundo zofunika kwambiri zimene mumazifotokoza mofatsa kwa nthaŵi yokwanira. Ndi mfundo zimene zimathandiza kwambiri kukwaniritsa cholinga chanu pankhaniyo.
Chinsinsi chokuthandizani kuunika mfundo zanu chagona m’kasankhidwe ka mfundo ndi kayalidwe ka nkhani yanu. Kaŵirikaŵiri, kufufuza nkhani kumachititsa munthu kupeza mfundo zochuluka zosati n’kuzigwiritsa ntchito zonse. Nanga mungadziŵe bwanji mfundo zoyenera kugwiritsa ntchito?
Choyamba, lingalirani omvera anu. Kodi pankhani yanuyo iwo sakudziŵapo zambiri, kapena amaidziŵa bwino? Kodi ambiri amakhulupirira zimene Baibulo limanena pankhaniyo, kapena pali ena okayika? Kodi ndi zovuta zotani zomwe amakumana nazo pamoyo wa tsiku ndi tsiku pamene ayesetsa kugwiritsa ntchito zimene Baibulo limanena pankhaniyo? Chachiŵiri, tsimikizani kuti mukudziŵa bwino cholinga chanu polankhula kwa anthuwo pankhani imene mwasankhayo. Pogwiritsa ntchito mfundo ziŵiri zimenezi, pendani mfundo zanu zonse ndipo sankhulani zoyenerera zokhazo.
Ngati mwapatsidwa autilaini yomwe ili kale ndi mutu ndi mfundo zazikulu, itsatireni. Komabe, zimene mukafotokoze zikawapindulitsa kwambiri omvera ngati mukakumbukira mfundo tatchulazo pofotokoza mfundo yaikulu iliyonse. Ngati simunapatsidwe autilaini, ndi udindo wanu kusankha mfundo zazikulu.
Mukazikonzekera bwino mfundo zazikulu m’maganizo mwanu limodzi ndi mfundo zina zothandizana nazo, kudzakhala kosavuta kuti mukambe nkhani. Mwachidziŵikire, omvera anunso adzapindulapo zambiri pankhaniyo.
Njira Zosiyanasiyana Zosanjira Mfundo Zanu. Pali njira zosiyanasiyana zoyalira nkhani yanu. Pamene muyamba kuzidziŵa bwino, mudzaona kuti zingapo zingakhale zogwira mtima, malinga ndi cholinga chanu chokambira nkhani.
Njira yoyamba ndi ya timitu ta nkhani. (Mfundo yaikulu iliyonse ndi yofunika chifukwa imathandiza omvera anu kumvetsa nkhani yanu kapena cholinga cha nkhani yanu.) Njira ina ndi yoŵerengera nthaŵi motsatira zochitika zake. (Mwachitsanzo, kuyamba ndi zochitika Chigumula chisanadze, kenako zochitika Yerusalemu asanawonongedwe mu 70 C.E., ndiyeno zochitika za masiku ano.) Njira yachitatu ndi yofotokoza kututa zimene munthu amafesa. (Mukhoza kuyamba ndi zimene munthu amatuta kapena zimene amafesa. Mwachitsanzo, mungayambe ndi vuto limene liripo, kenako sonyezani chochititsa chake.) Njira yachinayi ndi yoonetsa zinthu zotsutsana. (Mungasiyanitse chabwino ndi choipa kapena choyenera ndi chosayenera.) Nthaŵi zina nkhani imodzi ingaphatikizepo njira zingapo.
Stefano ataonekera pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda pamlandu womusemera, anafotokoza umboni wamphamvu mwa kugwiritsa ntchito zochitika zakale. Monga timaŵerengera pa Machitidwe 7:2-53, iye anasankha mfundozo ndi cholinga. Stefano choyamba anamveketsa mfundo yakuti apereka umboni wa zochitika zakale umene omvera ake sakanatsutsa. Ndiyeno anatchula kuti ngakhale kuti Yosefe anakanidwa ndi abale ake, Mulungu anamugwiritsa ntchito kupulumutsira anthu ake. Kenako, anasonyeza kuti Ayudawo anali osamvera kwa Mose, amene Mulungu anali kumugwiritsa ntchito. Anamaliza mwa kutsindika kuti mzimu wosonyezedwa ndi Ayuda a mibadwo yakalewo ndi umene unaonekeranso mwa aja amene anaphetsa Yesu Kristu.
Musachulukitse Mfundo Zazikulu. Pamakhala mbali zochepa chabe zotambasulira mutu uliwonse. Kaŵirikaŵiri, sizimaposa zisanu. Zimakhalabe choncho kaya nkhani yanu ndi ya mphindi 5, 10, 30, kapena kuposapo. Peŵani kuunika mfundo zochuluka kwambiri. Omvera anuwo angathe kumvetsa mfundo zingapo m’nkhani imodzi. Ndipo ngati nkhaniyo ndi yotalikirapo, tsindikani mfundozo ndipo zimveketseni bwino kwambiri.
Kaya mugwiritsa ntchito mfundo zazikulu zingati, onetsetsani kuti mukutambasula iliyonse mokwanira. Patsani omvera mpata wokwanira wakuti amvetse mfundo yaikulu imodzi ndi imodzi kotero kuti ikhomerezeke zolimba m’maganizo mwawo.
Nkhani yanu izimveka mosavutikira. Sikuti zimenezi nthaŵi zonse zimadalira kuchepa kwa mfundo zanu ayi. Ngati malingaliro anu muwaika m’timitu ta nkhani toŵerengeka tokha, ndipo mutambasula timituto kamodzikamodzi, nkhani yanu idzakhala yosavuta kuitsatira ndi kuikumbukira.
Unikani Mfundo Zazikulu. Ngati nkhani yanu mwaiyala bwino, kudzakhala kosavuta kumveketsa mfundo zazikulu polankhula.
Njira yofunika kwambiri younikira mfundo zazikulu ndiyo kufotokoza mfundo za umboni, malemba, ndi mfundo zina m’njira yozipangitsa kumveketsa lingaliro lalikulu ndi kulifutukula. Mfundo zazing’ono zonse ziyenera kuthandiza kumveketsa mfundo yaikulu, kuperekapo umboni, ndi kuifutukula. Musawonjezere malingaliro osafunikira kwenikweni kokha chifukwa ndi osangalatsa. Pamene mukutambasula mfundo zazing’ono, sonyezani bwino lomwe mgwirizano wake ndi mfundo yaikulu imene zikuchirikiza. Musasiyire omvera kuti adzipezere okha. Mgwirizanowo mungausonyeze mwa kubwereza mawu ofunika omwe akupereka lingaliro lalikulu kapena mwa kubwereza nthaŵi ndi nthaŵi cholinga cha mfundo yaikulu.
Okamba nkhani ena amaunika mfundo zazikulu poziika m’manambala. Imeneyo pokhala njira imodzi younikira mfundo zazikulu, siiyenera kutilepheretsa kusankha mosamala ndi kutambasula mwa dongosolo mfundo za nkhaniyo.
Mungayambe ndi kutchuliratu mfundo yaikulu musanapereke umboni wake. Zimenezi zingapatse omvera chidwi chofuna kumvetsa zotsatira, ndipo kungakhomereze mfundo yaikuluyo. Mungatsindike mfundoyo mwa kuitchulanso mwachidule pambuyo poti yatambasulidwa yonse.
Mu Utumiki wa Kumunda. Malangizo omwe tafotokozawo sagwira ntchito pankhani za pamsonkhano zokha, komanso pokambirana ndi anthu mu utumiki wa kumunda. Pokonzekera, ganizirani za nkhani yaikulu imene anthu m’dera lanu ali nayo m’maganizo. Sankhani mutu wosonyeza kuti chiyembekezo chimene Baibulo limapereka chidzathetsa vutolo. Sankhani mfundo zazikulu ziŵiri zotambasulira mutuwo. Pezani malemba amene mudzagwiritsa ntchito ochirikiza mfundozo. Ndiyeno konzekerani mmene mukayambire makambiranowo. Kukonzekera koteroko kumapangitsa kukambirana mwachibadwa. Kumakuthandizaninso kunena chinthu chimene eninyumba adzakumbukira.