Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 27 tsamba 133-138
  • Kugogomeza Mutu wa Nkhani ndi Mfundo Zazikulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugogomeza Mutu wa Nkhani ndi Mfundo Zazikulu
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • **********
  • Kutambasula Mutu wa Nkhani
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kuunika Mfundo Zazikulu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kukonza Autilaini
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 27 tsamba 133-138

Phunziro 27

Kugogomeza Mutu wa Nkhani ndi Mfundo Zazikulu

1-4. Kodi mutu wa nkhani n’chiyani? Fotokozani.

1 Nkhani iliyonse imafuna mutu kuti njira yake ioneke ndi kuti mbali zake zonse zigwirizane bwinobwino. Kaya musankha mutu wotani, m’pofunika kuti uonekere m’nkhani yonseyo. Mutu wa nkhani ndiwo mfundo yaikulu ya nkhani yanu; ukhoza kutchulidwa mwa sentensi imodzi yokha koma ukumakhudza mbali iliyonse ya nkhani yanu. Mutu uyenera kuonekera kwa aliyense mwa omvetsera, ndipo udzatero ngati ugogomezedwa m’njira yoyenera.

2 Mutu wa nkhani sumangokhala wachisawawa, monga “chikhulupiriro”; uyenera kuloza mbali yapadera imene nkhaniyo idzafotokoza. Mwachitsanzo, mutuwo ungakhale wakuti “Chikhulupiriro Chanu—Kodi N’chachikulu Motani?” Kapena ungakhale wakuti “Chikhulupiriro N’chofunika Kuti Mukondweretse Mulungu” kapena wakuti “Maziko a Chikhulupiriro Chanu” kapenanso wakuti “Kulanibe m’Chikhulupiriro.” Ngakhale kuti mitu yonseyi ikunena za chikhulupiriro, uliwonse umafotokoza nkhaniyo m’njira yosiyana ndipo uliwonse umafuna mfundo zosiyana kotheratu zoufotokozera.

3 Nthaŵi zina mungafunikire kusonkhanitsa mfundo zanu musanasankhe mutu wake. Koma mutuwo uyenera kukhazikitsidwa bwino lomwe musanayambe kukonza autilaini ya nkhani yanu kapena musanayambe kusankha mfundo zazikulu. Mwachitsanzo, pambuyo pa phunziro la Baibulo lapanyumba lililonse mungafune kufotokoza gulu la Mboni za Yehova. Imeneyo ndi nkhani yoloŵetsamo zambiri. Kuti musankhe mbali zoti mufotokoze pankhaniyo, muyenera kuganizira omvetsera anu ndi cholinga cha nkhani yanu. Pamaziko amenewo mungasankhe mutu wa nkhani. Ngati mufuna kuyambitsa watsopano kuloŵa mu utumiki, mungafune kum’sonyeza kuti Mboni za Yehova zimatsanzira Yesu Kristu mwa kulalikira kunyumba ndi nyumba. Umenewo ndiwo ungakhale mutu wanu wa nkhani. Chilichonse chimene munena chiyenera kukhala chofutukula nkhani yotakata imeneyo, Mboni za Yehova.

4 Kodi mungaugogomeze motani mutu wa nkhani yanu? Choyamba, muyenera kusankha mutu woyenerana ndi cholinga chanu. Izi zimafuna kukonzekera pasadakhale. Mutasankha mutuwo ndi kukonza nkhani yanuyo mogwirizana ndi mutuwo, kuugogomeza kudzakhala kosavuta polankhula nkhani imene mwaikonzekera kale. Komabe, pokalankhula nkhani yanu, mungagogomeze mutu wake mwa kubwereza nthaŵi ndi nthaŵi mawu ofunika kwambiri kapena maganizo aakulu.

5, 6. Kodi mungadziŵe bwanji ngati mutu wa nkhani uli woyenerera?

5 Mutu wa nkhani woyenerera. M’Sukulu ya Utumiki Wateokalase kaŵirikaŵiri mutu wa nkhani woyenerera sukhala vuto, chifukwa nthaŵi zambiri umaperekedwa. Koma sikuti nkhani zonse zimene mudzalankhula muzipatsidwa mutu wake. Choncho n’kofunika kudziŵa bwino za mutu wa nkhani.

6 Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti mutu ndi woyenerera? Zilipo zinthu zingapo. Muyenera kuganizira omvetsera anu, cholinga chanu, ndi mfundo zimene mwagaŵiridwa kuti muzifotokoze, ngati nkhaniyo mwachita kupatsidwa. Ngati muona kuti nkhani zimene mumalankhula mitu yake sigogomezedwa, chingakhale chifukwa chakuti simukonza nkhanizo mogwirizana ndi mfundo yaikulu iliyonse. Mwinanso mumaphatikizapo mfundo zambiri zosakhudzana kwenikweni ndi mutu wa nkhaniyo.

7, 8. Sonyezani njira zimene munthu angagogomezere mutu wa nkhani.

7 Kubwereza mawu kapena ganizo la mutu wa nkhani. Njira imodzi yochititsira kuti mbali zonse za nkhani zigogomeze mutu wake ndiyo kubwereza mawu ofunika kwambiri otchulidwa m’mutuwo kapena kubwereza ganizo lalikulu la mutuwo. M’nyimbo, mutu wake ndiwo umatchulidwa mobwerezabwereza kwambiri. Ndipo n’kosavuta kupangitsa nyimboyo kudziŵika mosavuta. Maimbidwe ake samangokhala amodzimodzi. Nthaŵi zina pamamveka liwu limodzi kapena aŵiri m’kuimbako, akumatchula mutu wake m’mawu osiyanasiyana, koma m’njira inayake, woimbayo amasakaniza m’maimbidwe akewo mawu a mutu wa nyimbo moti amamvekera m’nyimbo yonseyo.

8 Ziyenera kukhalanso motero ndi mutu wa nkhani. Kubwerezabwereza mawu aakulu kapena maganizo a mutuwo kuli ngati kubwereza mawu m’nyimbo. Kugwiritsa ntchito mawu ena ofanana nawo tanthauzo kapena kubwerezanso maganizo aakulu kumagogomeza mutuwo. Ngati njira zimenezi zigwiritsidwa ntchito mosamala, osati kungobwereza mawu amodzimodzi, mutu wa nkhaniyo udzagogomezeka m’nkhani yonseyo ndipo udzakhala mfundo yaikulu imene omvetsera adzatolapo.

**********

9-13. Fotokozani zimene zili mfundo zazikulu m’nkhani. Perekani fanizo.

9 Mutasankha mutu wa nkhani yanu, sitepe lotsatira pokonzekera ndilo kusankha mfundo zazikulu zolankhulira nkhaniyo. Pasilipi lanu la Uphungu wa Kulankhula, mfundo imeneyi yatchedwa “Kumveketsa mfundo zazikulu.”

10 Kodi mfundo zazikulu m’nkhani n’chiyani? Sindizo malingaliro ongosangalatsa chabe kapena mfundo zongokondweretsa zofotokozedwa mwachidule ayi. Izo ndi zigawo zazikulu za nkhani, malingaliro amene amafotokozedwa kwa kanthawi ndithu. Izo zili ngati malebulo pamashelufu kapena zizindikiro m’sitolo zothandiza munthu kudziŵa katundu amene ali pamashelufupo, ndipo zimasonyezanso zofunika kupezeka pamalo amenewo ndi zosafunika kupezekapo. Pashelufu yolembedwa MPUNGA, sipafunika kupezeka majamu ndi manyuchi chifukwanso zingasokoneze anthu. Pa chizindikiro chakuti KHOFI NDI TIYI, sipafunika mpunga. Ngati malebulo a mashelufu sakuoneka chifukwa chochuluka zinthu kapena kupakira zinthu zochuluka kwambiri, kumakhala kovuta kupeza chilichonse. Koma ngati zizindikirozo zioonekera bwino, munthu atha kuzindikira msanga zimene zilipo. N’chimodzimodzinso ndi mfundo zazikulu za nkhani yanu. Malinga ngati zikumveka mosavuta ndipo n’zosavuta kukumbukira, omvetsera anu sadzafunikira notsi zambirimbiri kuti akutsatireni mpaka kumapeto ake a nkhani yanu.

11 Chinthu china ndi ichi. Kasankhidwe ndi kagwiritsidwe ka mfundo zazikulu kadzasiyana malinga ndi omvetsera komanso malinga ndi cholinga chake cha nkhaniyo. Pachifukwa chimenechi, woyang’anira sukulu ayenera kuona mmene wophunzirayo wasankhira mfundo zazikulu mwa kuona mmene akuzigwiritsira ntchito, osati mwa kuyerekeza ndi mfundo zimene phunguyo wasankhiratu kale.

12 Posankha mfundo zazikulu sankhani zofunika zokhazokha. Motero, funsani kuti, kodi n’chiyani chimapangitsa mfundo kukhala yofunika? Imakhala yofunika ngati simungathe kukwaniritsa cholinga cha nkhani yanu popanda mfundo imeneyo. Mwachitsanzo, pokambirana za dipo ndi munthu wosadziŵa chiphunzitsocho, m’pofunika kuyamba mwafotokoza za moyo wa Yesu monga munthu padziko lapansi, apo phuluzi n’kosatheka kuti munthuyo azindikire mtengo wolinganira wa nsembe ya Yesu. Choncho mungaone imeneyi kukhala imodzi mwa mfundo zazikulu zokambirana. Koma ngati munatsimikizira kale kwa munthuyo kuti chiphunzitso cha Utatu ndi chonama, pamenepo kukambirana kwanu za malo amene Yesu anawatenga monga munthu sikungakhale kofunika kwenikweni chifukwa munthuyo anakuvomereza kale. Ndipo chifukwa cha ichi tsopano kungakhale kosavuta kwenikweni kufotokoza mtengo wolinganira wa dipo la Yesu. Motero kukambirana za moyo wa Yesu monga munthu sikungakhale kofunikira kwenikweni.

13 Choncho dzifunseni kuti, Kodi n’chiyani chimene omvetsera anga akuchidziŵa kale? Kodi ndiyenera kumveketsa chiyani choyamba kuti ndikwaniritse cholinga changa? Ngati yankho la funso loyambalo mukulidziŵa, mukhoza kuyankha lachiŵirilo mwa kusonkhanitsa mfundo zanu, mukumapatulapo kaye zonse zimene akuzidziŵa kale ndi kusankhulapo mfundo zonse zotsalazo kukhala m’magulu angapo chabe. Magulu ameneŵa amakhala zizindikiro zanu zosonyeza mtundu wa chakudya chauzimu chimene muti muchigaŵire kwa omvetsera. Malebulo ameneŵa kapena mfundo zazikulu zimenezi siziyenera kuphimbika kapena kubisika. Ndizo mfundo zanu zazikulu, zimene ziyenera kuonekera.

14-17. Perekani zifukwa zimene sitiyenera kukhalira ndi mfundo zazikulu zambirimbiri.

14 Kusachulukitsa mfundo zazikulu. M’nkhani iliyonse mfundo zofunika zimakhalamo zingapo zokha. Nthaŵi zambiri mutha kuziŵerenga. Zimenezi zimakhalabe choncho mosasamala kanthu za nthaŵi imene muli nayo yozilankhulira. Musagwere m’mbuna yofuna kulongosola mfundo zambirimbiri kuti zionekere. Ngati sitolo n’njaikulu kwambiri ndipo ili ndi zigawo zambiri, wina angafunikire kufunsa. Omvetsera anu angangomvetsa maganizo angapo panthaŵi imodzi. Ndipo pamene mulankhula kwanthaŵi yaitali, m’pamenenso mufunikira kufeŵetsa nkhani yanu, komanso m’pamene mfundo zanu zazikulu ziyenera kuonekera bwino mosavuta. Choncho musayese kupangitsa omvetsera anu kukumbukira zinthu zambiri. Sankhani mfundo zimene muona kuti afunikiradi kutolapo ndiyeno nthaŵi yonseyo fotokozani zokhazo.

15 Kodi n’chiyani chimadziŵitsa kuti mwachulukitsa mfundo zazikulu kapena ayi? Mwachidule tinganene kuti, ngati mfundo ina mutha kuisiya komabe cholinga chanu n’kuchikwaniritsabe, mfundo imeneyo ili yosafunika kwenikweni. Kuti nkhaniyo imveke bwino, mungangophatikiza mfundoyo monga yolumikizira kapena monga yokumbutsira, koma siiyenera kuonekera monga yapadera mofanana ndi zinazo zimene simungathe kuzisiya.

16 Chinthu china, muyenera kukhala ndi nthaŵi yokwanira kufotokozera mfundo iliyonse bwino lomwe ndi motsimikiza. Ngati pali zochuluka zoti mulankhule m’nthaŵi yaifupi, chepetsani zimene omvetsera akuzidziŵa kale. Chotsani zinazo ndi kusiya zimene sakuzidziŵa zokha ndipo zimveketseni bwino lomwe moti kukhale kovuta kwa iwo kuziiŵala.

17 Chotsirizira, nkhani yanu iyenera kuoneka kuti ndi yosavuta. Chimenechi sichimangodalira unyunji wa mfundo zolankhulidwa. Nthaŵi zina ingangokhala njira imene mwasanjira pamodzi mfundo zanu. Mwachitsanzo, ngati mungaloŵe m’sitolo ndi kupeza kuti zinthu zonse anangoziunjika pamodzi pansi pakati pa nyumbayo, zingaoneke zongosakanikirana komanso zosokoneza kwambiri. Ndipo kungakhale kovuta kuti mupeze chilichonse. Koma, ngati chilichonse chaikidwa m’malo ake bwinobwino ndipo zinthu zonse zofanana zaikidwa malo amodzi olembedwa chizindikiro chake, zimakhala zokondweretsa ndipo china chilichonse mutha kuchipeza mosavuta. Pangitsani nkhani yanu kukhala yosavuta mwa kusanja maganizo anu m’mfundo zazikulu zoŵerengeka chabe.

18. Kodi mfundo zazikulu ziyenera kufotokozedwa motani?

18 Kufotokoza mfundo zazikulu payokhapayokha. Mfundo yaikulu iliyonse iyenera kuima payokha. Iliyonse ifotokozedwe payokha. Kumeneku sikunena kuti simungafotokoze mwachidule mitu yaikulu m’mawu oyamba kapena kumapeto kwa nkhani yanu. Koma m’thunthu la nkhani muyenera kulankhula za mfundo imodzi yaikulu panthaŵi imodzi, mukumatchula mfundo zina kokha powolokera ku ina kapena pobwereza mawu ndi cholinga chogogomeza mfundoyo. Kuphunzira kupanga autilaini ya timitu tokhatokha kudzathandiza kwambiri kuona ngati mfundo zazikulu zikufotokozedwa payokhapayokha.

19-21. Kodi mfundo zazing’ono ziyenera kugwiritsidwa ntchito motani?

19 Mfundo zazing’ono ziloza ku mfundo zazikulu. Mfundo zopereka umboni, malemba, kapena mfundo zina zoperekedwa ziyenera kuloza ku mfundo yaikulu ndi kuifutukula.

20 Pokonzekera, pendani mfundo zonse zazing’ono ndi kusunga zokha zimene zimachirikiza mwachindunji mfundo yaikulu imeneyo, kaya ndi mwa kuimveketsa bwino, kupereka umboni kapena kuifutukula. Mfundo iliyonse yosachirikiza mfundo yaikulu iyenera kuchotsedwa. Idzangosokoneza nkhaniyo.

21 Mfundo iliyonse yochirikiza mfundo yaikulu iyenera kugwirizana mwachindunji ndi mfundo yaikuluyo mwa zimene mukunena. Musasiyire omvetsera kuti agwirizanitse okha. Ufotokozeni momvekera bwino mgwirizanowo. Nenani chimene chili mgwirizanowo. Ambiri sangazindikire chinthu chimene simunachinene. Mungachite chimenecho mwa kubwereza mawu aakulu amene amapereka mfundo yaikulu kapena mwa kubwereza nthaŵi ndi nthaŵi ganizo lalikulu la mfundo yaikuluyo. Mutadziŵa luso losumika mfundo zanu zonse zazing’ono pamfundo zazikulu za nkhani, komanso kulunzanitsa mfundo yaikulu iliyonse ndi mutu wa nkhani, nkhani zanu zizikhala zosavuta kumva komanso zokoma. Chimenecho chidzazipangitsa kukhalanso zosavuta kulankhula koma zovuta kuiŵala.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena