Phunziro 9
Kukonza Autilaini
1-4. Ndi motani mmene tingasankhire mutu wa nkhani ndi mfundo zake zazikulu?
1 Wolemba Uthenga Wabwino Luka anati kwa mnzake Teofilo: “Ndinatsimikizanso mtima, chifukwa ndalondola zinthu zonse mosamalitsa kuyambira pachiyambi, kuti ndikulembere mwatsatanetsatane.” (Luka 1:3, NW) Chotero, iye atafufuza, atasonkhanitsa maumboni enieni a nkhani yake, anayamba kulemba zinthuzo mwatsatanetsatane womvekera bwino. Ifenso tingachite bwino kutsata dongosolo limenelo pokonza nkhani zathu. Kumeneko ndiko kukonza autilaini.
2 Kusankha mfundo zazikulu. Popeza cholinga chenicheni cholankhulira Mawu a Mulungu ndicho kupereka malingaliro ku maganizo a munthu wina, ndi bwino kuti malingaliro amene tikufuna kuwamveketsawo m’nkhani yathu akhale otsimikizika m’maganizo mwathu. Mutasonkhanitsa mfundo zanu, mumakhala wotsimikiza za kanthu kena kamene mukufuna kuti omvetsera anu apindulepo pamene mumaliza. Yesani kuika kanthuko m’sentensi imodzi. Ngati kanthuko ndiko mfundo yaikulu ya nkhaniyo imene mukufuna kuti omvetsera anu akaikumbukire, pangani kanthuko kukhala mutu wa nkhani yanuyo. Mungachite bwino kuulemba kuti muziugwirizanitsa ndi mfundo zanu pokonzekera nkhaniyo.
3 Tsopano pamfundo zimene mwasonkhanitsazo sankhanipo malingaliro aakulu ofunikira omveketsa mutu waukulu umenewo. Ameneŵa ndiwo akhale mfundo zazikulu za nkhaniyo. Ngati mwalemba mfundo zanu pamakadi, aikeni pathebulo patsogolo panu mwa dongosolo lake. Tsopano sankhani malingaliro ena ochirikiza mfundo zazikuluzo, mukumaika lililonse m’malo ake oyenera motsatizana ndi mfundo yaikulu imene likuchirikiza. Mutasankha mfundo zazikulu ndi zina zazing’ono zosiyanasiyana ndi kuziika paautilaini yanu, mungapeze kuti zina mwa mfundo zimenezo sizikuchirikiza kwenikweni mutu wa nkhani yanu. Ngati zili choncho, musakayike konse kuzichotsa. Ndibwino kuchita zimenezo koposa kungochulukitsa m’nkhaniyo mfundo zosathandiza kapena zosagwirizana ndi mutu wake. Onetsetsaninso kuti malingaliro alembedwa mwa ndondomeko yomvekera bwino ndi yotsatirika. Mwa kutsatira njira yoperekedwa panopo, malingaliro osagwirizana bwino pa autilainiyo amaonekera mosavuta ndipo mutha kuwawongolera. Motero mungaone kuti mitu yam’kati mwa autilainiyo ikutsatizana bwino lomwe ndipo ikuchirikiza mutu waukulu wa nkhani yonse. Ndipo ngati mfundo iliyonse yokhala pansi pa mitu yam’katiyo ikupereka chichirikizo choyenera, nkhaniyo idzakhala yotsatirika bwino.
4 Mfundo za chilangizo zimene mwazisanja ndizo thunthu la nkhani yanu. Chimene changotsala tsopano ndicho mawu oyamba ndi omalizira. Pezani mawu amene mukufuna kuyamba nawo nkhani yanuyo, ndipo malinga ndi kakambidwe kamene mwakonzekera, sankhani mawu omalizira amene adzalimbikitsa omvetsera anu mogwirizana ndi cholinga cha nkhani yanuyo. Tsopano mwakonzekera kuisanja bwino komalizira papepala. Mutha kuchita zimenezi m’njira zosiyanasiyana.
5, 6. Kodi autilaini ya timitu n’chiyani? nanga autilaini ya masentensi n’chiyani?
5 Mitundu ya nkhani za autilaini. Mitundu iŵiri yodziŵika kwambiri ya nkhani za autilaini ndiyo ya timitu ndi ya masentensi. Mochulukira, mitundu iŵiriyi imaphatikizidwa pamodzi. Kuti mukonze autilaini ya timitu, choyamba lembani mutu wa nkhaniyo pamwamba pa pepalalo. Ndiyeno ndandalikani mfundo zazikulu zachidule pansi pa mutu wa nkhaniwo, mfundo yaikulu iliyonse ikumayambira kumanzere kwenikweni koyambira. Mfundo zina zochirikiza mfundo yaikulu iliyonse ziziyambira chamkati pang’ono, ndiko kuti, kuloŵetsedwa m’kati pang’ono pansi pa mfundo yaikulu imene mfundoyo ikuchirikiza. Ngati iliyonse ya mfundo zinazi ilinso ndi mfundo zina zowonjezera zoichirikiza, zimenezi zizikankhiridwa cham’kati ndithu. Tsopano mutha kuona mwa kungoyang’ana mofulumira papepala lanu mfundo zimene zili zazikulu kwenikweni zimene mukufuna kuti omvetsera anu azidziŵe. Zimenezi n’nzothandiza pokamba nkhani chifukwa mutha kugogomezera mfundozo, mukumabwereza mawu ofunika okhala ndi lingaliro lalikulu pamene mukulankhula kuti zimveketsedwe bwino ndi kusaiŵalika msanga. Chitani zimenezi ndi mfundo yaikulu iliyonse poifotokoza. Chofunika kwambiri pamtundu umenewu wa autilaini ndicho kulemba mawu achidule koma olunjika pamfundo iliyonse.
6 Mtundu wina wodziŵika kwambiri ndiwo autilaini ya masentensi. Mu autilaini ya mtundu umenewu, maganizo onse kaŵirikaŵiri amalembedwa monga masentensi athunthu koma ophatikizapo zambiri moti sentensi iliyonse imakhala ndi ganizo lonse lalikulu monga ndime ya nkhaniyo. Ndithudi, ena mwa masentensi ameneŵa, angayambire chamakati pang’ono pansi pa ena kuti mfundo zazikulu za nkhaniyo zionekere. Pokamba nkhani, nthaŵi zina wokambayo amaŵerenga sentensi mmene yakhalira kenako n’nkuifotokoza. Mitundu yonse iŵiriyi ya maautilaini ili ndi maubwino ake. Autilaini ya masentensi, popeza imafotokoza mokwanirapo maganizo onse, kaŵirikaŵiri imakhala bwinopo pankhani zokonzedwa mlungu umodzi pasadakhale kapena zimene zimakambidwa mobwerezabwereza, makamaka patapita miyezi ingapo, monga zimakhalira ndi nkhani zapoyera
7, 8. Ponena za kakambidwe kenikeniko ka nkhani, kodi mungachitenji ndi autilaini yanu?
7 Mutha kugwiritsa ntchito uliwonse pamitundu iŵiri imeneyi ya maautilaini, ya masentensi kapena ya timitu, monga autilaini yoyambirira, ndipo itha kukhala yokwanira monga momwe mungafunire. Mwa njira imeneyi mutha kuphatikizamo mfundo zonse zabwino kwambiri zimene mungafune kuzimveketsa kwa omvetsera anu. Komabe, ena polankhula nkhani amafuna autilaini yofupikirapo. Pokonza nkhani yanu yoti mukakambe mutha kukhala ndi maautilaini onse aŵiri patsogolo panu. Yesezani ndi autilaini yolongosola zochulukirapo kufikira mutasunga m’maganizo tsatanetsatane wa mfundo zonse zimene muli nazo pa autilaini yanu yoyambirira. Pamene mutha kukumbukira mfundo zimenezi kuchokera pa autilaini yofotokoza zambiriyo, ndiye kuti mwakonzekera kuikamba nkhaniyo.
8 Mwachidule, izi ndizo mfundo zazikulu zokonzera autilaini. Ndi bwino tsopano kuti tifotokoze mwatsatanetsatane zigawo zazikulu zitatu za nkhani.
9-12. (a) Kodi cholinga cha mawu oyamba a nkhani n’chiyani? (b) Perekani chitsanzo cha mtundu umodzi wa mawu oyamba.
9 Mawu oyamba. Cholinga cha mawu oyamba chiyenera kukhala kukopa chidwi cha omvetsera anu. Masentensi oyambirira ayenera kukopera chidwi chawo ku nkhani yanu ndi kuwathandiza kuona chifukwa chake ili yofunika kwa iwo. Makamaka sentensi yoyamba imafunikira kulingalira kozama. M’pofunika kuti sentensiyo ipangitse kumvana bwino pakati pa inu ndi omvetsera, osati kuwalamula kapena kumvekera monga kuwatsutsa.
10 Mawu oyamba alipo mitundu yambiri yosiyanasiyana. Mutha kugwiritsa ntchito fanizo, kapena kugwira mawu odziŵika bwino. Mungayambe ndi kutchula chothetsa nzeru chofuna yankho. Mwina mbiri ya nkhaniyo ingakhale mawu anu oyamba nawo. Mungayambe mwa kufunsa mafunso angapo. Mwinanso mungatchule mwachidule mfundo zazikulu zimene muti muzifotokoze.
11 M’pofunika kuti mawu oyamba ayenerane bwino ndi nkhaniyo. N’chifukwa chake fanizo lokopa chidwi lingakhale logwira mtima kwambiri, makamaka ngati wokamba nkhaniyo aligwiritsabe ntchito m’nkhani yake yonse. Zimenezi zidzathandiza kuti nkhaniyo ikhale yosangalatsa ndi yosavuta kutsatira ndi kukumbukira, komanso idzakhala yogwirizana bwino, malinga ngati fanizolo lasankhidwa bwino.
12 Chidwi chimene omvetsera angasonyeze chimadalira kwenikweni pa kakambidwe ka mawu anu oyamba. Mlankhuli ayenera kuyamba nkhani yake ndi mawu amphamvu komanso achidaliro, osadodoma kapena kumveka okayikira. Pa chifukwa chimenechi alankhuli ena amaona kuti n’kothandiza kwambiri kulemba sentensi yoyamba kapena aŵiri a nkhani yawo, kuti akhale ndi chiyambi chosadodoma.
13-16. (a) Fotokozani mmene mungakonzere thunthu la nkhani. (b) Kodi kagaŵidwe ka nthaŵi kayenera kugwirizana motani ndi kakonzedwe ka thunthu la nkhani?
13 Thunthu la nkhani. Zilipo njira zambiri zimene mungakonzere thunthu la nkhani yanu. Mungayambe ndi mfundo zing’onozing’ono kenako n’kumakwera mpaka pachimake, mfundo zamphamvu kwambiri zikumafotokozedwa potsirizira pake. Mukhozanso kupereka mfundozo mwa tsatanetsatane wa nthaŵi kapena zaka, monga nkhani yolembedwa pa Machitidwe 7:2-53. Njira ina yabwino ndiyo kugaŵa nkhaniyo m’zigawo zingapo zazikulu malinga ndi mfundo zazikulu za mutu wake waukulu. Mwachitsanzo, ngati mutu waukulu unali “Kuomboledwa ku Imfa,” mungagaŵe nkhaniyo m’mfundo zazikulu izi, “Mmene Imfa Inakhalirako,” “Mtundu wa Anthu Sutha Kupereka Dipo,” “Ndani Yekhayo Angapereke Dipo, ndi Chifukwa Chake,” ndi “Madalitso Ochokera ku Dipo Loperekedwalo.”
14 Nthaŵi zina mungaone kuti mutha kugaŵa nkhani yanu m’magulu achibadwa, monga mmene anachitira Paulo popereka malangizo, choyamba ku mpingo wonse, kenako kwa akazi okwatiwa, ndiyeno kwa amuna okwatira komanso kwa ana. (Onani Aefeso, machaputala 5 ndi 6.) Kapena mungapeze kuti nkhani yanu imafuna kuti mufotokoze chochitika ndi zotsatirapo zake, kapena kuti mutchule vuto linalake kenako mupereke yankho lake kapena mankhwala a vutolo. Nthaŵi zina mutha kugwiritsa ntchito bwino lomwe njira ziŵiri kapena zoposerapo mwa zimene tatchulazo.
15 Kungofotokoza zochitika, popanda kutsatira kwenikweni dongosolo la nthaŵi pamene zinthuzo zinachitika, ndiyo njira yofala yokambira nkhani. Mfundo zolongosola zinthu kaŵirikaŵiri zimawonjezera zochuluka ku nkhani yanu. Komabe nkhani zinanso zitha kukonzedwa mwa autilaini yokondweretsa pa mfundo zina zochirikiza kapena zotsutsa nkhani ina yapanthaŵiyo.
16 Pofuna kusunganso nthaŵi, musachulukitse mfundo zambiri mu autilaini yanu. Ngati mulibe nthaŵi yokwanira yoti mufotokoze mfundo zabwino, phindu lake la mfundozo limatayika. Komanso munthu sayenera kulongosola zonse zimene amadziŵa pankhaniyo nthaŵi imodzi. Mwina mfundo zina za nkhaniyo zingadzafotokozedwe nthaŵi ina. Gaŵani nthaŵi yolinga mfundo iliyonse yaikulu m’nkhani yanuyo ndiyeno, sinthani unyinji wa mfundo zanu kuti zigwirizane ndi nthaŵi. Chofunika kwenikweni sindicho kuchuluka kwa mfundo ayi, koma kugwira kwake mtima.
17-20. N’chifukwa chiyani mawu omalizira ali ofunika kwambiri, ndipo angakonzedwe m’njira zotani?
17 Mawu omalizira. Chigawo chomalizira cha nkhani iliyonse chimafunikira kuchikonzekera bwino kwambiri. Cholinga chake ndicho kugwirizanitsa mfundo zonse za nkhaniyo ndi kuzisumika pamodzi kotero kuti zikhutiritse omvetsera ndi kuti ziwasonkhezere kuchitapo kanthu pa zimene azimvazo. Komabe chigawochi chiyenera kukhala chachifupi komanso cholunjika pa mfundo zenizeni.
18 Ilipo mitundu ingapo ya mawu omalizira imene mungasankhe malinga ndi mutu wa nkhani umene mwaufutukula. Mutha kundandalika mwachidule mfundo zazikulu za nkhaniyo mwatsatanetsatane, zikumatsogolera ku mawu omalizira. Kapena mawu anu omalizira angakhale mwa kutanthauzira mfundozo, kumveketsa kwa omvetserawo mmene zingagwirire ntchito kwa iwo, ndi kuwauza zimene angachite kuti apindule ndi chidziŵitso chimene achipezacho. Ponena za nkhani zina, makamaka maulaliki okambidwa mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, n’kofunika kukhala ndi mawu omalizira osonkhezera munthu. Mwachitsanzo, mawu omalizira angasonkhezere mwininyumba kulandira buku kapena kulola kumaphunzira naye Baibulo panyumba pake.
19 Mawu omalizira angakhalenso okwera kupita ku mfundo yaikulu imene iyenera kutsala m’maganizo a omvetsera. Kuti mumalize nkhani mogwira mtima, m’pofunikiranso kuphatikiza m’mawu omalizirawo kanthu kena kamene mwakatchula m’mawu oyamba. Mutha kutchulanso fanizo kapena mawu ogwidwa amene munayamba nawo. Kaŵirikaŵiri, kufunika kopanga chosankha ndi kuchikwaniritsa kumasonyezedwa m’mawu omalizira. Chitsanzo chabwino kwambiri ndicho mawu a Yoswa pomaliza mawu ake otsazikira ali pafupi kumwalira.—Yos. 24:14, 15.
20 Choncho mungaone kuti nkhani yolembedwa mu autilaini yabwino iyenera kukhala ndi mawu oyamba okopa chidwi. Iyenera kukhala ndi mafotokozedwe otsatirika bwino a mfundo zazikulu zosankhidwa mosamala zochirikiza mutu wa nkhani. Ndipo iyenera kukhala ndi mawu omalizira osonkhezera omvetsera kuti achitepo kanthu pa uphungu wa m’Malemba umene waperekedwa. Mbali zonsezi ziyenera kukonzekeredwa bwino pokonza autilaini. Kukonza autilaini yanu mwaluso kungakusungireni nthaŵi, ndipo kumapangitsa nkhani kukhala yatanthauzo ndi yokhomereza chilangizo chokhalitsa m’maganizo mwa omvetsera.