Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be tsamba 39-tsamba 42
  • Kukonza Autilaini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukonza Autilaini
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pendani, Sankhani, Ndipo Yalani
  • Kukonza Autilaini
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kugogomeza Mutu wa Nkhani ndi Mfundo Zazikulu
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kuunika Mfundo Zazikulu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be tsamba 39-tsamba 42

Kukonza Autilaini

ANTHU ambiri akapatsidwa nkhani yoti akambe, amaloŵa ntchito yolemba mawu onse a nkhaniyo, kuyambira pa mawu oyamba mpaka kumawu omaliza. Pofika poti amaliza nkhaniyo, angakhale atailemba mobwerezabwereza. Nthaŵi zina zimawatengera maola ambiri.

Kodi ndi mmene inunso mumakonzera nkhani zanu? Kodi mungakonde kudziŵa njira yosavuta? Mukaphunzira kakonzedwe ka autilaini, simudzafunikiranso kumalemba mawu onse. Mukafika pamenepo, muzikhala ndi nthaŵi yokwanira yofotokozera nkhani yanu. Nkhani zanu zizikhala zosavuta kukamba, komanso zomveka zokoma ndi zolimbikitsa omvera anu.

Kunena za nkhani za onse zokambidwa pampingo, pamakhala autilaini yokonzedwa kale. Koma sizikhala choncho ndi nkhani zina zambiri. Angangokupatsani mutu wa nkhani basi. Kapena angakupempheni kukamba nkhani kuchokera pa nkhani yofalitsidwa kale. Nthaŵi zina mungapatsidwe malangizo, koma ochepa chabe. Pankhani ngati zimenezo, mudzafunikira kudzikonzera nokha autilaini.

Chitsanzo chimene chili patsamba 41 chidzakuthandizani kuona mmene mungakonzere autilaini yaifupi. Onani kuti mfundo yaikulu iliyonse imayambira kumanzere kwenikweni ndipo yalembedwa m’malembo aakulu. Pansi pa mfundo yaikulu iliyonse pali malingaliro oichirikiza. Mfundo zowonjezera zofotokozera maganizowo zaikidwa pansi pakepo ndipo zikumayambira m’kati pang’ono kuchokera kumanzere. Ipendeni mosamala autilaini imeneyi. Onani kuti mfundo zazikulu ziŵirizo zikukhudzana mwachindunji ndi mutu wa nkhani. Onaninso kuti mfundo zing’onozing’ono sizili mfundo zosangalatsa zoima pazokha. M’malo mwake, iliyonse imachirikiza mfundo yaikulu imene ili pamwamba pakepo.

Mukakonza autilaini, mwina siingaoneke yofanana ndendende ndi yachitsanzoyo. Koma ngati mumvetsa bwino malangizo amene tafotokozawa, adzakuthandizani kuyala bwino mfundo zanu ndi kukonzekera nkhani mosachita kutenga nthaŵi yochuluka kwambiri. Kodi muyenera kuyambira pati?

Pendani, Sankhani, Ndipo Yalani

Choyamba, mufunikira mutu wa nkhani. Mutu wa nkhani sumangokhala wachisawawa monga mawu amodzi basi. Uyenera kukhala ganizo lalikulu limene mukufuna kulifotokoza, ndipo umasonyeza mbali ya nkhani yanu imene mukufuna kuikamba. Ngati mutu wa nkhani ulipo kale, pendani liwu lalikulu lililonse mosamala. Ngati nkhani yanu ikuchokera m’nkhani yofalitsidwa kale ndipo mufunikira kugwiritsa ntchito mutu wa nkhaniyo, ŵerengani nkhaniyo mukumaigwirizanitsa ndi mutuwo. Ngati mwapatsidwa nkhani yokha, muyenera kusankha nokha mutu wake. Koma musanatero, ndi bwino kuyamba mwafufuza. Mwa kukhala ndi maganizo otseguka, kaŵirikaŵiri mudzapeza mfundo zatsopano.

Pamene mukutenga masitepe ameneŵa, nthaŵi zonse dzifunseni kuti: ‘N’chifukwa chiyani mfundo zimenezi zili zofunika kwa omvera anga? Kodi cholinga changa n’chiyani?’ Chisakhale kungofuna kumaliza nkhaniyo kapena kungokamba nkhani yosangalatsa ayi. Chikhale kukwaniritsa kanthu kena kopindulitsa omvera anu. Pamene cholinga chanu mwachipeza, chilembeni. Chikumbukireni nthaŵi zonse pamene mukukonzekera.

Mutapeza cholinga chanu ndi kusankha mutu wogwirizana ndi cholingacho (kapena kupenda mmene mutu umene mwapatsidwa ukugwirizanira ndi cholingacho), mumakhala wokhoza kufufuza muli ndi cholinga. Funafunani mfundo zimene zidzakhala zopindulitsa omvera anu. Musamafune mfundo zilizonse, koma funafunani mfundo zopatsa chidziŵitso ndi zothandizadi. Musapambanitse m’kufufuza kwanu. Kaŵirikaŵiri mudzapeza mfundo zochuluka kuposa zimene mungagwiritse ntchito, choncho muyenera kusankha zofunikira zokha.

Dziŵani mfundo zazikulu zimene ziyenera kufotokoza mutu wanu ndi kukwaniritsa cholinga chanu. Zimenezi zidzakhala ngati maziko anu, kapena kuti autilaini yanu. Kodi payenera kukhala mfundo zazikulu zingati? Mwina ziŵiri n’zokwanira ngati ili nkhani yaifupi, ndipo nthaŵi zambiri zisanu zimakhala zokwanira ngakhale itakhala nkhani ya ola limodzi. Mfundo zanu zikakhala zocheperapo, kumakhala kosavuta kuti omvera anu azikumbukire.

Mutadziŵa mutu wanu ndi mfundo zazikulu, yalani mfundo zimene mwafufuzazo. Onani ndi mfundo ziti zimene zikugwirizana mwachindunji ndi mfundo zanu zazikulu. Sankhani zimene zidzapangitsa nkhani yanu kumveka yatsopano. Posankha malemba ochirikiza mfundo zanu zazikulu, pezani malingaliro amene angakuthandizeni kufotokoza malembawo m’njira yopindulitsa. Ikani mfundo iliyonse pansi pa mfundo yake yaikulu. Ngati mfundo ina siikugwirizana bwino ndi iliyonse ya mfundo zanu zazikulu, ichotseni—ngakhale itakhala yosangalatsa kwambiri—kapena ilembeni m’faelo kuti mukaigwiritse ntchito nthaŵi ina. Sungani mfundo zofunikira zokha. Ngati mulemba zambiri, mudzayamba kulankhula mothamanga ndipo nkhani yanu idzakhala yosagwira mtima. Kuli bwino kwambiri kukamba mfundo zochepa zimene zili zaphindu kwa omvera, komanso zimene mukhoza kuzikamba bwino. Musadye nthaŵi.

Pamene mwafikapa tsopano, yalani mfundo zanu m’dongosolo la tsatanetsatane. Wolemba nkhani za Uthenga Wabwino, Luka, anachitanso zimenezi. Atasonkhanitsa mfundo zambiri zokhudza nkhani yake, anaziyala mwa “tsatanetsatane.” (Luka 1:3) Mukhoza kuyala mfundo zanu m’dongosolo la zaka kapena la timitu, malinga ndi zochitika ndi zochititsa, kapena malinga ndi vuto ndi njira yake yolithetsera. Zimadalira njira imene mwaiona kukhala yabwino koposa kuti mukwaniritse cholinga chanu. Musamasinthe mwadzidzidzi kuchoka pa ganizo ili kupita pa lina. Muyenera kuwatsogolera bwinobwino omvera anu kuchokera pa lingaliro ili kupita pa lina, m’malo mosiya mipata yopanda ulalo. Umboni umene mukupereka uyenera kuthandiza omvera kuona mfundo zokhutiritsa. Pamene mukuyala mfundo zanu, lingalirani za mmene nkhani yanu iti ikamvekere kwa omvera anu. Kodi akatha kutsatira pamene muzifotokoza mfundo zanu? Kodi akalimbikitsidwa kuchita zimene akamva, mogwirizana ndi cholinga chanu?

Chotsatira, konzani mawu oyamba okopa chidwi pa nkhani yanu ndi osonyeza omvera anu kuti zimene muwafotokozere n’nzaphindu kwa iwo. Kungakhale bwino kulemba masentensi angapo oyambirira. Chinthu chomaliza, konzani mawu omaliza olimbikitsa komanso ogwirizana ndi cholinga chanu chija.

Ngati mukonza autilaini yanu nthaŵi ikalipo, mudzakhala ndi nthaŵi yabwino yoti muisalaze bwinobwino lisanafike tsiku lokamba nkhani yanu. Mungaonenso kuti ndi bwino kuchirikiza mfundo zanu ndi ziŵerengero zingapo, chitsanzo, kapena chochitika china. Kugwiritsa ntchito chochitika cha panthaŵiyo kapena nkhani ina yokhudza ambiri kuderako kungathandize omvera anu kuona msanga kufunika kwa nkhaniyo. Pamene mukuipenda nkhani yanuyo, mungaonenso mipata ina yosinthira mfundo zanu kuti ziyenerere omvera anu. Kachitidwe kobwereranso m’mfundo zanu ndi kuzisalaza bwinobwino n’kofunikira pokonza nkhani kuti ikhale yogwira mtima.

Okamba nkhani ena angafunikire kulemba manotsi ochulukirapo kuposa ena. Koma ngati musanja mfundo zanu pansi pa mfundo zazikulu zingapo, chotsani zimene sizikuchirikiza mfundo zazikuluzo, ndipo lembani malingaliro anuwo mwatsatanetsatane. Mudzaona kuti mukazoloŵera simudzafunikiranso kumalemba zonse. Imeneyo ndi njira imodzi yopulumutsa nthaŵi yochuluka! Ndipo nkhani zanu zizikhala zogwira mtima kwambiri. Umenewo udzakhala umboni wakuti mukupinduladi ndi maphunziro anu a Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.

MMENE MUNGAKONZERE AUTILAINI

  • Pezani chifukwa chake nkhani yanu ilili yofunika kwa omvera anu ndiponso dziŵani cholinga chanu

  • Sankhani mutu wa nkhani; ngati ulipo kale, upendeni mosamala

  • Sanjani mfundo zanu, zikhale zothandiza zokhazokha

  • Sankhani mfundo zazikulu

  • Yalani mfundo zanu mwadongosolo; zoyenera zokhazokha

  • Konzani mawu oyamba okopa chidwi

  • Konzani mawu omaliza olimbikitsa

  • Bwererani m’nkhani yanu; isalazeni bwinobwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena