PHUNZIRO 25
Kugwiritsa Ntchito Autilaini
ANTHU ambiri amachita mantha poganiza zokamba nkhani kuchokera pa autilaini. Amakhala achidaliro akalemba zonse zimene akukalankhula kapena akaziloŵeza pa mtima.
Koma kwenikweni, tonse timalankhula masiku onse mosachita kulemba zimene tikufuna kunena. Timangolankhula kuchokera m’maganizo kwa a m’banja mwathu kapena mabwenzi athu. Timateronso polalikira mu utumiki wa kumunda. Ndiponso timatero popereka pemphero, kaya lamseri kapena patsogolo pa anthu.
Pamene mukukamba nkhani, kodi mumaona kusiyana mukagwiritsa ntchito nkhani yoŵerenga kapena autilaini? Ngakhale kuti kuŵerenga nkhani yolemba yonse kungathandize kunena zinthu zolondola zokhazokha ndi mawu osankhidwa kale mosamala, iko sikuwafika pamtima anthu kwenikweni. Mukaŵerenga masentensi angapo, kaŵirikaŵiri mumayamba kulankhula mwanjira yosiyana ndi chibadwa chanu. Ngati omvera anu aona kuti mukuganizira kwambiri za mawu a papepala koposa iwo, ambiri angasiye kumvetsera. Amamvetsera akaona kuti mukuganiza za iwowo ndipo mukugwirizanitsa nkhani yanu ndi mikhalidwe yawo. Kuti nkhani yanu ikhale yolimbikitsa koposa, muyenera kuikamba kuchokera mu mtima.
Cholinga cha Sukulu ya Utumiki wa Mulungu n’chakuti itithandize pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Sikuti tikakumana ndi anzathu timatulutsa pepala lolemba ndi kuyamba kuwaŵerengera maganizo athu pofuna kulankhula mawu osankhidwa bwino. Ngakhale mu utumiki wa kumunda, sitiyenda ndi pepala lokhala ndi mawu onse oti tiziŵerenga, kuti tingaiŵale mfundo zina zimene takonzekera kukambirana ndi anthu. Pokamba nkhani ya m’sukulu yosonyeza ulaliki wa kumunda, yesetsani kulankhula mwachibadwa. Ngati mwakonzekera bwino, mudzaona kuti autilaini, kaya ya m’maganizo kapena yolemba, imakhala yokwanira kukukumbutsani mfundo zazikulu zimene mwakonzekera kuzifotokoza. Koma ndi motani mmene mungakhalire ndi chidaliro choyamba kugwiritsa ntchito autilaini?
Konzani Maganizo Anu. Kuti autilaini ikakuthandizeni bwino pokamba nkhani, muyenera kukonza maganizo anu. Zimenezi sizikutanthauza kusankha mawu oti mukawalankhule ayi. Zikungotanthauza kuyamba mwalingalirapo musanakalankhule.
Kaŵirikaŵiri, munthu wasontho kapena kuti waphuma amabwetuka zinthu zimene pambuyo pake amakhumba akanapanda kuzilankhula. Komanso munthu wina angakhale wolankhula zosatsatirika bwinobwino, kumangoti watchula mfundo iyi wasiya, n’kukatchulanso mfundo ina n’kusiya, choncho basi. Zofooka zonse ziŵirizi zingathetsedwe mwa kuima kaye ndi kukonza ka autilaini ka m’maganizo musanayambe kulankhula. Choyamba khalani ndi cholinga m’maganizo, kenako pezani ndondomeko yoti muitsatire kuti mukwaniritse cholingacho, ndiyeno yambani kulankhula.
Kodi mukukonzekera utumiki wa kumunda? Khalani ndi nthaŵi yokonza bwino chola chanu cha m’munda komanso maganizo anu. Ngati mukufuna kugwiritsa ntchito ulaliki wa mu Utumiki Wathu wa Ufumu, uŵerengeni ulalikiwo kangapo konse kuti mumvetse mfundo zake zazikulu. Tchulani mfundo zazikuluzo m’masentensi aŵiri achidule. Zilankhuleni m’mawu anuanu ndi mogwirizana ndi mikhalidwe ya m’gawo lanu. Mudzaona kuti n’kothandiza kukhala ndi autilaini ya m’maganizo. Kodi imeneyo iyenera kukhala ndi mbali ziti? (1) Mawu oyamba; mungatchule nkhani imene ili m’maganizo mwa anthu ambiri kwanuko. Pemphani munthuyo kuperekapo maganizo ake. (2) Khalani ndi mfundo imene mwaikonzekera pankhaniyo, kuphatikizapo lemba limodzi kapena aŵiri osonyeza zimene Mulungu analonjeza pothetsa vutolo. Ngati mwayi ulipo, mveketsani mfundo yakuti Yehova adzachita zimenezo kupyolera mu Ufumu wake, boma lake lakumwamba. (3) Limbikitsani munthuyo kuchitapo kanthu pazimene mwakambirana. Mungamugaŵire buku, Baibulo, kapena zonse ziŵiri ndi kupangana naye zoti mudzakambiranenso nthaŵi ina.
Autilaini imene mungafunikire pa kukambirana koteroko ndi yam’maganizo basi. Ngati mukufuna kuyang’ana pa autilaini yolemba musanalankhule ndi munthu woyamba, autilainiyo iyenera kukhala ndi mawu oyamba ochepa chabe, kenako lemba limodzi kapena aŵiri, ndi mawu omaliza pang’ono. Kukonzekera ndi kugwiritsa ntchito autilaini yotero kungatiletse kulankhula mwachisawawa, ndipo tingapereke uthenga womveka bwino wosavuta kukumbukira.
Ngati ndi funso kapena nkhani imene kaŵirikaŵiri anthu amatsutsa m’gawo lanu, ndi bwino kuifufuza nkhaniyo. Nthaŵi zambiri, mudzangofunikira mfundo zazikulu ziŵiri kapena zitatu limodzi ndi malemba opereka umboni. Mungapeze autilaini imene mukuifunayo pa “Nkhani za m’Baibulo Zokambirana” kapena pa timitu ta malembo akuda kwambiri m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Mungagwirenso mawu oyenerera kuchokera m’zolembedwa zina zosakhala za Mboni amene mungafune kuphatikizapo. Lembani autilaini yachidule yophatikizapo mawu ogwidwawo, ndipo iikeni m’mabuku anu opita nawo mu utumiki wa kumunda. Ngati mwininyumba afunsa funsolo kapena atsutsa nkhaniyo, muuzeni kuti mungakonde kupereka zifukwa pa zimene mumakhulupirira. (1 Pet. 3:15) Tengani zifukwazo pa autilaini imene mwakonza.
Pamene mukukaimira m’pemphero banja lanu, gulu la phunziro la buku, kapena mpingo, m’pofunikanso kukonza bwino maganizo anu. Pa Luka 11:2-4, Yesu anapereka kwa ophunzira ake autilaini yosavuta ya pemphero latanthauzo. Popereka kachisi kwa Mulungu ku Yerusalemu, Solomo anapereka pemphero lalitali. Mwachidziŵikire, iye anaganiziratu zimene anayenera kutchula m’pemphero. Choyamba analankhula za Yehova ndi lonjezo Lake kwa Davide; kenako analankhula za kachisi; ndiyeno chimodzi ndi chimodzi, anatchula mikhalidwe yosiyanasiyana ndi magulu a anthu. (1 Maf. 8:22-53) Tingaphunzire zambiri pa zitsanzo zimenezi.
Lembani Autilaini Yosavuta. Kodi autilaini yanu ndi yokakambira nkhani? Kodi iyenera kukhala ndi zochuluka motani?
Kumbukirani kuti cholinga cha autilaini ndicho kungokukumbutsani mfundo basi. Mungafune kulemba masentensi angapo a mawu oyamba. Koma mukatha apo, ikani maganizo pa mfundo, osati pamawu. Ngati mukufuna kulemba mfundozo, lembani masentensi afupiafupi. Mfundo zazikulu zingapo zimene mukufuna kukazifotokoza ziyenera kuonekera bwino pa autilainipo. Zingaonekere mwa kuzilemba m’malembo aakulu, mwa kuzilemba mzera kunsi kwake, kapena mwa kuziika chizindikiro chilichonse. Pansi pa mfundo yaikulu iliyonse, ndandalikani malingaliro ofotokozera mfundozo amene mukufuna kuwagwiritsa ntchito. Lembani malemba amene mukufuna kukaŵerenga. Ndi bwino kuŵerenga m’Baibulo mwenimwenimo. Lembaninso mafanizo amene mukufuna kukagwiritsa ntchito. Mungakhalenso ndi mawu ogwidwa oyenerera otengedwa m’zolembedwa zakunja. Manotsi anu azikhala omveketsa bwino mfundo. Ndipo autilainiyo idzakhala yosavuta kugwiritsa ntchito ngati ilembedwa mwaudongo.
Ena amagwiritsa ntchito autilaini yokhala ndi mawu ochepa chabe. Autilaini ingakhale ndi mawu ofunikira kwambiri, malemba amene wokambayo angawagwire mawu kuchokera pamtima, ndi zithunzi zojambula mwini pamanja kapena zotenga kwina zimene zingam’kumbutse malingaliro osiyanasiyana. Ndi manotsi osavuta ameneŵa, wokambayo akhoza kukamba nkhani yake m’ndondomeko yotsatirika komanso m’njira yokhala ngati kukambirana. Chimenechi ndiye cholinga cha phunziro limeneli.
Pamasamba 39 mpaka 42 m’buku lino, pali nkhani yakuti “Kukonza Autilaini.” Pamene mwapatsidwa kukonzekera mfundo yakuti “Kugwiritsa Ntchito Autilaini,” chimakhala chinthu chothandiza kwambiri kuŵerenga nkhani imeneyo.
Kugwiritsa Ntchito Autilaini. Cholinga chanu tsopano, sindicho kungokonza autilaini ya nkhani yanu ayi; koma kugwiritsa ntchito autilainiyo mwaluso.
Sitepe loyambirira ndilo kukonzekera kakambidwe kake. Yang’anani mutu wake, ŵerengani mfundo yaikulu iliyonse, ndipo tchulani mmene mfundo yaikulu iliyonse ikugwirizanira ndi mutuwo. Onani ndi nthaŵi yochuluka motani imene mungafotokozere mfundo yaikulu iliyonse. Tsopano bwererani ndipo pendaninso mfundo yaikulu yoyamba. Pendani malingaliro ali pamenepowo, malemba, mafanizo, ndi zitsanzo zimene mwasankha zokafotokozera mfundoyo. Ŵerengani chigawo chimenecho mobwerezabwereza kufikira chitamveka bwino m’maganizo mwanu. Chitani chimodzimodzi pa mfundo yaikulu iliyonse. Ngati kungakhale kofunika, onani zimene mungachotsepo kuti mukasunge nthaŵi. Ndiyeno bwererani m’nkhani yonseyo. Ikani maganizo pa malingaliro, osati pa mawu. Musailoŵeze pamtima nkhaniyo.
Pokamba nkhaniyo, muyenera kumayang’ana omvera anu moyendera nawo pamodzi. Mukaŵerenga lemba, lingalirani palembalo pamodzi ndi omvera anu m’Baibulo momwemo popanda kuyang’ana pa manotsi anu. Mofananamo, ngati mugwiritsa ntchito fanizo, lifotokozeni mmene mungalifotokozere kwa anzanu; osati kuliŵerenga pa manotsi anu. Pamene mukulankhula, musamayang’ane pa manotsi anu pofuna kutchula sentensi iliyonse. Lankhulani kuchokera mu mtima, ndipo mudzawafika pamtima amene akukumverani.
Mukadziŵa luso lolankhula kuchokera pa autilaini, mudzakhala mutapyola sitepe lofunika kwambiri pa kukhala waluso pa kukamba nkhani pamaso pa anthu.