Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 28 tsamba 138-142
  • Kuyendera Limodzi ndi Omvetsera ndi Ntchito ya Notsi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyendera Limodzi ndi Omvetsera ndi Ntchito ya Notsi
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • **********
  • Kuyang’ana Omvera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kugwiritsa Ntchito Autilaini
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kukonzekera Nkhani za Onse
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 28 tsamba 138-142

Phunziro 28

Kuyendera Limodzi ndi Omvetsera ndi Ntchito ya Notsi

1. Fotokozani kufunika kwa kuyendera limodzi ndi omvetsera ndi mmene notsi zimathandizira m’chimenechi.

1 Kuyendera limodzi kwabwino ndi omvetsera anu kumathandiza kwambiri pophunzitsa. Iwo amakulemekezani ndipo kuphunzitsa kwanu kumakhala kogwira mtima kwambiri. Kuyendera nawo limodzi kumatheketsa mgwirizano waukulu moti inuyo monga mlankhuli mumatha kuzindikira msanga mulimonse mmene iwo akulabadilira. Notsi zimakuthandizani kudziŵa kaya mukuyendera limodzi ndi omvetsera kapena ayi. Notsi zochuluka kwambiri zingakhale chopinga; koma kugwiritsa ntchito notsi mwaluso sikungakupombonezeni, ngakhale ngati mikhalidwe ingafune kuti notsizo zikhale zochulukirapo kuposa nthaŵi zonse. Zimenezo zimatheka chifukwa mlankhuli waluso satayana ndi omvetsera ake kaya mwa kuyang’ana panotsi kwa nthaŵi yaitali kapena panthaŵi zolakwika. Mfundo imeneyi yaikidwanso pasilipi lanu la Uphungu wa Kulankhula, ndipo yatchedwa “Kuyendera limodzi ndi omvetsera, ntchito ya notsi.”

2-5. N’chiyani chimatheketsa kuyendera limodzi ndi omvetsera mwa kuwayang’ana?

2 Kuyendera limodzi ndi omvetsera mwa kuwayang’ana. Kuyendera nawo limodzi mwa kuwayang’ana kumatanthauza kuona omvetsera anu. Sikutanthauza kuyang’ana omvetsera mwachisawawa koma kuwayang’ana mmodzimmodzi. Kumatanthauza kuona chimene nkhope zawo zikukuuzani ndi kulabadira moyenerera.

3 Kuyang’ana omvetsera anu sikutanthauza kungoyendetsa maso kuchokera uku mpaka uku kuti musaphonye aliyense ayi. Yang’anani munthu mmodzi mwa omvetserawo ndipo nenani sentensi imodzi kapena aŵiri kwa iye. Ndiyeno yang’anani wina ndi kunena masentensi angaponso kwa iyeyo. Koma samalani, musayang’anitsitse munthu mmodzi kwa nthaŵi yaitali moti mpaka womvetserayo n’kuchita manyazi, kapena musangosumika maso pa anthu oŵerengeka chabe mwa omvetsera onsewo. Pitirizani kuyendetsa maso anu mwa omvetsera onse motero, koma, pamene mukulankhula kwa munthu mmodzi, lankhulani naye ndithu ndipo onani mmene akuchitira musanasamukire kwa wina. Ikani notsi zanuzo pagome lolankhulirapo kapena m’manja kapenanso m’Baibulo kotero kuti muthe kuyang’anapo mofulumira, mwa kungoponyapo maso. Ngati mwaika notsi zanu m’njira yofuna kuti muziŵeramitsa mutu wanu wonse kuti muzione, pamenepo kuyendera limodzi ndi omvetsera kudzasokonekera.

4 Phungu wanu sadzangofuna kuona ngati notsi zanu mukuziyang’ana kaŵirikaŵiri, komanso adzafuna kuona ngati mukuziyang’ana panthaŵi yoyenera. Ngati muyang’ana notsi zanu pamene mukufika pachimake, simudzaona kachitidwe ka omvetsera anu. Ndiponso ngati muyang’ana notsi zanu pafupipafupi kwambiri, mudzatayanso omvetsera anu. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimasonyeza kuti munthuyo ali ndi chizoloŵezi cha mantha kapena sanakonzekere nkhani yake mokwanira.

5 Nthaŵi zina alankhuli ozoloŵera amayembekezeka kulankhula nkhani yonse kuchokera pankhani yolembedwa kale, ndipo chimenechi chimachepetsako kuyang’ana omvetsera kuti muyendere limodzi. Koma ngati nkhaniyo akuidziŵa bwino chifukwa choikonzekera bwino, amatha kuyang’ana omvetsera awo nthaŵi ndi nthaŵi popanda kupombonezeka, ndipo zimenezo zimawalimbikitsa kuti aŵerenge mwaumoyo.

6-9. Tchulani njira ina yoyendera limodzi ndi omvetsera, komanso mbuna zimene tiyenera kuchenjera nazo.

6 Kuyendera limodzi ndi omvetsera mwa mawu owaphatikizamo. Kumeneko n’kofunika kwambiri mofanana ndi kuyang’ana omvetsera. Kumaphatikizapo mawu amene mugwiritsa ntchito polankhula ndi omvetsera anu.

7 Polankhula kwa munthu wina panokha mumagwiritsa ntchito mawu owaphatikizamo akuti “inu,” “zanu” kapena “ife,” “zathu.” Pamene kuli koyenera, mutha kulankhula m’njira yofananayo kwa omvetsera ochulukirapo. Nkhani yanuyo ipangeni ngati kuti mukukambirana ndi munthu mmodzi kapena aŵiri panthaŵi imodzi. Ayang’anitsitseni kwambiri kotero kuti mulankhule ngati mukuwayankha zimene akufunsani. Zimenezo zidzapangitsa nkhani yanu kumveka ngati kulankhulana kwa anthu aŵiri.

8 Komabe chenjezo pang’ono. Peŵani kuchita chizoloŵezi kwambiri ndi omvetsera anu. Muyenera kuzoloŵerana mwaulemu monga zimakhalira pokambirana ndi munthu mmodzi kapena angapo pakhomo mu utumiki wakumunda, koma mukhoza ndipo muyenera kukhala wolunjika.

9 Mbuna ina nayi. Muyenera kusamala pogwiritsa ntchito aloŵam’malo oloza (personal pronoun). Mwachitsanzo, m’nkhani yonena za kupulupudza, simungagwiritse ntchito mawu osonyeza ngati kuti omvetsera anuwo ali opulupudza. Kapena, ngati ndi pamsonkhano wautumiki ndiye mukunena za maola otsika, mungachite bwino kudziphatikizapo inumwini, mwa kugwiritsa ntchito mloŵam’malo wakuti “ife” m’malo mwakuti nthaŵi zonse muzingoti “inu.” Kumvera chifundo ena ndi kuwaganizira kungatithandize kupeŵa mbuna imeneyo.

**********

10, 11. N’chiyani chiyenera kutilimbikitsa kuphunzira kugwiritsa ntchito autilaini?

10 Ntchito ya autilaini. Atsopano oŵerengeka ongoyamba kumene kulankhula nkhani amakamba kuchokera pa autilaini. Nthaŵi zambiri amalemberatu nkhani yonse kenako n’kuilankhula moiŵerenga kapena kuchokera pamtima atailoŵeza. Kumayambiriro phungu wanu adzanyalanyaza zimenezo, koma pamene mufika pa luso lakuti “Ntchito ya autilaini” pasilipi lanu la Uphungu wa Kulankhula, iye adzakulimbikitsani kulankhula kuchokera panotsi. Pamene muzoloŵera, mudzaona kuti mwapita patsogolo kwambiri pakulankhula nkhani pamaso pa anthu.

11 Ngakhale ana aang’ono ndi achikulire osatha kuŵerenga amalankhula nkhani, mwa kugwiritsa ntchito mafanizo popereka maganizo. Mukhoza kukonzekera nkhani yanu ndi autilaini yosavuta, mofanana ndi maulaliki a Malemba osonyezedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Nthaŵi zonse mumalankhula ndi anthu mu utumiki wakumunda popanda nkhani yolemberatu. Mungateronso mosavuta m’sukulu mutangoikirapo mtima.

12, 13. Perekani maganizo a mmene mungapangire autilaini.

12 Popeza cholinga cha luso limeneli n’chakuti muleke kumalemba nkhani yonse, ponse paŵiri pokonzekera ndi polankhula, musaloŵeze pamtima nkhani yanu. Mukatero mudzawononga cholinga cha Phunziro limeneli.

13 Ngati mukugwiritsa ntchito malemba, mungadzifunse mafunso ofuna yankho akuti, Motani? Ndani? Liti? Kuti? ndi ena otero. Ndiyeno, molingana ndi kugwirizana kwake ndi nkhaniyo, gwiritsani ntchito mafunso ameneŵa monga mbali ya notsi zanu. Polankhula nkhani, ŵerengani lemba, dzifunseni nokha kapena funsani mwininyumba mafunso ameneŵa moyenerera, kenako perekani mayankho. Basitu ndi zomwezo.

14, 15. Kodi ndi zinthu zotani zimene siziyenera kutigwetsa mphwayi?

14 Atsopano amakhala ndi nkhaŵa yakuti adzaiŵala kanthu kena. Komabe, ngati mwafutukula nkhani yanu m’dongosolo labwino, palibe amene adzaona kuti mwaphonya mfundo ina ngakhale mutaiphonyadi. Ndi iko komwe, panthaŵi inoyi mfundo yaikulu imene ikuyang’aniridwa si kukwaniritsa mfundo zonse. Choncho m’pofunika kuti muphunzire kulankhula kuchokera pa autilaini.

15 N’kutheka kuti polankhula nkhani ya mtundu umenewu mudzaona ngati maluso ambiri amene mwaphunzira m’mbuyomu onse abalalika. Musade nkhaŵa kwenikweni. Amenewo abweranso okha ndipo mudzaona kuti mudzawatha bwino koposa mutadziŵa kulankhula popanda kulemba nkhani yonse.

16, 17. N’chiyani chimene tiyenera kukumbukira polemba notsi?

16 Tinenepo pang’ono za notsi zogwiritsa ntchito m’sukulu yateokalase. Cholinga cha notsi ndicho kukukumbutsani malingaliro, osati kuti muziŵerenge mmene zakhalira ayi. Komanso notsi ziyenera kukhala zachidule. M’pofunikanso kuzilemba mwaudongo, m’dongosolo labwino komanso zoŵerengeka bwino. Ngati chochitika cha nkhani yanu ndi ulendo wobwereza, ikani notsi zanu posaonekera, mwina m’kati mwa Baibulo lanu. Ngati ili nkhani ya papulatifomu ndipo mukudziŵa kuti mudzagwiritsa ntchito gome lolankhulirapo, pamenepo notsi siziyenera kukhala vuto. Koma ngati muli wosatsimikiza, konzekerani bwino pasadakhale.

17 China chimene chingakuthandizeni ndi kulemba mutu pamwamba pa notsi zanu. Mfundo zazikulu ziyeneranso kuonekera bwino. Yesani kuzilemba m’zilembo zazikulu zokhazokha kapena kulemba mzera pansi pake.

18, 19. Kodi tingapange bwanji pulakatisi yogwiritsa ntchito autilaini?

18 Pamene tikuti muyenera kugwiritsa ntchito notsi zochepa sitikutanthauza kuti kukonzekera kwanu kuzingokhala kofulumira ndi kwachisawawa. Konzani nkhaniyo choyamba mwatsatanetsatane, mukumapanga autilaini yokwanira ndithu. Ndiyeno, konzani autilaini yachiŵiri yofupikirapo. Imeneyi ndiyo autilaini imene mudzaigwiritse ntchito polankhula nkhani yanu.

19 Tsopano ikani maautilaini aŵiriwo patsogolo panu, ndiyeno pamene mukuyang’ana pa yofupikitsidwayo, lankhulani zambiri zimene mungathe pa mfundo yaikulu yoyamba. Kenako, yang’anani pa autilaini yokhala ndi zonseyo ndi kuona zimene mwaphonya. Fikani pa mfundo yaikulu yachiŵiri mu autilaini yanu yofupikitsidwayo ndi kuchitanso chimodzimodzi. M’kupita kwa nthaŵi, autilaini yaifupiyo idzakhala yozoloŵereka kwambiri kwa inu moti mukhoza kukumbukira zambiri za pa autilaini ya zambiriyo mwa kungoyang’ana notsi zanu zingapo. Mwa pulakatisi ndi kuzoloŵera mudzayamba kuzindikira mapindu a kulankhula kochokera m’maganizo ndipo nkhani yoŵerenga mudzangoigwiritsa ntchito pamene kukhaladi kofunikira. Pamenepo mudzakhala womasuka kwambiri polankhula ndipo omvetsera anu adzamvetsera ndi ulemu waukulu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena