Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 13 tsamba 124-tsamba 127 ndime 1
  • Kuyang’ana Omvera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyang’ana Omvera
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyendera Limodzi ndi Omvetsera ndi Ntchito ya Notsi
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Sonyezani Ena Chidwi mwa Kuwayang’ana Polankhula Nawo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 13 tsamba 124-tsamba 127 ndime 1

PHUNZIRO 13

Kuyang’ana Omvera

Kodi muyenera kuchita motani?

Yang’anani anthu amene mukulankhula nawo, polola maso anu kukumana ndi maso awo mwachidule, ngati zili zololeka kwanuko. Onani munthu mmodzi panthaŵi imodzi, osati gulu la anthu mwachisawawa.

N’chifukwa chiyani kuli kofunika?

M’mayiko ambiri, kuyang’ana munthu polankhulana naye kumaonetsa kuti muli naye chidwi. Kumaonetsanso kuti mukulankhula ndi chidaliro.

MASO athu amaonetsa maganizo athu ndi mmene tikumvera mu mtima. Angasonyeze kudabwa kapena mantha. Angasonyeze chifundo kapena chikondi. Nthaŵi zina, angavumbule kukayikira kapena chisoni. Ponena za anthu akwawo amene anavutika kwambiri, mwamuna wina wachikulire anati: “Timalankhula ndi maso.”

Anthu ena angaganize zinthu zina ponena za ife ndi zimene tinganene malinga ndi kumene maso athu akuyang’ana kwambiri. Kumayiko ambiri, anthu amakonda kukhulupirira munthu amene amawayang’ana mwaubwenzi. Koma amakayikira munthu amene amayang’ana pansi kapena kumbali m’malo moyang’ana munthu amene akulankhula naye. M’madera ena, kuyang’anitsitsa munthu kwambiri amakuyesa mwano, ukali, kapena kuopseza. Zimakhala choncho makamaka mwamuna polankhula kwa mkazi kapena mkazi kwa mwamuna, polankhula kwa mfumu kapena munthu wina waudindo. Ndiponso m’madera ena, ngati munthu wamng’ono ayang’ana pamaso wachikulire pokambirana naye, amati ndi kupanda ulemu.

Komabe, kumene zili zololeka, kuyang’ana munthu pamaso potchula mfundo yofunika kumathandiza kutsindika zimene mukunena. Umakhala umboni wakuti mukulankhula motsimikiza. Onani mmene Yesu anachitira ophunzira ake atadabwa kwambiri ndi mawu ake akuti: “Angapulumuke ndani?” Baibulo limati: ‘Yesu anawayang’ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.’ (Mat. 19:25, 26) Malemba amasonyezanso kuti mtumwi Paulo anayang’ana mwachidwi pofuna kuona kulabadira kwa omvera ake. Panthaŵi ina, mwamuna wina wolemala analipo pamene Paulo anali kulankhula. Machitidwe 14:9, 10 amati: ‘Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang’anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo, anati ndi mawu aakulu, Taimirira.’

Mmene Mungachitire mu Utumiki wa Kumunda. Pamene muli mu utumiki wa kumunda, khalani waubwenzi ndi wosangalala pamene mufikira anthu. Ngati kuli kotheka, funsani mafunso ochititsa munthu kuganiza pofuna kukambirana naye nkhani imene iyenso angachite nayo chidwi. Pochita zimenezi, yesetsani kuyang’anana ndi munthuyo—kapena kumuyang’ana pankhope m’njira yaulemu ndipo mosangalala. Munthu amene maso ake amasonyeza chimwemwe, kumwetulira kwake kumakopa chidwi. Nkhope yoteroyo ingadziŵitse munthu winayo za inu ndipo amakhala womasuka pamene mukulankhula naye.

Poona mmene maso a munthu akuonekera, ngati kuli koyenera, mungadziŵe mmene muyenera kulankhulira naye. Ngati munthuyo wakwiya kapena ngati sakufuna, mutha kuona zimenezo. Ngati sakukumvetsani, mukhoza kuona zimenezo. Ngati akuchita mphwayi, mukhozanso kuzindikira zimenezo. Ngati ali wofunitsitsa, mutha kuonanso zimenezo. Maso ake angakudziŵitseni kuti muyenera kusintha liŵiro, kuti muyenera kum’limbikitsa kulankhulapo, kuti muyenera kusiya kukambiranako, kapenanso kuti mungam’sonyeze mmene timachitira phunziro la Baibulo.

Kaya mukulalikira kwa anthu kapena mukuchititsa phunziro la Baibulo la panyumba, yesetsani kuyang’ana pankhope munthu amene mukulankhula naye. Komabe, musangoti maso dwii pa iye, angachite manyazi. (2 Maf. 8:11) Koma mwachibadwa ndi mwaubwenzi, yang’anani munthuyo pankhope nthaŵi ndi nthaŵi. M’mayiko ambiri, zimenezi zimaonetsa kuti munthuyo muli naye chidwi chenicheni. N’zoona kuti poŵerenga Baibulo kapena chofalitsa china, maso anu amakhala pabuku. Koma pofuna kutsindika mfundo, muyenera kuyang’ana munthuyo pankhope, koma mwachidule chabe. Ngati mum’yang’ana nthaŵi ndi nthaŵi, mudzatha kuona mmene akulabadirira ku zimene mukuŵerenga.

Ngati poyambirira zikukuvutani kuyang’ana omvera chifukwa cha manyazi, musataye mtima. Mwa kuyesayesa, mudzatha kuyang’ana omvera mwachibadwa, ndipo muzitha kulankhula ndi anthu mogwira mtima.

Pokamba Nkhani. Baibulo limatiuza kuti Yesu asanayambe Ulaliki wake wa pa Phiri, “anakweza maso ake kwa ophunzira ake.” (Luka 6:20) Tengerani chitsanzo chake. Pofuna kulankhula pamaso pa gulu, ayang’aneni anthuwo kenako imani pang’ono musanayambe kulankhula. M’madera ambiri zimenezi zingafune kuyang’anana ndi ena mwa omverawo. Kuzengereza pang’ono kumeneku kungakuthandizeni kukhazika mtima pansi. Kungathandizenso omvera kukonzekera maganizo awo kuti agwirizane ndi mzimu umene nkhope yanu yasonyeza. Ndiponso, kuzengerezako kudzalola omvera anu kukhazikitsa pansi mtima ndi maganizo kuti akumvetsereni.

M’kati mwa nkhani yanu, muziyang’ana omvera anu. Musamayang’ane gulu lonse mwachisawawa. Yesetsani kuyang’ana anthuwo mmodzimmodzi. Kwina kulikonse, wokamba nkhani amayembekezeka kuyang’anana ndi wina m’gulumo.

Kuyang’ana omvera anu sikutanthauza kungodutsitsa maso kuchokera mbali ina kufika mbali inayo ayi. Yang’ananani mwaulemu ndi wina m’gulumo, ndipo ngati n’koyenera, nenani sentensi yonse kwa munthuyo. Kenako yang’anani munthu wina ndipo lankhulani sentensi imodzi kapena aŵiri kwa iyenso. Musayang’ane munthu mmodzi kwa nthaŵi yaitali momuchititsa manyazi, ndipo musamangoyang’ana anthu oŵerengeka okhaokhawo m’gulu lonselo. Pitirizani kuyang’ana anthu osiyanasiyana m’gulumo, koma polankhula ndi munthu mmodzi, lankhulanidi ndi munthuyo ndipo onani kuti akulabadira motani musanapite kwa wina.

Autilaini yanu ikhale pasitandi yolankhulirapo, m’manja mwanu, kapena m’Baibulo kotero kuti muzitha kuyang’ana pa autilainiyo mwa kusuntha maso okha. Ngati muchita kuzyolika mutu wonse kuti muyang’ane pa autilaini, kuyang’ana omvera kumasokonekera. Musamayang’ane pa autilaini yanu pafupipafupi kwambiri. Muyang’anepo panthaŵi zoyenerera zokha. Ngati muyang’ana pa autilaini yanu pafupipafupi, mudzalephera kuyang’ana omvera moyendera nawo limodzi. Komanso, ngati muyang’ana pa autilaini yanu pamene mukufika pamfundo yaikulu m’nkhani yanu, simutha kuona kuti omvera alabadira motani, ndipo simungathe kulankhula mwamphamvu kwenikweni.

Mukaponyera munthu mpira, mumayang’ana kuti muone ngati auŵakha. Lingaliro lililonse limene mutchula m’nkhani yanu ndiwo “mpira” umene mwaponyera omvera anu. “Kuuŵakha” kungakhale mwa kulabadira—mwa kugwedeza mutu, kumwetulira, ndi kuyang’ana mwachidwi. Ngati muyang’ana omvera moyendera nawo limodzi, mudzakhala otsimikiza kuti malingaliro anu “akuŵakhidwa.”

Ngati mwapatsidwa mbali yokaŵerenga pamaso pa mpingo, kodi muyenera kuyang’ana omvera pamene mukuŵerenga? Ngati omvera akutsatirani poŵerenga m’mabaibulo awo, ambiri sangadziŵe kaya mukuwayang’ana kapena ayi. Koma kuyang’anabe omvera kungakuthandizeni kuŵerenga mwamphamvu chifukwa mumaona mmene akulabadirira. Ndipo ena m’gulu amene sakuŵerenga Baibulo amene maganizo awo angakhale akuyendayenda, kuyang’anana ndi wolankhula kungawathandize kuika maganizo pa zimene zikuŵerengedwa. Inde, yang’anani omvera mwachidule, ndipo kukhale mwa njira yosadodometsa kuŵerenga kwanu. Pachifukwa chimenecho, ndi bwino kugwira Baibulo lanu m’dzanja ndi kukweza mutu wanu, kuti chibwano chisayandikire kwambiri pachifuŵa.

Nthaŵi zina, akulu amapatsidwa nkhani zoŵerenga pamisonkhano yaikulu. Kukamba nkhani zimenezi kumafuna kuzoloŵera, kukonzekera bwino, ndi kuyeseza kwambiri. N’zoona kuti kukamba nkhani yoŵerenga kumachepetsa mpata woyang’ana omvera. Koma ngati wokambayo wakonzekera bwino, akhozabe kuyang’ana omvera nthaŵi ndi nthaŵi popanda kutaya pamene ali. Ngati achita zimenezo adzathandiza omvera kusunga maganizo awo ndi kupindula kwathunthu ndi malangizo auzimu ofunika omwe akuperekedwawo.

MFUNDO ZOYENERA KUZIKUMBUKIRA

  • Khalani wachibadwa, waubwenzi, ndi wosonyeza chidwi chenicheni kwa omvera anu.

  • Poŵerenga, nkhani ikhale m’dzanja ndipo kwezani chibwano chanu kuti muthe kumasuntha maso anu okha osati mutu wonse.

ZOCHITA: M’kukambirana kwa tsiku ndi tsiku ndi apabanja panu kapena ndi mabwenzi, yesetsani kuwayang’ana pankhope, koma m’njira yolemekeza chikhalidwe cha kumeneko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena