Sonyezani Ena Chidwi mwa Kuwayang’ana Polankhula Nawo
1 Pamene tikulalikira m’malo amene mumapezeka anthu ambiri ndiponso kunyumba ndi nyumba, kawirikawiri timayamba tayang’ana kaye anthu tisanayambe kulankhula nawo. Panthawi yochepayo, tikaona mmene akuonekera pa nkhope pawo, tingadziwe ngati akusangalala nafe kapena sakusangalala nafe ndiponso ngati pali zinthu zowasokoneza maganizo kapena ayi. Anthu amene tikufuna kulankhula nawowo angadziwenso zambiri za ife mwa kutiyang’ana. Mayi wina analankhula za Mboni ina imene inabwera pakhomo pake, kuti: “Chimene ndimakumbukira n’choti ankamwetulira ndipo nkhope yake inkaoneka kuti ali ndi mtendere wamumtima. Zinandichititsa chidwi.” Zimenezi zinapangitsa mzimayiyu kumvetsera uthenga wabwino.
2 Kuyang’ana ena polankhula nawo ndi njira yothandiza kwambiri kuyambitsira ulaliki pamene tikulalikira malo amene mumapezeka anthu ambiri. Mbale wina amayang’ana anthu akamamuyandikira. Akawayang’ana, amamwetulira ndipo kenako amawasonyeza magazini. Chifukwa cha zimenezi, amakambirana bwino kwambiri ndi anthu ochuluka ndiponso amagawira mabuku ambiri.
3 Dziwani Mmene Ena Akumvera: Kuyang’ana anthu kungatithandize kudziwa mmene ena akumvera. Mwachitsanzo, ngati munthu wina sakumvetsa zimene tikulankhula kapena sakugwirizana ndi chinachake chimene talankhula, nthawi zambiri nkhope yake imasonyeza. Ngati munthuyo ali wotanganidwa kapena wayamba kusamvetsera, tingadziwe poona mmene munthuyo akuonekera. Nthawi yomweyo tingasinthe kapena kufupikitsa ulaliki wathu. Kudziwa mmene anthu ena akumvera ndi njira yabwino yowasonyezera chidwi.
4 Kukhala Woona Mtima ndi Wotsimikiza: Pa zikhalidwe zambiri, kuyang’ana munthu m’maso ndi umboni woti munthuwe ukunena zoona. Taonani mmene Yesu anayankhira ophunzira ake atam’funsa kuti: “Angapulumuke ndani?” Baibulo limati: ‘Ndipo Yesu anawayang’ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.’ (Mat. 19:25, 26) Mosakayikira kutsimikiza kwa Yesu, kunapangitsa kuti ophunzirawo akhulupirire mawu ake. Mwa njira yomweyo, kuyang’ana anthu kudzatithandiza kupereka uthenga wa Ufumu kwa anthu moona mtima ndiponso motsimikiza.—2 Akor. 2:17; 1 Ates. 1:5.