Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira April 10
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse woyenererana ndi gawo lanu, sonyezani zitsanzo za zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya April 15 ndi Galamukani! ya April. M’chitsanzo chimodzi, wofalitsa agawirenso buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kwa munthu amene wachita chidwi kwambiri ndi uthenga wa m’Baibulo. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi wathawo.)
Mph. 15: “Mmene Tingapitirizire Kukhala Achangu.”a Phatikizanimo mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2002, tsamba 14, ndime 13.
Mph. 20: “Kodi Mungasinthe Ndandanda Yanu?”b Gwirizanitsani nkhaniyi ndi zochitika m’gawo lanu. Tchulani dongosolo lililonse limene mpingo wakonza lolalikira masana.
Nyimbo Na. 13 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 17
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Tsindikani zimene mpingo wanu wakonza zokhudza nkhani ya onse yapadera. Limbikitsani onse kuti apitirize kugwiritsa ntchito tsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya April 1 kuitanira anthu ku nkhani yapaderayi, kaya ndi anthu amene anabwera ku Chikumbutso, anthu amene amaphunzira nawo Baibulo, kapena anthu ena achidwi. Fotokozani mwachidule nkhani ziwiri kapena zitatu za zimene zinachitika pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda imeneyi poitana anthu kuti adzamvere nkhani ya onse yapadera.
Mph. 15: “Ntchito Yapadera ya Padziko Lonse Yolengeza za Msonkhano Wachigawo Wakuti ‘Chipulumutso Chayandikira.’”c Onetsetsani kuti mwawerenga ndime zonse. Lengezani deti limene ntchito yapaderayi idzayambe mu mpingo wanu.
Mph. 15: “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.”d
Nyimbo Na. 162 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 24
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pasitetimenti. M’mwezi wa May tipitiriza kugawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse woyenererana ndi gawo lanu, sonyezani zitsanzo za zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya May. Zitsanzozo zikatha, fotokozani nkhani zina za m’magaziniwa zimene anthu a m’gawo lanu angasangalale nazo. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi wathawo.)
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2006 wakuti ‘Chipulumutso Chayandikira.’”e Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo. Limbikitsani onse kuti akonzekere mwamsanga.
Nyimbo Na. 191 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 1
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa April. Kambiranani bokosi lakuti “Kodi Mumafunsa Maphunziro Anu za Anthu Ena Amene Angafunenso Kuphunzira?” lomwe lili patsamba 6.
Mph. 15: “Sonyezani Ena Chidwi mwa Kuwayang’ana Polankhula Nawo.”f Chitaninso chitsanzo chachidule cha wofalitsa akuyang’ana munthu amene akulankhula naye pamalo amene pamapezeka anthu ambiri. Wofalitsayo ayambitse nkhani, kenako n’kumulalikira.
Mph. 20: Mphatso Zachikondi Zotipindulitsa. Ikambidwe ndi mkulu. Werengani ndi kukambirana kalata ya pa January 3, 2006, yochokera ku ofesi ya nthambi kupita ku mipingo yonse yolongosola za njira zimene tingapindulire ndi ntchito ya Komiti Yolankhulana ndi Achipatala (HLC) ndiponso Gulu Lozonda Odwala (PVG).
Nyimbo Na. 82 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
e Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
f Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.