Mmene Tingapitirizire Kukhala Achangu
1 Utumiki wachangu umene Apolo ankachita ungatikumbutse makamaka za Akristu anzathu masiku ano amene amalalikira mwachangu kwambiri. (Mac. 18:24-28) Komabe, tonsefe, tikulimbikitsidwa kuti: “Musakhale aulesi m’machitidwe anu; khalani achangu mumzimu.” (Aroma 12:11) Kodi chimene chingatithandize kuyamba ndi kupitiriza kukhala achangu mu utumiki wachikristu n’chiyani?
2 Kukhala Achangu Chifukwa cha Zomwe Tikuphunzira: Yesu ataonekera kwa awiri mwa ophunzira ake ‘n’kuwatanthauzira iwo m’malembo onse zinthu za Iye yekha,’ ophunzirawo anati: “Mtima wathu sunali wotentha m’kati mwathu nanga mmene analankhula nafe m’njira?” (Luka 24:27, 32) Mofanana ndi zimenezo, kodi ifenso mitima yathu sitentha ndi chisangalalo pamene tamvetsa Mawu a Mulungu? Zoonadi, timakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zomwe tikuphunzira. Lemba la Aroma 10:17 limati: “Munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene akumva.” (Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Tikamakhulupirira malonjezo a Yehova m’mitima mwathu, sitingasiye kulankhula za zinthu zimene taphunzira!—Sal. 145:7; Mac. 4:20.
3 Kuti tizimukonda Mulungu kwambiri ndiponso kuti tipitirizebe kukhala achangu pamene tikum’tumikira, sitingadalire chabe zinthu zimene tinaphunzira kale. Tiyenera kupitirizabe kumvetsetsa choonadi ndi kukonda kwambiri Yehova. Tikapanda kutero, pang’ono ndi pang’ono tikhoza kuyamba kutumikira Yehova mwamwambo chabe. (Chiv. 2:4) Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti ‘timke tiwonjezerawonjezera nzeru zathu za kudziwa Mulungu.’—Akol. 1:9, 10, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono.
4 Mmene Timaphunzirira: Motero, tingachite bwino kuonanso bwinobwino mmene timaphunzirira. Mwachitsanzo, tingathe kulemba mizere kunsi kwa mayankho a m’nkhani yophunziridwa ya mu Nsanja ya Olonda, n’kupereka ndemanga zolondola. Koma kodi timawerenga malemba a m’nkhaniyo omwe mawu ake mulibe ndi kuona mmene tingawagwiritsire ntchito m’moyo wathu? Powerenga Baibulo mlungu uliwonse, kodi timachita khama kufufuza zowonjezereka ngati tingathe kutero, ndi kusinkhasinkha pa maphunziro amene amapezeka tikamawerenga Baibulowo? (Sal. 77:11, 12; Miy. 2:1-5) Tingapindule kwambiri ngati tisinkhasinkha ndi kuganizira kwambiri Mawu a Mulungu. (1 Tim. 4:15, 16) Phunziro lopindulitsa lotere lingalimbitse mitima yathu ndi kutipatsa mphamvu kuti tikhale “achangu pa ntchito zokoma.”—Tito 2:14.