Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/09 tsamba 2
  • “Yakani ndi Mzimu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Yakani ndi Mzimu”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Tiyeni Tipitirize Kukhala Achangu Muutumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Mutsanzira Kudzipereka kwa Yehova ndi Yesu pa Nyengo ya Chikumbutso Ikubwerayi?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Lalikani Uthenga Wabwino Mwachangu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Ndinu “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 11/09 tsamba 2

“Yakani ndi Mzimu”

1. Kodi tikamalalikira tiyenera kusonyeza kuti ndife anthu otani?

1 Palibe mbali ya utumiki wathu wachikhristu imene iyenera kukhala yosapita patsogolo. M’malomwake, tikulimbikitsidwa ‘kuyaka ndi mzimu’ ndiponso ‘kutumikira Yehova monga akapolo.’ (Aroma 12:11) Komabe, pali zinthu zambiri zimene zingachititse kuti changu chathu pa utumiki chichepe. Kodi tingatani kuti ‘tikolezere ngati moto’ changu chathu ndiponso kuti tizisangalala kwambiri ndi utumiki wathu wa Ufumu?—2 Tim. 1:6, 7.

2. Kodi kuchita phunziro la Baibulo laumwini n’kogwirizana bwanji ndi kukhala achangu mu utumiki?

2 Phunziro la Baibulo Laumwini: Mlaliki wa Ufumu wolalikira mogwira mtima ndi amene amakonda malamulo a Mulungu ndipo choonadi chimene chimapezeka m’malamulowo chimamusangalatsa kwambiri. (Sal. 119:97) Tikapeza mfundo za choonadi za m’Baibulo pa phunziro laumwini, zimatilimbikitsa kuti tiwonjezere changu chathu. Kukonda Mulungu amene amapereka mfundo za choonadi zimenezi ndiponso kufunitsitsa kuuza ena uthenga wabwino kumatilimbikitsa kutamanda Mulungu ndi kulengeza poyera dzina lake. (Aheb. 13:15) Zoonadi, tikamalengeza uthenga wabwino mwakhama timasonyeza kuti timadziwadi kufunika kwake.

3. Kodi mzimu wa Mulungu ungatithandize bwanji pa utumiki wathu?

3 Muzipempha Mzimu wa Mulungu: Sitingathe kuchita utumiki mogwira mtima podalira mphamvu zathu zokha. Munthu amachita changu chenicheni mu utumiki ngati mzimu wa Mulungu ukugwira bwino ntchito m’moyo wake. (1 Pet. 4:11) Kuyandikira Mulungu yemwe amapereka ‘mphamvu zazikulu’ kudzatipezetsa mphamvu zauzimu zotithandiza kulalikira molimba mtima. (Yes. 40:26, 29-31) Mtumwi Paulo atakumana ndi mavuto pa utumiki wake, ‘analandira thandizo kuchokera kwa Mulungu.’ (Mac. 26:21, 22) Mzimu wa Yehova ndi wamphamvu ndipo ungatithandize kuti tizisangalala mu utumiki wathu, choncho tiyenera kumapempha Mulungu kuti atipatse mzimuwu.—Luka 11:9-13.

4. Kodi zinthu zabwino zimene zingachitike chifukwa chokhala achangu ndi zotani, komano tiyenera kusamala kuti tisachite chiyani?

4 Tikamachita changu kwambiri polalikira za Ufumu, nthawi zambiri timalimbikitsa Akhristu anzathu kuti nawonso akhale achangu. (2 Akor. 9:2) N’zosakayikitsa kuti anthu a m’gawo lathu angamvetsere uthenga umene tikuwalalikira mosangalala ndiponso motsimikizira. Komabe, nthawi zonse changu chathu chiyenera kuyendera limodzi ndi kukhala wosamala komanso kukhala wofatsa. (Tito 3:2) Nthawi zonse tiyenera kulemekeza mwininyumba ndiponso ufulu wake wosankha.

5. Kodi tiyenera kutsatira malangizo ouziridwa ati?

5 Monga olengeza Ufumu, tiyeni nthawi zonse ‘tiziyaka ndi mzimu.’ Tiyeni tiwonjezere changu chathu pomachita phunziro la Baibulo laumwini ndi kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima, ndipo iye angatipatse mzimu woyera wamphamvu. Tikamachita zimenezi, tingathe kuchita utumiki wathu mwachangu tili “ndi mzimu woyera ndi chitsimikizo champhamvu.”—1 Ates. 1:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena