Kodi Mutsanzira Kudzipereka kwa Yehova ndi Yesu pa Nyengo ya Chikumbutso Ikubwerayi?
1. Kodi abale ndi alongo amayesetsa kuchita chiyani pa nthawi ya Chikumbutso?
1 Yehova amakwaniritsa cholinga chake modzipereka kwambiri. Mwachitsanzo, pofotokoza mmene adzabweretsere madalitso mu Ufumu wake, lemba la Yesaya 9:7 limati: “Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.” Yesunso anasonyeza kuti anali wodzipereka kwambiri pamene ankachita utumiki wake padziko lapansi. (Yoh. 2:13-17; 4:34) Chaka chilichonse ikafika nyengo ya Chikumbutso, abale ndi alongo ambiri padziko lonse amatsanzira kudzipereka kwa Yehova ndi Yesu. Amachita zimenezi poyesetsa kuchita zambiri potumikira Yehova. Kodi nanunso mudzasonyeza mtima wodzipereka umenewu?
2. Kodi mtima wodzipereka udzatithandiza kuchita chiyani kuyambira pa 7 March?
2 Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso: Chaka chino, tidzayamba kuitanira anthu ku mwambowu, Loweruka pa 7 March. Yambani kukonzekera panopa kuti mudzagwire nawo ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso modzipereka. Mipingo idzasangalala kwambiri kugwira ntchitoyi, m’gawo lawo lonse. Yesetsani kudzaitana amene mumagwira nawo ntchito, achibale anu komanso anzanu akusukulu powapatsa kapepala kapena powauza kuti aone pa webusaiti yathu ya jw.org/ny.
3. Kodi tingatani kuti tidzachite zambiri m’mwezi wa March ndi April?
3 Upainiya Wothandiza: Mtima wodzipereka udzatithandizanso kuyesetsa kuti tichite zambiri potumikira Mulungu. Tikukhulupirira kuti ambiri adzachita upainiya wothandiza m’mwezi wa March ndi April chifukwa m’miyezi imeneyi apainiya othandiza angathe kudzapereka maola 30. Pa kulambira kwa pabanja kapena pophunzira pa nokha, ganizirani zimene mungachite kuti mudzakwanitse kuchita upainiya wothandiza. (Miy. 15:22) Anthu ena akaona kuti mukugwira ntchitoyi mwakhama, nawonso angachite chimodzimodzi. Mukasintha zina ndi zina n’cholinga choti muthe kuchita zambiri, ndiye kuti mukutsanzira Yesu.—Maliko 6:31-34.
4. Tikadzatsanzira Yehova ndi Yesu pa nthawi ya Chikumbutso, kodi zotsatira zake zidzakhala zotani?
4 Tikadzatsanzira Yehova ndi Yesu pa nthawi ya Chikumbutso, zotsatira zake zidzakhala zabwino kwambiri. Choyamba, anthu ambiri m’gawo lathu adzamva uthenga wa m’Baibulo. Chachiwiri, tidzasangalala kwambiri chifukwa chodziwa kuti tatumikira Yehova komanso tathandiza anthu ena. (Mac. 20:35) Ndipo chofunika kwambiri n’choti tidzasangalatsa Mulungu ndi Mwana wake.