Kukonzekera Nkhani za Onse
MLUNGU uliwonse, mipingo yambiri ya Mboni za Yehova imakhala ndi nkhani ya onse pa mutu wochokera m’Malemba. Ngati ndinu mkulu kapena mtumiki wotumikira, kodi mumaonetsa umboni wakuti ndinu wokamba nkhani waluso, mphunzitsi? Ngati mumatero, angakupempheni kuti mukambe nkhani ya onse. Sukulu ya Utumiki wa Mulungu yathandiza zikwizikwi za abale kuti ayenerere utumiki umenewu. Mukapatsidwa nkhani ya onse, kodi muyenera kuyambira pati kukonzekera?
Iŵerengeni ndi Kuimvetsa Bwino Autilainiyo
Musanayambe kufufuza kulikonse, ŵerengani autilainiyo ndipo musinkhesinkhe kufikira mutamvetsa mfundo yake yaikulu. Sungani m’maganizo mutu wake. Kodi n’chiyani chimene mukayenera kuphunzitsa omvera anu? Kodi cholinga chanu n’chiyani?
Mvetsetsani mitu ya m’katiyo. Zimenezo ndizo mfundo zazikulu, choncho zipendeni mofatsa. Kodi iliyonse imagwirizana motani ndi mutu waukulu? Pansi pa mfundo yaikulu iliyonse, pandandalikidwa mfundo zina zing’onozing’ono. Malingaliro ochirikiza mfundo zing’onozing’ono zimenezi andandalikidwa pansi pake. Onani mmene chigawo chilichonse cha autilainiyo chikutulukira m’chigawo chapamwamba ndi mmene chikuloŵera m’chigawo chotsatira, ndi mmenenso chikuthandizira kukwaniritsa cholinga cha nkhaniyo. Mutazindikira bwino mutu wa nkhani, cholinga cha nkhaniyo, ndi mmene mfundo zazikulu zikukwaniritsira cholingacho, ndiye kuti mwakonzeka kuyamba kuikonza nkhani yanu.
Choyamba, mungachite bwino kuiona nkhani yanu ngati nkhani zinayi kapena zisanu zifupizifupi, iliyonse yokhala ndi mutu wake. Zikonzekereni payokhapayokha.
Autilainiyo yangokhala chipangizo chokonzekerera. Si manotsi akuti muzikambirapo nkhani yanu ayi. Yangokhala ngati mafupa okhaokha, titero kukamba kwake. Ndiye mufunikira kuikamo mnofu, mtima, ndi mpweya kuti ikhale yamoyo.
Kugwiritsa Ntchito Malemba
Yesu Kristu ndi ophunzira ake anali kuphunzitsa kuchokera m’Malemba. (Luka 4:16-21; 24:27; Mac. 17:2, 3) Mukhoza kutero inunso. Malemba ayenera kukhala maziko a nkhani yanu. M’malo mongofotokoza mawu a pa autilaini yoperekedwayo ndi kusonyeza mmene amagwirira ntchito, onani mmene Malemba amachirikizira mawuwo, ndiyeno phunzitsani kuchokera pa Malembawo.
Pokonzekera nkhani yanu, ŵerengani ndi kupenda lemba lililonse losagwidwa mawu pa autilainipo. Onetsetsani nkhani yake ya lembalo. Malemba ena amangopereka mfundo zongopereka chithunzi chokwanira. Si onse amene muyenera kuŵerenga kapena kulankhulapo pokamba nkhani yanu. Sankhani okhawo amene angathandize kwambiri omvera anu. Ngati mukonzekera bwino lomwe malemba osagwidwa mawu a pa autilaini, simungafunikire kwenikweni kutenganso kwina Malemba ena owonjezerapo.
Kuti nkhani yanu ikhale yogwira mtima, sizidalira kwenikweni kuchuluka kwa malemba oŵerengedwa, koma luso la kuphunzitsa. Potchula lemba loti muŵerenge, nenani chifukwa choliŵerengera. Fotokozani mmene tingaligwiritsire ntchito. Mutaŵerenga lemba, Baibulo lanu likhale chitsegukire pamene mukufotokoza lembalo. Mwachidziŵikire, omvera anu adzachitanso chimodzimodzi. Kodi mungalimbikitse motani chidwi cha omvera anu ndi kuwathandiza kuti apindule kwathunthu ndi Mawu a Mulungu? (Neh. 8:8, 12) Mungatero mwa kuwafotokozera lemba, kuperekapo chitsanzo, ndi kuwaonetsa mmene tingaligwiritsire ntchito.
Kufotokozera. Pokonzekera kufotokozera lemba lofunika, dzifunseni kuti: ‘Kodi limatanthauzanji? N’chifukwa chiyani ndikuligwiritsa ntchito m’nkhani yangayi? Kodi omverawo angakhale akudzifunsa zotani pa vesiyi?’ Mungafunikire kupenda mavesi ozungulira, zochitika za m’lembalo, malo a zochitikazo, mphamvu ya mawuwo, ndi cholinga cha wolemba wake. Zimenezi zimalira kufufuza. Mudzapeza mfundo zothandiza zankhaninkhani m’mabuku ofalitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Musayese kufotokoza zonse zokhudza vesiyo, koma fotokozani chimene mwapemphera omvera anu kuti aiŵerenge, malinga ndi mfundo imene mukukambirana.
Kuperekapo Chitsanzo. Cholinga cha zitsanzo ndicho kuthandiza omvera anu kumvetsa lingaliro lozamirapo kapena kuwathandiza kukumbukira mfundo ina imene mwaifotokoza. Zitsanzo zimathandiza anthu kumvetsa zimene mwawauza ndi kuzigwirizanitsa ndi zimene akuzidziŵa kale. Umu ndi mmene Yesu anachitira pa Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri. Mawu akuti “mbalame za kumwamba,” “maluŵa akuthengo,” “chipata chopapatiza,” ‘nyumba yomangidwa pathanthwe,’ limodzi ndi mawu ena ambirimbiri anapangitsa kuphunzitsa kwake kukhala kotsindika, komvekera bwino, ndi kosaiŵalika.—Mat., macha. 5–7.
Kuonetsa Mmene Tingawagwiritsire Ntchito. Kufotokozera lemba ndi kuperekapo chitsanzo kumaphunzitsa zambiri, koma kugwiritsa ntchito zimene taphunzira n’kumene kumabala zipatso. Zoona, ndi udindo wa omvera anu kuchitapo kanthu pa uthenga wa m’Baibulo umene akumvera, komabe mukhoza kuwathandiza kuzindikira zimene ayenera kuchita. Mutatsimikiza kuti omvera anu amvetsa vesi imene mwafotokozayo ndipo aona mmene ikugwirizanira ndi mfundo yanu, aonetseni mmene imakhudzira chikhulupiriro chathu ndi khalidwe lathu. Unikani mapindu ake a kusiya maganizo kapena khalidwe lolakwika losemphana ndi choonadi chimene mukufotokoza.
Pamene mukulingalira za mmene mungagwiritsire ntchito malembawo, kumbukirani kuti omvera anuwo anakula mosiyanasiyana ndipo mikhalidwe ya moyo wawo n’njosiyanasiyananso. Mwa iwo mungakhale atsopano, achinyamata, okalamba, ndi aja omwe akulimbana ndi mavuto osiyanasiyana pamoyo wawo. Nkhani yanu ikhale yothandiza ndi yonena zenizeni. Peŵani kupereka uphungu womveka ngati muli ndi anthu oŵerengeka chabe m’maganizo.
Zimene Wokamba Nkhani Ayenera Kusankha
Zinthu zina zokhudza nkhani yanu anakusankhirani kale. Mfundo zazikulu n’zosonyezedwa bwino lomwe, ndipo nthaŵi imene muyenera kuwonongera pa mutu waung’ono uliwonse yasonyezedwanso bwinobwino. Koma zinthu zina muyenera kusankha nokha. Mungasankhe kuwonongera nthaŵi yochulukirapo pa mutu waung’ono wina kusiyana ndi mitu ina. Musaganize kuti muyenera kumveketsa bwino mfundo ya mutu waung’ono uliwonse mofanana. Zimenezo zingakupangitseni kudutsa mofulumira pa mfundo zanu ndi kuwasiya m’malere omvera anu. Kodi mungadziŵe bwanji mutu waung’ono umene mungafotokozepo mfundo zambiri ndi umene mungafotokoze mwachidule, kapena mongodutsa? Dzifunseni kuti: ‘Ndi mfundo ziti zimene zingandithandize kumveketsa lingaliro lalikulu la nkhaniyi? Nanga zimene zikuoneka kuti zingapindulitse kwambiri omvera anga ndi ziti? Kodi kuchotsapo lemba lina losagwidwa mawu ndi mfundo zake kungafooketse tsatanetsatane wa umboni umene ukuperekedwa?’
Yesetsani kwambiri kusaloŵetsapo nkhambakamwa kapena maganizo anuanu. Ngakhaletu Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anapeŵa kulankhula za ‘iye yekha.’ (Yoh. 14:10) Dziŵani kuti chifukwa chimene anthu amafikira pamisonkhano ya Mboni za Yehova n’chakuti adzamve mfundo za m’Baibulo. Ngati inuyo mumadziŵika ngati wodziŵa kukamba bwino nkhani, mwachidziŵikire n’chifukwa chakuti nkhani zanu sizikopera maganizo a anthu kwa inu mwini, koma ku Mawu a Mulungu. Pachifukwa chimenechi, anthu amazikonda nkhani zanu.—Afil. 1:10, 11.
Popeza kuti mu autilaini ya mafupa okhaokhayo mwaikamo mnofu wa malongosoledwe a Malemba, tsopano mufunikira kuyeseza nkhani yanu. N’kothandiza kuchita zimenezo motulutsa mawu. Koma chofunikira ndicho kutsimikiza kuti mfundo zonse mwazisunga bwino lomwe m’maganizo mwanu. Mufunikira kukamba nkhani yanu mwachidaliro, mwaumoyo, ndi kufotokoza choonadi mosangalala. Musanakambe nkhani yanu, dzifunseni kuti: ‘Kodi cholinga changa n’chiyani? Kodi mfundo zazikulu zikuonekera? Kodi ndayaladi Malemba kukhala maziko a nkhani yanga? Kodi mfundo yaikulu iliyonse imatsogolera moonekera bwino ku inzake? Kodi nkhaniyi idzathandizadi anthu kuŵirikiza chiyamikiro chawo kwa Yehova ndi zogaŵira zake? Kodi mawu omaliza akukhudzana mwachindunji ndi mutu wake. Kodi akusonyeza omvera zimene ayenera kuchita, ndi kuwalimbikitsa kukachita zimenezo?’ Ngati mungayankhe kuti inde pa mafunso ameneŵa, ndiye kuti mwakonzeka ‘kunena bwino zimene mudziŵa,’ kuti mupindulitse mpingo ndi kuti Yehova atamandike!—Miy. 15:2.