PHUNZIRO 7
Kutsindika Malingaliro Ofunika Kwambiri
WOŴERENGA waluso saona masentensi okha, ngakhalenso ndime zokha mmene muli masentensiwo. Akamaŵerenga, amaganizira malingaliro ofunika kwambiri m’nkhani yonseyo. Zimenezi zimam’thandiza kudziŵa mofunikira kutsindika.
Ngati njira imeneyi siitsatiridwa, mfundo zazikulu sizingaonekere m’nkhaniyo. Pamene nkhaniyo itha, kungakhale kovuta kukumbukira mfundo yapadera iliyonse.
Kutsindika bwino malingaliro ofunika kwambiri kungathandize kuti nkhani ya m’Baibulo imveke bwino. Kutsindika koteroko kungachititse kaŵerengedwe ka ndime paphunziro la Baibulo la panyumba kapena pamsonkhano wa mpingo kukhala katanthauzo kwambiri. Ndipo kumakhala kofunika kwambiri pokamba nkhani yoŵerenga, muja zimakhalira pamisonkhano yathu yaikulu.
Mmene Mungatsindikire. M’sukulu, mungapatsidwe mbali yoŵerenga Baibulo. Kodi mukafunikira kutsindika chiyani? Ngati pali lingaliro lofunika kwambiri limene lili maziko a nkhani imene mukaŵerenga, ndi bwino kulitsindika lingalirolo kuti lionekere.
Kaya mbali imene mwapatsidwa kukaŵerenga ndi ndakatulo kapena nkhani yokamba wekha, mwambi kapena nkhani yosimba zochitika, kuti omvera anu akapindule, muyenera kukaŵerenga bwino. (2 Tim. 3:16, 17) Kuti mukachite zimenezo muyenera kulingalira za mbali imene mukaŵerengeyo komanso omvera anu.
Ngati mukaŵerenga kuchokera m’buku paphunziro la Baibulo kapena pamsonkhano wa mpingo, kodi ndi malingaliro ofunika kwambiri ati amene mukayenera kuwatsindika? Mayankho a mafunso a m’nkhani yophunzirayo ndiwo malingaliro ofunika kwambiri. Tsindikaninso malingaliro okhudzana ndi mitu yaing’ono yolembedwa m’malembo aakulu.
Si bwino kukhala ndi chizoloŵezi cholemba mawu onse a nkhani yanu ndi kukaikamba ngati nkhani yoŵerenga mumpingo. Komabe nthaŵi zina, nkhani zoŵerenga zimaperekedwa pamisonkhano yaikulu kotero kuti mfundo zake ziperekedwe mofanana kulikonse pamisonkhanoyo. Kuti wokamba nkhaniyo atsindike malingaliro ofunika kwambiri m’nkhaniyo, ayenera kuti choyamba apende nkhaniyo mosamala. Kodi mfundo zazikulu ndi ziti? Ayenera kuzizindikira mfundozo. Sikuti mukapeza malingaliro okusangalatsani ndiye kuti mwapeza mfundo zazikulu ayi. Malingaliro ofunika kwambiri ndi mfundo zimene zimamanga nkhani yonseyo. Nthaŵi zina ndemanga yachidule yopereka lingaliro lofunika kwambiri m’nkhani yoŵerenga ingakhale kalambulabwalo wa nkhani yosimba zochitika zakutizakuti kapena mndandanda wa mfundo zogomeka nkhani. Kaŵirikaŵiri, tikapereka umboni wotsimikizira nkhani, timaphera mphongo ndi ndemanga yamphamvu. Wokamba nkhani akazindikira mfundo zofunika zimenezo, ayenera kuzilemba mzera kunsi kwake m’nkhani yake yoŵerengayo. Zimenezi zimakhala zochepa chabe, mwina zosapitirira zinayi kapena zisanu. Kenako ayenera kuyeseza kuŵerenga m’njira yothandiza omvera kuona mfundozo mosavuta. Zimenezi ndizo mfundo zazikulu za nkhaniyo. Ngati nkhaniyo ikambidwa ndi kutsindika koyenerera, malingaliro ofunika kwambiri ameneŵa adzakumbukika kwa nthaŵi yaitali. Cholinga cha wokamba nkhani chizikhala chimenecho.
Zilipo njira zosiyanasiyana zimene wokamba nkhani angatsindikire mawu pothandiza omvera kuzindikira mfundo zazikulu. Angagwiritse ntchito mawu amphamvu, kusintha liŵiro, kuonetsa kukhudzika mtima, kapena zizindikiro za manja zoyenerera, ndi zina zambiri.