Kodi Mumafunsa Maphunziro Anu za Anthu Ena Amene Angafunenso Kuphunzira?
Ngati muli ndi phunziro la Baibulo panopa, bwanji osam’fusa wophunzirayo ngati pali anzake, achibale ake, kapena anthu ena alionse odziwana naye amene angakonde kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa? Nthawi zambiri wophunzirayo amatha kupereka maina angapo. Wophunzirayo akavomereza, mungathe kutchula dzina lake mukapita kwa anthu amenewo kukawapempha kuti muziphunzira nawo Baibulo. Munganene kuti, “[Wakutiwakuti] akusangalala kuphunzira Baibulo, ndipo akuganiza kuti nanunso mungakonde kuphunzira Baibulo kwaulere.” Kenako, pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, sonyezani mwachidule mmene timachitira phunziro.
Ngati muli ndi wophunzira amene akupita patsogolo, mungathe kumulimbikitsa kuti azifotokoza za phunzirolo kwa anzake ndi achibale ake amene angakhale ndi chidwi. Angathe kuwauza kuti azikhala nawo pa phunziro lake. Kapena ngati ndi zovuta kutero, angakonze zoti inuyo mukumane nawo ndi kuwasonyeza mmene timachitira phunziro. Kuchita zimenezi kungalimbikitse wophunzirayo kuyamba kuuza ena zinthu za m’Baibulo zimene iye waphunzira.
Nawonso anthu omwe mumawapitira nthawi ndi nthawi pamaulendo obwereza angakupatseni maina a anthu amene angafune kuphunzira Baibulo, ngakhale kuti iwowo sanavomere kuyamba phunziro la Baibulo la nthawi zonse. Mukawagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, mungathe kungowafunsa kuti, “Kodi mukudziwako wina aliyense amene angakonde kulandira buku limeneli?”
Popeza tikukhala mu nthawi yofunika kuchita zinthu mwachangu, tikufunika kuchita chilichonse chotheka kuti tithandize anthu kumva ndi kulabadira uthenga wabwino. Kodi mumafunsa maphunziro anu za anthu ena amene angafunenso kuphunzira?