Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/06 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 4/06 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu a chidwi, kuphatikizanso amene amapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo, yesetsani kuwagawira buku la latsopano la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Cholinga chathu chikhale kuyambitsa phunziro la Baibulo. June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, agawireni buku la Chimwemwe cha Banja. July: Mungathe kugwiritsa ntchito kalikonse ka timabuku ta masamba 32 totsatirati: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dikirani!, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha!

◼ Kuyambira mu April, tizitumiza mabaji a msonkhano wachigawo wa 2006 tikamatumiza mabuku. Simukufunika kuitanitsa mabajiwa pokhapokha ngati mpingo wanu uli ndi kagulu kolankhula chinenero chakunja. Ngati mpingo ukufuna mabaji ena, itanitsani pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Muitanitse mapulasitiki oikamo baji a aliyense mu mpingo amene alibe, kapena amene pulasitiki yake ya m’mbuyomu inatayika. Ngati tisamala mapulasitiki oikamo bajiwa, tingakhale nawo kwa zaka zambiri.

◼ Alembi a mipingo azisunga mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Angaitanitse mafomuwa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Muzikhala ndi mafomu okwanira chaka chimodzi. Musanatumize ku nthambi mafomu a anthu amene afunsira upainiya wokhazikika, onetsetsani kuti mafunso onse ayankhidwa.

◼ Ofesi ya nthambi imayenera kukhala ndi maadiresi ndi manambala a telefoni amene akugwira ntchito panopo a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse. Zimenezi zikangosintha nthawi ina iliyonse, Komiti ya Utumiki ya Mpingo izilemba ndi kusaina fomu ya Kusintha Adiresi ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi. Zimenezi zikuphatikizapo kusintha kulikonse kwa manambala a telefoni.

◼ Mipingo iyambe kufunsira mabaundi voliyumu a Watchtower ndi Awake! a 2005. Mabaundi voliyumuwa adzakhalapo m’Chingelezi. Mabaundi voliyumuwa azidzalembedwa kuti zoyembekezeredwa pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo kufikira pamene mabaundi voliyumu adzakhalepo ndi kutumizidwa. Mabaundi voliyumu ndi zinthu zofunsira mwapadera.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena