Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira June 12
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya June 15 ndi Galamukani! ya June. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani wofalitsa akugawira magazini mwamwayi. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.20: “Utumiki Wathu Ndi Ntchito Imene Imasonyeza Chifundo.”a Ngati pali nthawi, pemphani omvera kuti aikepo ndemanga pa malemba opezeka m’nkhaniyi.
Mph.15: Khulupirirani “Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru.” Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, chaputala 3.
Nyimbo Na. 47 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 19
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph.20: Mawu a pa Nthawi Yake Kodi Sali Abwino? Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2006, tsamba 16 mpaka 19. M’mawu anu oyamba, tchulani mfundo zinayi zonena za ubwino woyamikira ena, zofotokozedwa pa kamutu kakuti “Ubwino Wake.” Ndiyeno pemphani omvera kuyankha mafunso otsatirawa: Kodi ndani amene ali woyenera kutamandidwa koposa? Kodi n’chifukwa chiyani olambira anzathu ali oyenerera kuwayamikira moona mtima? Kodi ndi mipata iti yoyamikirira ena imene tili nayo mumpingo? Kodi n’chifukwa chiyani kuyamikira anthu apabanja pathu kuli kopindulitsa, ndipo tingachite motani zimenezi? Kodi mwalimbikitsidwapo motani chifukwa choyamikiridwa?
Mph.15: “Sonyezani Ena Chidwi mwa Kuwayamikira.”b Phatikizanipo chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akumumvetsera mwininyumba mosamala, akumuyamikira moona mtima, kenako akukambirana naye nkhani yokhudzana ndi zimene anamuyamikira nazozo mwa kuwerenga naye lemba loyenerera.
Nyimbo Na. 96 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 26
Mph.15: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka amene alembedwa pa sitetimenti. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July. Pamapeto pa chitsanzo chilichonse, wofalitsa afunse funso lochititsa chidwi loti lidzayankhidwe pa ulendo wotsatira pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.15: Kutumikira Mumpingo wa Chinenero China. Nkhani yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2006, tsamba 17 mpaka 20. Phatikizanipo ndemanga za m’buku la Gulu, tsamba 112, ndime 2. Fotokozani mmene mpingo wanu ungagwiritsire ntchito mfundo za m’nkhaniyi. Mungafunsenso mwachidule munthu mmodzi kapena awiri amene akufuna kuwonjezera utumiki wawo mwa kuphunzira chinenero china.
Mph.15: Kulalikira Uthenga Wabwino M’mwezi wa July. Kodi anthu ambiri m’gawo lanu amachita chidwi ndi nkhani zotani? Funsani mwachidule wofalitsa mmodzi kapena awiri amene agwiritsa ntchito bwino kwambiri buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo mwina anayambitsa phunziro la Baibulo. Chitani chitsanzo cha wofalitsa ali mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba akugawira bukuli pogwiritsa ntchito ulaliki umene uli wogwira mtima m’gawo lanu.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, tsa. 8, ndime 5.
Nyimbo Na. 208 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 3
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka lipoti lawo la utumiki wa kumunda la mwezi wa June ngati sanapereke.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: “Mmene Mungakwaniritsire Zolinga Zanu Zauzimu.”c Pemphani achinyamata a mumpingo wanu kuti afotokoze zolinga zawo zauzimu ndi zimene akuchita kuti akwaniritse zolingazo. Mungakonzeretu pasadakhale kuti wachinyamata mmodzi kapena awiri adzapereke ndemanga zawo.
Nyimbo Na. 30 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.