Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/06 tsamba 4
  • Mmene Mungakwaniritsire Zolinga Zanu Zauzimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungakwaniritsire Zolinga Zanu Zauzimu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Achinyamata, Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Ndingakwanitse Bwanji Zolinga Zanga?
    Galamukani!—2010
  • Achinyamata—Kodi Zolinga Zanu Zauzimu Nzotani?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 6/06 tsamba 4

Mmene Mungakwaniritsire Zolinga Zanu Zauzimu

1. Kodi achinyamata ambiri ali ndi zolinga zauzimu zotani?

1 N’zosakayikitsa kuti kukonda Yehova komanso mawu a Yesu opita kwa Akristu onse akuti “muthange mwafuna Ufumu,” ndizo zimatsogolera zosankha zanu Akristu achinyamatanu. (Mat. 6:33) Mungathe kukhala ndi cholinga chofutukula utumiki wanu potumikira monga mpainiya kapena kukatumikira kumadera kumene olengeza Ufumu ndi ochepa. Enanu mungakonde kudzipereka kukatumikira pa Beteli, kapena kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Zimenezi ndi zolinga zabwino ndiponso zotamandika kwambiri!

2. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanu zauzimu?

2 Chinthu chimene chingakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanu zauzimu ndicho kulemba zolinga zanuzo. Nsanja ya Olonda ya July 15, 2004, inati: ‘Zinthu zimene mumangoziganizira zimatsatirika bwino mukazilongosola m’mawu omveka bwino. Motero mungachite bwino kulemba zolinga zanu ndiponso mmene mukufuna kuzikwaniritsira.’ Komanso kukhala ndi zolinga zoti mukwaniritse, musanakwaniritse zolinga zanu zazikulu, kungakuthandizeni kudziwa ngati mukuchita bwino kapena ayi ndipo zimathandiza kuti musasokonekere maganizo pa cholinga chanu chachikulucho.

3. Tchulani zolinga zotenga nthawi yochepa zomwe zingathandize munthu kuti ayenerere kubatizidwa.

3 Zolinga Zotenga Nthawi Yochepa: Ngati simunabatizidwe panopo, ganizirani za zimene mukufunikira kuchita kuti mukwaniritse cholinga chimenechi. Mungafunikire kumvetsa bwino ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Ngati ndi choncho, phunzirani mozama buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndipo werengani malemba onse osonyezedwa m’bukuli. (1 Tim. 4:15) Khalaninso ndi cholinga chowerenga Baibulo lonse kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso, monga mmene abale ndi alongo a pa Beteli komanso ophunzira a sukulu ya Gileadi amachitira. Mukatha kuchita zimenezi, khalani ndi ndandanda yokhazikika yowerengera Baibulo tsiku ndi tsiku. (Sal. 1:2, 3) Tangoganizirani mmene kuchita zimenezi kungakuthandizireni kukula mwauzimu! Powerenga ndi kuphunzira Baibulo, yambani ndiponso malizani ndi pemphero, ndipo yesetsani kugwiritsa ntchito zimene mukuphunzirazo.—Yak. 1:25.

4. Kodi ndi zolinga ziti zimene Mkristu angapange asanakwaniritse zolinga zokatumikira pa Beteli kapena kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki?

4 Ngati ndinu wobatizidwa kale, kodi n’zolinga zina zotani zimene mungafune kukwaniritsa? Kodi mukufuna kukulitsa luso lanu lolalikira? Mwachitsanzo, kodi mungakonde kukhala ndi cholinga chakuti muzigwiritsa ntchito mwaluso Mawu a Mulungu mu utumiki wa kumunda? (2 Tim. 2:15) Kodi mungafutukule motani utumiki wanu? Khalani ndi zolinga zoyenererana ndi msinkhu komanso mkhalidwe wanu, zoti zikuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanu zazikulu.

5. Kodi kukhala ndi zolinga zoti zikwaniritsidwe pofuna kukwaniritsa cholinga chachikulu, kunam’thandiza motani mbale wina kuti akwaniritse cholinga chake chokatumikira pa Beteli?

5 Zinamuyendera Bwino: Mnyamata wina wa zaka 19, dzina lake Tony atakaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, anakhumbira utumiki wa pa Beteli. Komano, anali ndi moyo wolowerera, ndipo anali asanadzipatulire kwa Mulungu. Kenako, iye anaganiza zotsatira miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino, ndipo anakhala ndi cholinga choti abatizidwe. Atakwaniritsa cholinga chimenecho, anadziikiranso cholinga chochita upainiya wothandiza kenako upainiya wokhazikika, ndipo ankalemba pa kalendala yake masiku amene ankafuna kuyamba kuchita utumiki umenewu. Atachita upainiya umenewu kwa kanthawi ndithu, anaitanidwa kuti akatumikire pa Beteli. Tangoganizirani chimwemwe chimene anali nacho!

6. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mukwaniritse zolinga zanu zauzimu?

6 Inunso mungakwaniritse zolinga zanu zauzimu pamene mukufunafuna zinthu za Ufumu choyamba. Perekani ‘zochita zanu’ kwa Yehova m’pemphero ndipo yesetsani kuzikwaniritsa.—Miy. 16:3; 21:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena