Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/06 tsamba 3
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 8/06 tsamba 3

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 28, 2006. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya July 3 mpaka August 28, 2006. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. Kodi kuyang’ana omvetsera kumatithandiza bwanji kukhala aphunzitsi abwino? (Mat. 19:25, 26; Mac. 14:9, 10) [ be-CN tsa. 124 ndime 3 mpaka tsa. 125 ndime 3]

2. Kodi kulankhula mwachibadwa n’kofunika chifukwa chiyani, ndipo n’chiyani chingatithandize kulankhula motero muutumiki wakumunda? [be-CN tsa. 128 ndime 1 mpaka 5, bokosi]

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira zokhala anthu aukhondo? [be-CN tsa. 131 ndime 1 mpaka 3]

4. Kodi ‘kudzichepetsa ndi kudziletsa’ kuyenera kukhudza bwanji mmene timavalira ndi kudzikongoletsera? (1 Tim. 2:9, NW) [be-CN tsa. 131 ndime 4 mpaka tsa. 132 ndime 1]

5. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene tiyenera kuzitsatira kuti tisamaoneke ngati kuti tikukonda dzikoli? [be-CN tsa. 133 ndime 2-3]

NKHANI NA. 1

6. Kodi phindu lalikulu kwambiri la kuwerenga n’lotani? [July 10, [be-CN tsa. 21 ndime 3]

7. Kodi n’chiyani chimachititsa munthu kukhala wanzeru kapena kukhala wopusa? (Miy. 14:2) [w04-CN 11/15 tsa. 26 ndime 5]

8. Kodi n’chifukwa chiyani “wozindikira saona vuto m’kuphunzira”? (Miy. 14:6) [w04-CN 11/15 tsa. 28 ndime 4-5]

9. Kodi kuphunzira n’kutani? [be-CN tsa. 27 ndime 3]

10. Kodi kusinkhasinkha za chilengedwe cha Yehova kuyenera kutikhudza motani? [w04-CN 11/15 tsa. 8 ndime 4]

KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. Kodi kale, Yehova “anapatsa mawu” m’njira yotani n’kuchititsa kuti ‘khamu lalikulu la akazi lizilalikira uthenga’ ndipo kodi zimenezi zikuchitika motani masiku ano? (Sal. 68:11)

12. Kodi n’chiyani chinachititsa Asafu kutsala pang’onong’ono kusiya kuchita zoyenera, ndipo kodi n’chiyani chinamuthandiza kusintha maganizo akewo? (Sal. 73:2, 3, 17)

13. N’chifukwa chiyani mana amene Aisrayeli ankapatsidwa anali kutchedwa kuti “tirigu wa kumwamba” ndiponso kuti “mkate wa omveka”? (Sal. 78:24, 25)

14. Kodi “mthunzi wa Wamphamvuyonse,” [“malo achinsinsi a Wamphamvuyonse,” NW] ndi chiyani ndipo kodi tingakhalemo bwanji? (Salmo 91:1, 2)

15. Kodi imfa ya anthu omwe ali okhulupirika kwa Yehova n’njamtengo wapatali kwa Iye m’njira yotani? (Sal. 116:15)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena