Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu August: Mungathe kugwiritsa ntchito kalikonse ka timabuku ta masamba 32 totsatirati: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dikirani!, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha! September: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Yesetsani mwapadera kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo wanu woyamba. Bwererani kwa aliyense amene munam’gawira bukuli n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo la panyumba. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Munthu amene wasonyeza chidwi, muonetseni kabuku kakuti Dikirani! n’cholinga chokulitsa chidwi chomwe ali nacho pa zinthu za m’Baibulo. November: Tidzagawira buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Eninyumba akanena kuti alibe ana, apatseni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? kapena kapepala kena koyenerera.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo pa September 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Akatha kuwerengerako, mukalengeze kumpingo mukamawerenga lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Kalendala ya 2007 ya Mboni za Yehova, Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2007 ndi Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 2007 pa fomu yawo yotsatira yofunsira mabuku. Makalendala adzakhalapo m’Chichewa ndi Chingelezi, mabuku a Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku m’Chichewa, Chingelezi ndi Chitumbuka ndipo Yearbook idzakhalapo m’Chingelezi mokha.
◼ Alembi a mipingo aonetsetse kuti alemba ndi kutumiza Lipoti la Kaimidwe ka Mpingo (S-10) limodzi ndi lipoti la mipingo yawo la August.