Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Munthu amene wasonyeza chidwi, muonetseni kabuku kakuti Dikirani! n’cholinga chokulitsa chidwi chomwe ali nacho pa zinthu za m’Baibulo. November: Tidzagawira buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Eninyumba akanena kuti alibe ana, apatseni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? kapena kapepala kena koyenerera. December: Gawirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ngati mpingo wanu uli nawo. January: Gawirani buku la Chidziŵitso kapena kabuku ka Dikirani!
◼ Popeza mwezi wa December uli ndi milungu isanu yathunthu, udzakhala mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza.
◼ Mphatika imene ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno ndi “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2007.” Isungeni kuti mudzaigwiritse ntchito chaka chonse cha 2007.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya nyengo ya Chikumbutso ya 2007 idzakambidwa Lamlungu, pa April 15, 2007. Mutu wa nkhaniyi tidzaulengeza m’tsogolo muno. Mipingo imene idzakhale ikuchezeredwa ndi woyang’anira dera kapena msonkhano wadera kapenanso tsiku la msonkhano wapadera mlungu umenewo idzakhala ndi nkhani yapaderayi mlungu wotsatira. Mpingo uliwonse usadzakhale ndi nkhani yapaderayi pasanafike pa April 15.
◼ Mabuku Atsopano amene alipo:
Revelation—Its Grand Climax At Hand!—Zilembo Zazikulu—Chifalansa, Chingelezi, Chiswahili
Dziwani kuti buku limeneli lili ndi masamba 800 ndipo lilibe zithunzi.