Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2007
Malangizo
Dongosolo lotsatirali ndilo lidzagwiritsidwe ntchito pochititsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu mu 2007.
MABUKU OPHUNZIRA: Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu [bi53-CN], Nsanja ya Olonda [w-CN], Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu [be-CN], Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova [od-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN].
Sukulu iyenera kuyamba PANTHAWI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno n’kupitirira monga mmene asonyezera m’munsimu. Pambuyo pa nkhani iliyonse, woyang’anira sukulu atchule nkhani yotsatira ndi kuitana wokamba wake.
LUSO LA KULANKHULA: Mphindi 5. Woyang’anira sukulu, mlangizi wothandiza, kapena mkulu wina woyenerera adzafotokoza luso la kulankhula kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki. (Mipingo imene ili ndi akulu ochepa ingagwiritse ntchito atumiki othandiza oyenerera.)
NKHANI NA. 1: Mphindi 10. Mkulu woyenerera kapena mtumiki wothandiza woyenerera ndi amene ayenera kukamba nkhani imeneyi, ndipo izitengedwa mu Nsanja ya Olonda, m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kapena m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. Imeneyi ndi nkhani yolangiza imene iyenera kukambidwa kwa mphindi khumi. Cholinga chake chisakhale kufotokoza mwachisawawa mfundo za m’nkhaniyo koma kusonyeza phindu la mfundozo, ndi kutsindika mfundo zimene zingathandize kwambiri mpingowo. Agwiritse ntchito mutu wosonyezedwa. Abale amene apatsidwa nkhani imeneyi azionetsetsa kuti akusunga nthawi. Malangizo am’seri angaperekedwe ngati pakufunika kutero.
MFUNDO ZAZIKULU ZA KUWERENGA BAIBULO: Mphindi 10. Kwa mphindi zisanu zoyambirira, mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera afotokoze mmene machaputala omwe awerengedwa mlunguwo angathandizire mpingowo. Angafotokoze mbali ina iliyonse ya chigawo cha kuwerenga Baibulo cha mlunguwo. Isakhale chidule chabe cha gawo lowerenga mlunguwo. Cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvera kuzindikira chifukwa chake ndiponso mmene mfundozo zilili zaphindu. Wokamba nkhani ayenera kuonetsetsa kuti asapitirire mphindi zisanu zoperekedwa pa mbali yoyambirira imeneyi. Aonetsetse kuti wagwiritsa ntchito mphindi zisanu zomalizira kuti omvera alankhulepo. Apemphe omvera kulankhulapo mwachidule (kwa masekondi 30 kapena kucheperapo) pa mfundo za m’Baibulo zimene zinawasangalatsa powerenga ndiponso phindu lake. Ndiyeno woyang’anira sukulu apemphe ophunzira amene ali m’makalasi ena kupita ku makalasi awo.
NKHANI NA. 2: Mphindi 4 kapena zocheperapo. Iyi ndi nkhani yoti mbale awerenge. Wophunzira awerenge nkhani imene wapatsidwa popanda kunena mawu oyamba kapena omaliza. Woyang’anira sukulu makamaka adzaonetsetsa kuti akuthandiza wophunzira kuwerenga mosonyeza kuti akumvetsa zimene akuwerengazo, kuwerenga mosadodoma, kutsindika ganizo moyenera, kusinthasintha mawu, kupuma moyenera, ndiponso kuwerenga mwachibadwa.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhani imeneyi azikamba ndi alongo. Wophunzira amene wapatsidwa nkhani imeneyi angasankhe yekha kapena azipatsidwa mtundu wa makambirano kuchokera pa mndandanda umene uli patsamba 82 m’buku la Sukulu ya Utumiki. Wophunzira agwiritse ntchito mutu wa nkhani umene wapatsidwa ndipo agwirizanitse ndi mbali ya utumiki wakumunda yomwe ndi yotheka ndiponso yothandiza m’gawo la mpingowo. Ngati sanasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyo mwa kufufuza m’mabuku athu. Ophunzira atsopano azipatsidwa nkhani zimene tasonyeza buku limene nkhaniyo yachokera. Woyang’anira sukulu adzaonetsetsa makamaka mmene wophunzira akufotokozera nkhaniyo ndiponso mmene akuthandizira mwininyumba kulingalira pa Malemba ndi kumvetsa mfundo zazikulu za nkhaniyo. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi.
NKHANI NA. 4 Mphindi 5. Wophunzira akambe nkhani pa mutu umene wapatsidwa. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyo mwa kufufuza m’mabuku athu. Akapatsidwa mbale, aziikamba monga nkhani yokambira omvera amene asonkhana m’Nyumba ya Ufumuyo. Mlongo akapatsidwa nkhani imeneyi, nthawi zonse aziikamba mofanana ndi Nkhani Na. 3. Woyang’anira sukulu angapereke Nkhani Na. 4 kwa mbale nthawi ina iliyonse imene akuona kuti m’poyenera kupatsa mbale. Dziwani kuti nkhani zimene zili ndi nyenyezi ziyenera kuperekedwa kwa abale basi kuti akambe ngati nkhani.
MALANGIZO: Mphindi imodzi. Nkhani ya wophunzira isanayambe, woyang’anira sukulu sadzalengeza luso la kulankhula limene wophunzirayo wauzidwa kuti agwiritse ntchito. Wophunzira aliyense akamaliza Nkhani Na. 2, Na. 3, ndi Na. 4, woyang’anira sukulu adzanena mfundo zolimbikitsa za mbali ya nkhaniyo zimene wophunzirayo wachita bwino. Cholinga chake sindicho kungonena kuti “mwachita bwino” koma kutchula zifukwa zenizeni zimene zachititsa kuti mbali za nkhaniyo zikhale zogwira mtima. Malinga ndi zimene wophunzira aliyense akufunikira, malangizo ena othandiza angaperekedwe m’seri misonkhano itatha kapena panthawi ina.
KUSUNGA NTHAWI: Nkhani iliyonse isadye nthawi, chimodzimodzinso ndi ndemanga za mlangizi. Nkhani Na. 2 mpaka Na. 4 ziziimitsidwa mwaluso nthawi yake ikatha. Ngati abale amene akamba nkhani yotsegulira ya luso la kulankhula, Nkhani Na. 1, kapena mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo adya nthawi, azilangizidwa m’seri. Aliyense ayenera kusamala kwambiri nthawi. Pulogalamu yonse izitenga mphindi 45, osaphatikizapo nthawi ya nyimbo ndi pemphero.
FOMU YOLANGIZIRA: Ili m’buku momwemo.
MLANGIZI WOTHANDIZA: Bungwe la akulu lingasankhe mkulu waluso, ngati alipo, kuphatikiza pa woyang’anira sukulu, kuti akhale mlangizi wothandiza. Ngati pali akulu angapo pa mpingo, ndiye kuti chaka chilichonse mkulu wina woyenerera angasamalire udindo umenewu. Ntchito yake idzakhala yopereka malangizo am’seri, ngati angafunike, kwa abale amene akamba Nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu za Baibulo. N’kosafunika kuti azipereka malangizo kwa akulu anzake kapena atumiki othandiza nthawi iliyonse yomwe akamba nkhani zimenezi.
KUBWEREZA: Mphindi 30. Miyezi iwiri iliyonse, woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwerezaku. Kudzatsatira pambuyo pa kukambirana luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo monga mmene tafotokozera pamwambapa. Kubwereza kudzakhala kwa nkhani zimene zinakambidwa m’sukulu m’miyezi iwiri yapita, kuphatikizapo mlungu wa kubwerezaku. Ngati mpingo wanu udzakhala ndi msonkhano wadera mlungu umene muyenera kukhala ndi kubwereza, ndiye kuti kubwerezako (limodzinso ndi pulogalamu ya mlungu ndi mlungu ya mlungu umenewo) ziyenera kudzachitika mlungu wotsatira ndipo pulogalamu ya mlungu wotsatirawo iyenera kuchitidwa mlungu wa msonkhanowo. Ngati woyang’anira dera akuchezera mpingo wanu mlungu umene muyenera kukhala ndi kubwerezaku, ndiye kuti nyimbo, luso la kulankhula, ndiponso mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo ziyenera kuchitika mogwirizana ndi ndandanda ya mlungu umenewo. Ndiyeno nkhani yachilangizo (yokambidwa pambuyo pa luso la kulankhula) iyenera kutengedwa ku ndandanda ya mlungu wotsatira. Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu wotsatira idzakhala ndi luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo mogwirizana ndi mmene zilili pa ndandanda ya mlunguwo, ndipo kubwereza kudzatsatira pambuyo pake.
NDANDANDA
Jan. 1 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 24-28 Nyimbo33
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Mmene Mfundo Zimagwirira Ntchito (be-CN tsa. 158 ndime 1-3)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani ya Wophunzira mu Sukulu (be-CN tsa. 43 ndime 1–tsa. 44 ndime 3)
Na. 2: Yesaya 26:1-18
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kutaya Mimba N’koletsedwa? (rs-CN mas. 210-211 ndime 8)
Na. 4: Kodi ‘Tingavale Ambuye Yesu Kristu’ Motani? (Aroma 13:14)
Jan. 8 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 29-33 Nyimbo 42
Luso la Kulankhula: Kuthandiza Ena Kuona Phindu la Nkhani Yanu (be-CN tsa. 159 ndime1-4)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani Yokambirana (be-CN tsa. 44 ndime 4–tsa. 46 ndime 2)
Na. 2: Yesaya 30:1-14
Na. 3: a Kuyankha Munthu Amene Anganene kuti: ‘Ine Ndili ndi Ufulu Wochita Chimene Ndikufuna Pankhani Zokhudza Thupi Langa’ (rs-CN tsa. 212 ndime 1)
Na. 4: Mmene Timadziwira Kuti Yehova Mulungu Amakonda Ana
Jan. 15 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 34-37 Nyimbo 222
Luso la Kulankhula: Kusankha Bwino Mawu (be-CN tsa. 160 ndime 1-3)
Na. 1: Kukhala ndi Maganizo a Yesu pa Nkhani ya Chabwino ndi Choipa (w05-CN 1/1 mas. 9-10 ndime 11-15)
Na. 2: Yesaya 34:1-15
Na. 3: Mmene Tingakhalire ndi Chikondi Chenicheni
Na. 4: Kodi Adamu ndi Hava Anali Anthu Enieni a M’mbiri? (rs-CN mas. 25-26)
Jan. 22 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 38-42 Nyimbo 61
Luso la Kulankhula: Kulankhula Kosavuta Kumva (be-CN tsa. 161 ndime 1-4)
Na. 1: Osafooka Chifukwa Chotsutsidwa (w05-CN 1/1 tsa. 15 ndime 16-18)
Na. 2: Yesaya 38:9-22
Na. 3: b Kuyankha Munthu Amene Anganene Kuti: ‘Tchimo la Adamu Linali Chifuniro cha Mulungu’ (rs-CN tsa. 27 ndime 1-2)
Na. 4: Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Kuganiza Kuti Anthu Ena Ali ndi Zolinga Zoipa
Jan. 29 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 43-46 Nyimbo 113
Luso la Kulankhula: Mawu Osiyanasiyana ndi Olondola (be-CN tsa. 161 ndime 5–tsa. 162 ndime 4)
Na. 1: Chifukwa Chake Tiyenera Kuvomereza Ziweruzo za Yehova (w05-CN 2/1 mas. 23-24 ndime 4-9)
Na. 2: Yesaya 45:1-14
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kulambira Makolo N’kosathandiza? (rs-CN tsa. 188 ndime 1–tsa. 189 ndime 6)
Na. 4: c Chifukwa Chake Akristu Ayenera Kupewa Kudziyerekezera ndi Ena Mwampikisano
Feb. 5 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 47-51 Nyimbo 79
Luso la Kulankhula: Mawu Opereka Mphamvu, Okhudza Mtima, ndi Opereka Bwino Chithunzi (be-CN tsa. 163 ndime 1–tsa. 164 ndime 2)
Na. 1: Mawu a Yehova Amatithandiza Kukhala Oyera Ndiponso Kukhala Okhulupirika (w05-CN 4/15 mas. 11-12 ndime 5-11)
Na. 2: Yesaya 50:1-11
Na. 3: Chifukwa Chake Kulambira Makolo Kuli Kosakondweretsa Yehova Mulungu (rs-CN tsa. 189 ndime 7–tsa. 190 ndime 3)
Na. 4: Kodi Baibulo Limalimbikitsa Kusapereka Mphatso?
Feb. 12 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 52-57 Nyimbo 139
Luso la Kulankhula: Kalankhulidwe Kotsatira Galamala (be-CN tsa. 164 ndime 3–tsa. 165 ndime 1)
Na. 1: Mawu a Yehova Amatilimbitsa Mtima (w05-CN 4/15 tsa. 12 ndime 12-14)
Na. 2: Yesaya 55:1-13
Na. 3: Kukhala ndi Moyo Wodzimana N’kothandiza
Na. 4: Kodi Ndani Amene ali Okana Kristu? (rs-CN mas. 414-415)
Feb. 19 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 58-62 Nyimbo 189
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Autilaini (be-CN tsa. 166 ndime 1–tsa. 167 ndime 1)
Na. 1: Ana Athu Ndi Cholowa Chamtengo Wapatali (w05-CN 4/1 tsa. 8 ndime 1–tsa. 9 ndime 9)
Na. 2: Yesaya 60:1-14
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kukhala Kapolo wa Mulungu Kuli Chinthu Chovomerezeka?
Na. 4: d Kuzindikira Anthu a Mpatuko (rs-CN tsa. 299 ndime 5–tsa. 301 ndime 2)
Feb. 26 Kuwerenga Baibulo: Yesaya 63-66 Nyimbo 141
Luso la Kulankhula: Kukonza Maganizo Anu (be-CN tsa. 167 ndime 2–tsa. 168 ndime 1)
Oral Review
Mar. 5 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 1-4 Nyimbo 70
Luso la Kulankhula: Lembani Autilaini Yosavuta (be-CN tsa. 168 ndime 2–tsa. 169 ndime 5)
Na. 1: Zoyenereza za m’Malemba za Atumiki Othandiza (od-CN tsa. 54 ndime 1-tsa. 56 ndime 1)
Na. 2: Yeremiya 3:1-13
Na. 3: Kodi N’chiyani Chimene Chimabweretsa Chimwemwe Chenicheni?
Na. 4: e Kodi Ampatuko Tiyenera Kuwaona Motani? (rs-CN tsa. 301 ndime 3–tsa. 302 ndime 3)
Mar. 12 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 5-7 Nyimbo 159
Luso la Kulankhula: Kukamba Nkhani M’njira Yotsatirika (be-CN tsa. 170 ndime 1–tsa. 171 ndime 2)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani Zokambira Mpingo (be-CN tsa. 47 ndime 1–tsa. 49 ndime 1)
Na. 2: Yeremiya 5:1-14
Na. 3: Kristu Sanamange Tchalitchi pa Petro (rs-CN tsa.196 ndime 1–tsa.198 ndime 2)
Na. 4: Kugwiritsa Ntchito Phunziro la pa Eksodo 14:11 M’nthawi Yathu Ino
Mar. 19 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 8-11 Nyimbo 182
Luso la Kulankhula: Kukamba Nkhani mwa Ndondomeko Yotsatirika (be-CN tsa. 171 ndime 3–tsa. 172 ndime 6)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani za Msonkhano wa Utumiki Ndiponso Nkhani Zina (be-CN tsa. 49 ndime 2–tsa. 51 ndime 2)
Na. 2: Yeremiya 10:1-16
Na. 3: Kodi Timadziwa Bwanji Kuti Abrahamu, Yobu, ndi Danieli Anali Ndi Chikhulupiriro Choti Akufa Adzauka?
Na. 4: Kodi Mfungulo Zimene Petro Anagwiritsa Ntchito Zinali Chiyani? (rs-CN tsa. 198 ndime 3–tsa. 200 ndime 4)
Mar. 26 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 12-16 Nyimbo 205
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Mfundo Zoyenera Zokha (be-CN tsa. 173 ndime 1-4)
Na. 1: Dipo Limasonyeza Bwino Chilungamo cha Mulungu (w05-CN 11/1 mas. 13-14)
Na. 2: Yeremiya 12:1-13
Na. 3: Anthu “Olowa M’malo Atumwi” Si Akristu Oona (rs-CN tsa. 200 ndime 5–tsa. 203 ndime 1)
Na. 4: Kodi ndi Motani Mmene Akristu Angakhalire Okondwa?
Apr. 2 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 17-21 Nyimbo 30
Luso la Kulankhula: Kulankhula Kuchokera mu Mtima (be-CN tsa. 174 ndime 1–tsa. 175 ndime 5)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani za Onse (be-CN tsa. 52 ndime 1–tsa. 54 ndime 1)
Na. 2: Yeremiya 20:1-13
Na. 3: Kodi Armagedo Idzamenyedwera Kuti? (rs-CN tsa. 37 ndime 3–tsa. 39 ndime 3)
Na. 4: f Kodi Tiyenera Kuona Motani Uphungu?
Apr. 9 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 22-24 Nyimbo 184
Luso la Kulankhula: Pewani Mbuna za Kulankhula Kochokera mu Mtima (be-CN tsa. 175 ndime 6–tsa. 177 ndime 2)
Na. 1: Zimene Wokamba Nkhani Ayenera Kusankha (be-CN tsa. 54 ndime 2-4; tsa. 55, bokosi)
Na. 2: Yeremiya 23:1-14
Na. 3: Chifukwa Chake Kugwira Nawo Ntchito Yolalikira Kumapatsa Chimwemwe
Na. 4: Kodi Ndani Kapena N’chiyani Chomwe Chidzawonongedwa pa Armagedo? (rs-CN tsa. 39 ndime 4–tsa. 40 ndime 2)
Apr. 16 Yeremiya 25-28 Nyimbo 27
Luso la Kulankhula: Pamene Ena Afunsa Chifukwa (be-CN tsa. 177 ndime 3–tsa. 178 ndime 3)
Na. 1: Kulitsani Luso la Kuphunzitsa (be-CN tsa. 56 ndime 1–tsa. 57 ndime 2)
Na. 2: Yeremiya 26:1-15
Na. 3: Kodi Ndani Amene Adzapulumuke Armagedo (rs-CN tsa. 40 ndime 3-8)
Na. 4: Kodi Nthaka Inakhala Yotembereredwa M’njira Yotani? (Gen. 3:17)
Apr. 23 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 29-31 Nyimbo 148
Luso la Kulankhula: Kukamba Nkhani Mmene Mumalankhulira ndi Anthu (be-CN mas. 179-180)
Na. 1: “Musiyanitse” (be-CN tsa. 57 ndime 3–tsa. 58 ndime 2)
Na. 2: Yeremiya 31:1-14
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Ukulu wa Yehova Uli Wopanda Malire?
Na. 4: Kuwonongedwa kwa Anthu Oipa pa Armagedo Sikudzatanthauza Kuti Mulungu Waphwanya Chikondi Chake (rs-CN tsa. 41 ndime 1-3)
Apr. 30 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 32-34 Nyimbo 100
Luso la Kulankhula: Kamvekedwe Kabwino ka Mawu (be-CN tsa. 181 ndime 1-4)
Kubwereza
May 7 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 35-38 Nyimbo 165
Luso la Kulankhula: Kapumidwe Koyenera (be-CN tsa. 181 ndime 5–tsa. 183 ndime 2; tsa. 182, bokosi)
Na. 1: Limbikitsani Omvera Kulingalira (be-CN tsa. 58 ndime 3–tsa. 59 ndime 3)
Na. 2: Yeremiya 36:1-13
Na. 3: N’zosatheka Kusakhudzidwa ndi Zomwe Zidzachitike pa Armagedo (rs-CN tsa. 41 ndime 4-7)
Na. 4: Kodi Akristu Angalimbane Bwanji ndi Vuto Lodera Nkhawa Zinthu Zam’tsogolo?
May 14 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 39-43 Nyimbo 56
Luso la Kulankhula: Kumasula Minofu Yokungika (be-CN tsa. 184 ndime 1–tsa. 185 ndime 2; tsa. 184, bokosi)
Na. 1: Sonyezani Mmene Zimagwirira Ntchito Ndiponso Khalani Chitsanzo Chabwino (be-CN tsa. 60 ndime 1–tsa. 61 ndime 3)
Na. 2: Yeremiya 39:1-14
Na. 3: Kodi Ndi Ndani Amene Akulimbikitsa Anthu Padzikoli Kuchita Zinthu Zimene Zidzawasonkhanitsira ku Armagedo? (rs-CN tsa. 41 ndime 8–tsa. 42 ndime 1)
Na. 4: g Chifukwa Chake Akristu Oona Amakhala Odzisunga Pamene Ali Pachibwenzi
May 21 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 44-48 Nyimbo 122
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Chidwi mwa Munthu Winayo (be-CN tsa. 186 ndime 1-4)
Na. 1: Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu (be-CN tsa. 62 ndime 1–tsa. 64 ndime 1)
Na. 2: Yeremiya 46:1-17
Na. 3: Kodi Kudzinyenga Tokha N’kutani, Ndipo Tingakupewe Bwanji?
Na. 4: Kuzindikira Babulo Wamkulu Wotchulidwa M’buku la Chivumbulutso (rs-CN tsa. 47 ndime 3–tsa. 48 ndime 1)
May 28 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 49-50 Nyimbo 95
Luso la Kulankhula: Mvetserani Mosamala (be-CN tsa. 186 ndime 5–tsa. 187 ndime 4)
Na. 1: Mmene Mungapitirizire Kucheza Kwanu (be-CN tsa. 64 ndime 2–tsa. 65 ndime 4)
Na. 2: Yeremiya 49:14-27
Na. 3: Kodi Babulo Wakale Ankadziwika ndi Makhalidwe Otani? (rs-CN tsa. 48 ndime 2–tsa. 50 ndime 2)
Na. 4: Chifukwa Chimene Makolo Ayenera Kumawerengera Ana awo Mabuku
June 4 Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 51-52 Nyimbo 166
Luso la Kulankhula: Kuthandiza Ena Kupita Patsogolo (be-CN tsa. 187 ndime 5–tsa. 188 ndime 3)
Na. 1: Atumiki Othandiza Amachita Ntchito Yofunika (od-CN tsa. 56 ndime 2-tsa. 58 ndime 3)
Na. 2: Yeremiya 52:1-16
Na. 3: N’kupusa Kufuna Kukhala Wodziimira Pawekha Osadalira Mulungu
Na. 4: Mmene Zipembedzo Zimene Zimati N’zachikristu Zilili Mbali ya Babulo Wamkulu (rs-CN tsa. 50 ndime 3–tsa. 51 ndime 3)
June 11 Kuwerenga Baibulo: Maliro 1-2 Nyimbo 129
Luso la Kulankhula: Athandizeni pa Zosowa Zawo (be-CN tsa. 188 ndime 4–tsa. 189 ndime 4)
Na. 1: Kufunika kwa Misonkhano ya Mpingo (od-CN tsa.59 ndime 1-tsa. 61 ndime 1)
Na. 2: Maliro 2:1-10
Na. 3: Kodi N’chifukwa Ninji Kutuluka m’Babulo Wamkulu Mofulumira Kuli Kofunika? (rs-CN tsa. 51 ndime 4–tsa. 52 ndime 3)
Na. 4: Kukhala ndi Chifundo Chenicheni Sikumatanthauza Kuti Munthuyo Ndi Wofooka
June 18 Kuwerenga Baibulo: Maliro 3-5 Nyimbo 140
Luso la Kulankhula: Kulemekeza Ena (be-CN tsa. 190 ndime 1–tsa. 191 ndime 1)
Na. 1: Kupindula ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda (od-CN tsa. 61 ndime 2-tsa. 62 ndime 2)
Na. 2: Maliro 4:1-13
Na. 3: Zimene Ubatizo Umatanthauza, Ndiponso Chifukwa Chake Anthu Okhulupirira Amabatizidwa (rs-CN tsa. 364 ndime 1-4)
Na. 4: h Chifukwa Chimene Akristu Oona Samatenga Nawo Mbali M’ndale
June 25 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 1-5 Nyimbo 1
Luso la Kulankhula: Ulemu Pokumana ndi Anthu (be-CN tsa. 191 ndime 1–tsa. 192 ndime 1)
Kubwereza
July 2 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 6-10 Nyimbo 26
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwaulemu (be-CN tsa. 192 ndime 2–tsa. 193 ndime 2)
Na. 1: Kupindula ndi Msonkhano wa Onse (od-CN tsa. 62 ndime 3-tsa. 64 ndime 2)
Na. 2: Ezekieli 7:1-13
Na. 3: Zimene Zimafunika Kuti Muyandikire kwa Yehova (Yak. 4:8)
Na. 4: Kuwaza Madzi Kapena Kubatiza Makanda, Si Ubatizo Wachikristu (rs-CN tsa. 364 ndime 5–tsa. 365 ndime 3)
July 9 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 11-14 Nyimbo 112
Luso la Kulankhula: Kulankhula Motsimikiza (be-CN tsa. 194 ndime 1–tsa. 195 ndime 2)
Na. 1: Musaleme Pakuchita Zabwino (w05-CN 6/1 mas. 29-30)
Na. 2: Ezekieli 11:1-13
Na. 3: Kodi Ubatizo Wam’madzi Wachikristu Umachotsa Machimo? (rs-CN tsa. 365 ndime 4–tsa. 366 ndime 1)
Na. 4: Kodi Mawu a pa Chivumbulutso 17:9-11 Akutanthauzanji?
July 16 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 15-17 Nyimbo 29
Luso la Kulankhula: Mmene Mungalankhulire Motsimikiza (be-CN tsa. 195 ndime 3–tsa. 196 ndime 4)
Na. 1: Pewani Maganizo Olakwika (w05-CN 9/15 mas. 26-28)
Na. 2: Ezekieli 16:1-13
Na. 3: Zimene Kukhala Wochenjera Kumatanthauza (Miy. 13:16)
Na. 4: Kodi Ndani Amabatizidwa ndi Mzimu Woyera? (rs-CN tsa.366 ndime 2–tsa. 367 ndime 3)
July 23 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 18-20 Nyimbo 193
Luso la Kulankhula: Khalani Wosamala Komanso Wolimba (be-CN tsa. 197 ndime 1-3)
Na. 1: Kuzindikira Maganizo a Wofunsayo (be-CN tsa. 66 ndime 1–tsa. 68 ndime 1)
Na. 2: Ezekieli 18:19-29
Na. 3: Kubatizidwa ndi Moto N’kosiyana ndi Kubatizidwa ndi Mzimu Woyera (rs-CN tsa. 367 ndime 4–tsa. 368 ndime 1)
Na. 4: Umboni Wosonyeza Kuti Ufumu wa Mulungu Ndi Weniwenidi
July 30 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 21-23 Nyimbo 35
Luso la Kulankhula: Kusamala Polalikira (be-CN tsa. 197 ndime 4–tsa. 198 ndime 5)
Na. 1: Dziwani Mayankhidwe Oyenera (be-CN tsa. 68 ndime 2–tsa. 70 ndime 3)
Na. 2: Ezekieli 23:1-17
Na. 3: Zifukwa Zophunzirira Baibulo (rs-CN tsa. 52 ndime 4–tsa. 54 ndime 2)
Na. 4: Kodi Maganizo Oyenerera Pankhani ya Kukhala Wamkulu ndi Wotchuka ndi Otani?
Aug. 6 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 24-27 Nyimbo 37
Luso la Kulankhula: Mawu Oyenera Panthawi Yoyenera (be-CN tsa. 199 ndime 1-4)
Na. 1: Kukambirana M’makalata (be-CN tsa. 71-73)
Na. 2: Ezekieli 24:1-14
Na. 3: Kodi Mose Anasonyeza Chitsanzo Chabwino Kwambiri M’njira Ziti, Zimene Akristu Angatengereko Phunziro?
Na. 4: Umboni wa M’mabuku a Yesaya ndi Yeremiya Wosonyeza Kuti Baibulo N’louziridwa (rs-CN tsa. 54 ndime 3–tsa. 55 ndime 2)
Aug. 13 Ezekieli 28-31 Nyimbo 123
Luso la Kulankhula: Kukhala Wosamala kwa a Pabanja Pathu ndi Akristu Anzathu (be-CN tsa. 200 ndime 1-4)
Na. 1: Khalani Womapitabe Patsogolo (be-CN tsa. 74 ndime 1–tsa. 75 ndime 3)
Na. 2: Ezekieli 28:1-16
Na. 3: Kukwaniritsidwa kwa Maulosi a Yesu Kumatsimikizira Kuti Baibulo N’louziridwa (rs-CN tsa. 55 ndime 3-4)
Na. 4: Zimene Mawu Akuti “Kudana ndi Chinthu” Amatanthauza M’Malemba
Aug. 20 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 32-34 Nyimbo 215
Luso la Kulankhula: Khalani Wolimbikitsa (be-CN tsa. 202 ndime 1–tsa. 203 ndime 2)
Na. 1: Gwiritsani Ntchito Mphatso Yanu (be-CN tsa. 75 ndime 4–tsa. 77 ndime 2)
Na. 2: Ezekieli 34:1-14
Na. 3: Kodi Mzimu wa Mulungu Umatithandiza Bwanji?
Na. 4: Baibulo N’lolondola Pankhani za Sayansi (rs-CN tsa. 56 ndime 1–tsa. 58 ndime 2)
Aug. 27 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 35-38 Nyimbo 94
Luso la Kulankhula: Mawu Anu Azimveka Olimbikitsa (be-CN tsa. 203 ndime 3–tsa. 204 ndime 1)
Kubwereza
Sept. 3 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 39-41 Nyimbo 194
Luso la Kulankhula: Pocheza ndi Okhulupirira Anzathu (be-CN tsa. 204 ndime 2–tsa. 205 ndime 4)
Na. 1: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukonda Mawu a Mulungu? (w05-CN 4/15 mas. 15-16 ndime 3-6)
Na. 2: Ezekieli 40:1-15
Na. 3: Kodi Anthu Angathedi Kum’kondweretsa Mulungu?
Na. 4: i Kuyankha Anthu Amene Amatsutsa Baibulo (rs-CN tsa. 58 ndime 3–tsa. 62 ndime 1)
Sept. 10 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 42-45 Nyimbo 77
Luso la Kulankhula: Kubwereza Komveketsa Mfundo (be-CN tsa. 206 ndime 1-4)
Na. 1: Ukalamba Umene Uli “Korona wa Ulemu” (w05-CN 1/15 mas. 8-9)
Na. 2: Ezekieli 43:1-12
Na. 3: Chifukwa Chake Akristu Samakondwerera Masiku a Kubadwa (rs-CN tsa. 362 ndime 1–tsa. 363 ndime 3)
Na. 4: j Kodi Tingadziwe Bwanji “Mawu a Alendo”? (Yohane 10:5)
Sept. 17 Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 46-48 Nyimbo 164
Luso la Kulankhula: Kubwereza mu Utumiki wa Kumunda Ndiponso Pokamba Nkhani (be-CN tsa. 207 ndime 1–tsa. 208 ndime 3)
Na. 1: Cholinga cha Msonkhano wa Utumiki (od-CN tsa. 64 ndime 3-tsa. 67 ndime 2)
Na. 2: Ezekieli 47:1-14
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Amasala Mwazi? (rs-CN tsa. 313 ndime 2–tsa. 315 ndime 1)
Na. 4: k N’chifukwa Chiyani Chuma Chauzimu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Yomwe Makolo Angasiyire Ana Awo?
Sept. 24 Kuwerenga Baibulo: Danieli 1-3 Nyimbo 179
Luso la Kulankhula: Kutambasula Mutu wa Nkhani (be-CN tsa. 209 ndime 1-3)
Na. 1: Cholinga cha Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (od-CN tsa. 67 ndime 3-tsa 69 ndime 1)
Na. 2: Danieli 2:1-16
Na. 3: Chifukwa Chake Nambala ya 144,000 Imaonedwa Kuti Ndi Yosaphiphiritsa (Chiv. 7:4)
Na. 4: Chifukwa Chimene Akristu Oona Amakanira Kuikidwa Magazi (rs-CN tsa. 315 ndime 2–tsa. 316 ndime 3)
Oct. 1 Kuwerenga Baibulo: Danieli 4-6 Nyimbo 14
Luso la Kulankhula: Kusankha Mutu Woyenera (be-CN tsa. 210 ndime 1–tsa. 211 ndime 1; tsa. 211, bokosi)
Na. 1: Kodi Kukhumudwa Koyenera N’kotani? (w05-CN 8/1 mas. 13-15)
Na. 2: Danieli 4:1-17
Na. 3: Kodi Tingatsanzire Motani Makhalidwe Abwino a Mefiboseti?
Na. 4: l Kuyankha Munthu Amene Angafune Kudziwa Zimene Timakhulupirira Pankhani ya Kuikidwa Magazi (rs-CN tsa. 317 ndime 1–tsa. 319 ndime 1)
Oct. 8 Kuwerenga Baibulo: Danieli 7-9 Nyimbo 34
Luso la Kulankhula: Kuunika Mfundo Zazikulu (be-CN tsa. 212 ndime 1–tsa. 213 ndime 2)
Na. 1: “Mawu” a Yehova Azikutchinjirizani (w05-CN 9/1 mas. 28-31)
Na. 2: Danieli 7:1-12
Na. 3: Kodi Kubadwanso Kumatanthauza Chiyani? (rs-CN tsa. 157 ndime 1–tsa. 158 ndime 8)
Na. 4: Kodi Kutenga Nawo Mbali Nthawi Zonse mu Utumiki wa Kumunda Kumabweretsa Chimwemwe Chapadera Chotani?
Oct. 15 Kuwerenga Baibulo: Danieli 10-12 Nyimbo 210
Luso la Kulankhula: Musachulukitse Mfundo Zazikulu (be-CN tsa. 213 ndime 3–tsa. 214 ndime 5)
Na. 1: Muzipindula Kwambiri ndi Phunziro la Buku la Mpingo (od-CN tsa. 69 ndime 2-tsa. 72 ndime 1)
Na. 2: Danieli 11:1-14
Na. 3: Mmene Kudzichepetsa Kungatithandizire Kuti Tithetse Vuto la Kusamvetsetsana
Na. 4: Kuti Munthu Adzapulumuke, Sizidalira Kuti Akhale Wobadwanso (rs-CN tsa. 159 ndime 1–tsa. 160 ndime 1)
Oct. 22 Kuwerenga Baibulo: Hoseya 1-7 Nyimbo 66
Luso la Kulankhula: Mawu Oyamba Okopa Chidwi (be-CN tsa. 215 ndime 1–tsa. 216 ndime 4)
Na. 1: Mipata Yothandiza Kuwonjezera Mayanjano Achikristu (od-CN tsa. 72 ndime 2-tsa. 75 ndime 1)
Na. 2: Hoseya 5:1-15
Na. 3: a Kuyankha Anthu Amene Angatifunse Pankhani Yokhudza Kubadwanso (rs-CN tsa. 160 ndime 3–tsa. 161 ndime 2)
Na. 4: Mmene Akristu Oona Amasonyezera Kuleza Mtima
Oct. 29 Kuwerenga Baibulo: Hoseya 8-14 Nyimbo 59
Luso la Kulankhula: Kukopa Chidwi cha Anthu Pamene Muli mu Utumiki wa Kumunda (be-CN tsa. 216 ndime 5–tsa. 217 ndime 3)
Kubwereza
Nov. 5 Kuwerenga Baibulo: Yoweli 1-3 Nyimbo 166
Luso la Kulankhula: Tchulani Nkhani Yanu M’mawu Oyamba (be-CN tsa. 217 ndime 4–tsa. 219 ndime 1)
Na. 1: Mgonero wa Ambuye—Msonkhano Wofunika Kwambiri wa Pachaka (od-CN tsa. 75 ndime 2-tsa. 76 ndime 3)
Na. 2: Yoweli 2:1-14
Na. 3: Zimene Kukhala ndi “Chikondi Changwiro” Kumatanthauza (1 Yohane 4:18)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Kuulula Machimo Pamaso pa Wansembe Kuli Kosagwirizana ndi Malemba? (rs-CN tsa. 218 ndime 2–tsa. 219 ndime 6)
Nov. 12 Kuwerenga Baibulo: Amosi 1-9 Nyimbo 211
Luso la Kulankhula: Mawu Omaliza Ogwira Mtima (be-CN tsa. 220 ndime 1-3)
Na. 1: Atumiki a Uthenga Wabwino Amatsanzira Yesu, Yemwe Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri (od-CN tsa. 77 ndime 1-tsa. 78 ndime 2)
Na. 2: Amosi 2:1-16
Na. 3: Chikwa Chake Kudziwa Zinthu Sikutanthauza Kukhala Mphunzitsi Wabwino
Na. 4: Kuulula Machimo Amene Munthu Wachimwira Mulungu Ndiponso Munthu Mnzake (rs-CN tsa. 220 ndime 5–tsa. 221 ndime 6)
Nov. 19 Kuwerenga Baibulo: Obadiya 1–Yona 4 Nyimbo 220
Luso la Kulankhula: Mfundo Zofunika Kuzikumbukira (be-CN tsa. 221 ndime 1-5)
Na. 1: Kuthandiza Anthu Atsopano Kuti Ayambe Kufalitsa (od-CN tsa. 78 ndime 3-tsa. 81 ndime 3)
Na. 2: Yona 1:1-17
Na. 3: Chifukwa Chimene Paradaiso Wauzimu Ayenera Kukhalapo Kaye Paradaiso Wapadziko Lapansi Asanayambe
Na. 4: b N’chifukwa Chiyani Machimo Akuluakulu Ayenera Kuululidwa kwa Akulu? (rs-CN tsa. 221 ndime 7–tsa. 222 ndime 2)
Nov. 26 Kuwerenga Baibulo: Mika 1-7 Nyimbo 18
Luso la Kulankhula: Mu Utumiki wa Kumunda (be-CN tsa. 221 ndime 6–tsa. 222 ndime 6)
Na. 1: Kuthandiza Ana Aang’ono Kuti Akhale Ofalitsa (od-CN tsa. 81 ndime 4–tsa. 83 ndime 1)
Na. 2: Mika 2:1-13
Na. 3: Zimene Kukhala Wofatsa Kumatanthauza
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Kuli Kwanzeru Kukhulupirira Chilengedwe? (rs-CN tsa. 74 ndime 2–tsa. 76 ndime 1)
Dec. 3 Kuwerenga Baibulo: Nahumu 1–Habakuku 3 Nyimbo 137
Luso la Kulankhula: Kunena Zoona Zokhazokha (be-CN tsa. 223 ndime 1-5)
Na. 1: N’chifukwa Chiyani Timasunga Lipoti la Utumiki wa Kumunda? (od-CN tsa. 83 ndime 2-tsa. 84 ndime 2)
Na. 2: Habakuku 1:1-17
Na. 3: Kumvetsa Nkhani ya M’Baibulo Yonena za Chilengedwe (rs-CN tsa. 76 ndime 2–tsa. 78 ndime 3)
Na. 4: Chifukwa Chake Moyo Wosatha Sudzakhala Wotopetsa
Dec. 10 Kuwerenga Baibulo: Zefaniya 1–Hagai 2 Nyimbo 78
Luso la Kulankhula: ‘Kugwiritsa Mawu Okhulupirika’ (be-CN tsa. 224 ndime 1-4)
Na. 1: Kodi Lipoti Lanu la Utumiki wa Kumunda N’chiyani? (od-CN tsa. 85 ndime 1-tsa. 87 ndime 2)
Na. 2: Zefaniya 3:1-17
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kulambira Mtanda N’kosagwirizana ndi Malemba? (rs-CN tsa. 305 ndime 3–tsa. 306 ndime 4)
Na. 4: c Kodi Ukwati Ungakhale Wotani Ngati Okwatiranawo Ali Paubwenzi Wabwino ndi Mulungu?
Dec. 17 Kuwerenga Baibulo: Zekariya 1-8 Nyimbo 209
Luso la Kulankhula: Tsimikizirani Zochokera ku Magwero Ena Kuti N’zolondola (be-CN tsa. 225 ndime 1-3)
Na. 1: N’chifukwa Chiyani Timapereka Lipoti la Utumiki wa Kumunda? (od-CN tsa. 88 ndime 1-tsa. 90 ndime 1)
Na. 2: Zekariya 7:1-14
Na. 3: Kodi Masomphenya a Kusandulika kwa Yesu Akukwaniritsidwa Motani?
Na. 4: Kodi Zaka Zakubadwa za Anthu Amene Anakhalapo Chigumula Chisanafike Zinkapimidwa Mofanana ndi Zaka Zimene Tikugwiritsa Ntchito? (rs-CN tsa. 230 ndime 4–tsa. 231 ndime 1)
Dec. 24 Kuwerenga Baibulo: Zekariya 9-14 Nyimbo 202
Luso la Kulankhula Kulankhula Zomveka Bwino kwa Ena (be-CN tsa. 226 ndime 1–tsa. 227 ndime 2)
Na. 1: Kudziikira Zolinga (od-CN tsa. 90 ndime 2-tsa. 91 ndime 2)
Na. 2: Zekariya 10:1-12
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Zimanena Kuti Ufumu wa Mulungu Unakhazikitsidwa mu 1914? (rs-CN tsa. 231 ndime 2–tsa. 233 ndime 2)
Na. 4: Kodi Chizunzo Tingachikonzekere Motani?
Dec. 31 Kuwerenga Baibulo: Malaki 1-4 Nyimbo 118
Luso la Kulankhula: Kufotokoza Mawu Achilendo (be-CN tsa. 227 ndime 3–tsa. 228 ndime 1)
Kubwereza
[Mawu a M’munsi]
a Mogwirizana ndi zimene zingachitikedi m’gawo la mpingo wanu, ndiponso ngati nthawi ingalole, sonyezani mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zosiyanasiyana, mmene tingatsimikizire kuti mfundo zathu n’zoonadi, ndiponso mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zotsutsa.
b Mogwirizana ndi zimene zingachitikedi m’gawo la mpingo wanu, ndiponso ngati nthawi ingalole, sonyezani mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zosiyanasiyana, mmene tingatsimikizire kuti mfundo zathu n’zoonadi, ndiponso mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zotsutsa.
c Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
d Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
e Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
f Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
g Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
h Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
i Mogwirizana ndi zimene zingachitikedi m’gawo la mpingo wanu, ndiponso ngati nthawi ingalole, sonyezani mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zosiyanasiyana, mmene tingatsimikizire kuti mfundo zathu n’zoonadi, ndiponso mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zotsutsa.
j Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
k Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
l Mogwirizana ndi zimene zingachitikedi m’gawo la mpingo wanu, ndiponso ngati nthawi ingalole, sonyezani mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zosiyanasiyana, mmene tingatsimikizire kuti mfundo zathu n’zoonadi, ndiponso mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zotsutsa.
a Mogwirizana ndi zimene zingachitikedi m’gawo la mpingo wanu, ndiponso ngati nthawi ingalole, sonyezani mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zosiyanasiyana, mmene tingatsimikizire kuti mfundo zathu n’zoonadi, ndiponso mmene tingayankhire anthu amene ali ndi mfundo zotsutsa.
b Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
c Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.