Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/07 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 9/07 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kwambiri kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo wanu woyamba. Ngati mwininyumba ali nalo kale bukuli, mum’sonyeze mmene angapindulire nalo mwa kupanga naye mwachidule phunziro la Baibulo. October: Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani! Anthu akasonyeza chidwi, agawireni ndi kukambirana nawo za m’kapepala ka Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Chitani zimenezi ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. November: Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, gawirani kabuku kakuti Dikirani! December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire buku la Yandikirani kwa Yehova kapena la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

◼ Mwezi wa September ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.

◼ Mipingo iyambe kuitanitsa mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2007, Watch Tower Publications Index 2007 ndiponso Watchtower Library—2007 Edition ya pa CD-ROM pafomu yawo yotsatira yofunsira mabuku. Zinthu zimenezi zili m’Chingelezi. Kumbukirani kuti Watchtower Library—2007 Edition inakonzedwera anthu obatizidwa okha ndipo mungaiitanitse kudzera kumpingo basi.

◼ Nkhani ya onse yapadera ya nyengo ya Chikumbutso ya 2008 idzakambidwa mlungu woyambira March 31, 2008. Mutu wa nkhaniyi tidzaulengeza m’tsogolo muno. Mipingo imene idzakhale ikuchezeredwa ndi woyang’anira dera kapena idzakhale ndi msonkhano waukulu mlungu umenewo, idzakhale ndi nkhani yapaderayi mlungu wotsatira. Mpingo uliwonse usadzakhale ndi nkhani yapaderayi usanafike mlungu woyambira March 31, 2008.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo a miyezi ya June, July, ndi August. Mukatha kuwerengerako, lengezani ku mpingo pamodzi ndi lipoti lotsatira la maakaunti.—Onani Malangizo Oyendetsera Maakaunti a Mpingo (S-27).

◼ Nthawi zina ofesi ya nthambi imalandira Mafomu Ofunsira Mabuku (S-14) kapena Maoda a Mpingo (M-202) opanda dzina ndi nambala ya mpingo. Zimenezi zikachitika, n’zosatheka kutumiza mabuku kapena magazini omwe mipingo inaitanitsa pa mafomuwo. Tikufuna kukukumbutsani kuti mlembi ayenera kuonetsetsa kuti dzina ndi nambala ya mpingo zalembedwa pafomu asanaisaine ndi kuitumiza ku ofesi ya nthambi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena