Bokosi la Mafunso
◼ Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amavomereza magulu a Mboni odziimira paokha amene amasonkhana kuti afufuze n’kukambirana zinthu za m’Malemba?—Mat. 24:45, 47.
Ayi, savomereza. Komabe, kumadera ena, anthu angapo m’gulu lathu apanga magulu odziimira paokha kuti afufuze nkhani zokhudza Baibulo. Ena a maguluwo aphunzira za Chiheberi ndi Chigiriki cha m’Baibulo kuti afufuze ngati Baibulo la Dziko Latsopano linamasuliridwa molondola. Magulu ena amafufuza nkhani za sayansi zimene zimakhudza Baibulo. Maguluwo apanga malo a pa Intaneti kuti aike zinthu zawo ndiponso kuti agawane nzeru ndi anthu ena. Iwo apanga misonkhano ndiponso asindikiza mabuku n’cholinga choti aonetse zimene apezazo komanso kuti aziwonjezera pa zimene timaphunzira m’mabuku athu ndiponso ku misonkhano yathu yachikhristu.
Padziko lonse, anthu a Yehova akuphunzira zinthu zambiri zauzimu ndiponso akulimbikitsidwa kwambiri kudzera m’misonkhano ya mpingo, misonkhano yaikulu, ndiponso mabuku ofalitsidwa ndi gulu la Yehova. Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera ndi Mawu ake a choonadi kuti apereke zinthu zofunika n’cholinga choti anthu ake akhale “ogwirizana bwino lomwe pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi” ndiponso kuti apitirize “kukhazikika m’chikhulupiriro.” (1 Akor. 1:10; Akol. 2:6, 7) Ndithudi, timayamikira kwambiri zinthu zauzimu zimene Yehova amatipatsa m’masiku ano otsiriza. Choncho, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” savomereza mabuku, misonkhano, kapena malo a pa Intaneti amene sanakonzedwe motsogoleredwa ndi kapoloyo.—Mat. 24:45-47.
N’zoyenera kuti anthu azigwiritsa ntchito nzeru pofalitsa uthenga wabwino. Komabe, zinthu zimene iwo akuchita paokha siziyenera kusokoneza kapena kupeputsa zimene Yesu Khristu akuchita masiku ano kudzera mumpingo wake padziko lapansi. M’nthawi yake, mtumwi Paulo anachenjeza za kuononga nthawi pokambirana ndi kufufuza zinthu zotopetsa monga “mibadwo ya makolo. Zimenezi n’zosapindulitsa, koma zimangoyambitsa mafunso ofuna kufufuza ndiponso siziphunzitsa chilichonse chochokera kwa Mulungu chokhudza chikhulupiriro.” (1 Tim. 1:3-7) Akhristu onse aziyesetsa ‘kupewa mafunso opusa ndi kukumba mibadwo ya makolo ndi mikangano ndi kulimbana pa za Chilamulo, pakuti n’zosapindulitsa ndiponso n’zachabechabe.’—Tito 3:9.
Timalimbikitsa anthu amene akufuna kuphunzira ndi kufufuza mozama m’Baibulo kuti azigwiritsa ntchito mabuku a Insight on the Scriptures, “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” ndiponso zofalitsa zathu zina monga zimene zimafotokoza ulosi wa m’mabuku a m’Baibulo a Danieli, Yesaya, ndi Chivumbulutso. M’mabuku amenewa muli zambiri zochokera m’Baibulo zoti tiphunzire ndi kusinkhasinkha kuti tikhale “odziwa molondola bwino lomwe chifuniro [cha Mulungu], mu nzeru zonse ndi kumvetsetsa zinthu kwauzimu. Inde, kotero kuti [tiziyenda] moyenera Yehova ndi kum’kondweretsa kwathunthu, pamene [tipitiriza] kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino, ndi kuwonjezera kudziwa [kwathu] Mulungu molondola.”—Akol. 1:9, 10.