Lalikirani Mwakhama
1 Nthawi zina tingalalikire m’gawo lathu lonse mobwerezabwereza koma osapeza anthu achidwi. Ngakhale zitatero, tili ndi zifukwa zomveka zopitirizira kulalikira.—Mat. 28:19, 20.
2 Kuti Ukhale Umboni: Yesu analosera kuti ntchito yolalikira za Ufumu idzakhala mbali yofunika kwambiri ya chizindikiro cha “mapeto a dongosolo lino la zinthu,” ndiponso kuti ntchitoyi idzachitika ‘kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.’ (Mat. 24:3, 14) Umakhala umboni wamphamvu anthu akamationa tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Tikachoka m’gawolo anthu ena, ngakhale amene sanamvetsere uthenga wathu, angamanene za ulalikiwo kwa maola kapena masiku angapo. Kuzindikira chifukwa chimene tikuchitira utumikiwu kumatithandiza kuti tichite khama. Yehova amasangalala tikamagwira ntchito yolalikira pokwaniritsa ulosi wa m’Baibulo mwa kuchitira umboni ndiponso kupereka chenjezo.—2 Ates. 1:6-9.
3 M’pofunika Khama: Popeza kuti anthu ndi otanganidwa kwambiri ndipo pali zinthu zambiri zimene zimawasokoneza, m’pofunika khama kuti tiwathandize kupitirizabe kukhala ndi chidwi. Mwachitsanzo, Mboni zina zinakhala zikuyendera mayi wina mlungu ulionse ndipo panatenga chaka chathunthu kuti mayiyo aitanire Mbonizo m’nyumba mwake kuti akambirane za Baibulo. Mayiyu anasangalala kwambiri ndi zimene anamva moti anavomera kuti aziphunzira naye Baibulo, anayamba kupezeka pa misonkhano ndipo pasanapite nthawi yaitali anasonyeza chidwi chofuna kubatizidwa.
4 Maganizo a anthu akusintha chifukwa choti zinthu zambiri padzikoli zikusintha mofulumira. N’kutheka kuti anthu ambiri omwe anakana kumvetsera uthenga wathu m’mbuyomu, tsopano angakhale ndi chidwi chofuna kumva uthenga wolimbikitsa umene timalalikira. Ngakhale patapezeka munthu mmodzi yekha womvera uthenga wa Ufumu, ndiye kuti khama lathu lapindula.
5 Padziko lonse, anthu ambiri “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse” zimene zikuchitika. (Ezek. 9:4) Zotsatirapo za ntchito yolalikira zikusonyeza kuti anthu amaganizo oyenerera akumvera uthenga wa Ufumu. (Yes. 2:2, 3) Motero, tiyeni tipitirize kulalikira mwakhama “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”—Yes. 52:7; Mac. 5:42.