Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/08 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 6/08 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu June: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. July ndi August: Mungagwiritse ntchito kabuku kalikonse mwa timabuku tamasamba 32 iti: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo paulendo woyamba. Ngati eninyumba ali nalo kale bukuli, athandizeni kuona mmene angapindulire nalo mwa kuwasonyeza mwachidule mmene timachitira phunziro la Baibulo.

◼ Mwezi wa August ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.

◼ M’bale amene woyang’anira wotsogolera wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo a miyezi ya March, April ndi May. Mukatha kuwerengerako, lengezani ku mpingo pamodzi ndi lipoti lotsatira la maakaunti.—Onani Malangizo Oyendetsera Maakaunti a Mpingo (S-27).

◼ Ndi bwino kuti mafomu olembetsera upainiya wokhazikika azitumizidwa ku ofesi ya nthambi patatsala masiku osachepera 30 kuti lifike tsiku limene munthuyo wafuna kuyamba upainiyawo. Mlembi wa mpingo ayenera kuonetsetsa kuti mafomuwo alembedwa bwino malo onse. Ngati amene akufuna kuchita upainiyayo sakukumbukira tsiku limene anabatizidwa, angangolemba loyerekezera ndi kulisunga. Mlembi ayenera kulemba tsiku limeneli pa Khadi la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa (S-21).

◼ Kumbukirani izi: Tikulimbikitsanso mipingo kuti izitumiza malipoti awo a pamwezi mofulumira. Padakali malipoti ambiri a chaka chino chautumiki omwe sanatumizidwebe.

◼ Dziwani kuti sitidzakhala ndi timapepala tapadera toitanira anthu ku msonkhano wachigawo wa 2008. Komabe, tikukonza zoti m’tsogolo muno tidzakhale ndi ntchito ina yapadera padziko lonse. Tidzakudziwitsani zambiri zokhudza ntchitoyi m’tsogolomu.

◼ Nyimbo zotsatirazi zidzaimbidwa pa msonkhano wachigawo wa chaka chino: 3, 4, 8, 10, 42, 46, 57, 79, 98, 123, 157, 163, 190, 191, 207, 209, 212, ndi 215. Kuti anthu adzathe kuimba bwinobwino nyimbozi, tikulimbikitsa mipingo yonse kuphunzira nyimbo imodzi kapena ziwiri pambuyo pa misonkhano.

◼ Zofalitsa Zimene Zidakalipobe:

Learn From the Great Teacher—On Audiocassette (cslr-E)—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena