Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 30, 2008. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya May 5 mpaka June 30, 2008. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30.
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi tingatani kuti anthu azimvetsa mafanizo amene timanena? [be-CN tsa. 242 ndime 3 mpaka 243 ndime 1]
2. N’chifukwa chiyani mafanizo osavuta kumva a zinthu zodziwika bwino amagwira mtima? [be-CN tsa. 245 ndime 2 mpaka 4]
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito bwino zinthu zooneka, ndipo kodi Yehova anagwiritsa ntchito motani zinthu zooneka popereka maphunziro ofunika kwambiri? (Gen. 15:5; Yer. 18:6; Yona 4:10, 11) [be-CN tsa. 247 ndime 1 ndi 2]
4. Kodi tingatani kuti tigwiritse ntchito bwino zinthu zooneka pophunzitsa? [be-CN tsa. 248 ndime 1 mpaka 3]
5. Kodi tingatani kuti tigwiritse ntchito bwino mapu pophunzitsa anthu Baibulo? [be-CN tsa. 248 ndime 4]
NKHANI NA. 1
6.L Kodi kuphunzira Baibulo kungatithandize kuzindikira chiyani mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu? [be-CN tsa. 32 ndime 3 ndi 4]
7. Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji Baibulo lenilenilo pofufuza tanthauzo la lemba? [be-CN tsa. 34 ndime 4 mpaka tsa. 35 ndime 2]
8. N’chifukwa chiyani masiku ano pali ntchito yaikulu kwambiri muutumiki wakumunda? [od-CN tsa. 109 ndime 2]
9. Kodi munthu amayamba liti kulalikira nyumba ndi nyumba kuuza ena uthenga wabwino? [od-CN tsa. 110 ndime 1]
10. Kodi nthawi zambiri ndi zinthu zotani zimene munthu angachite pokonza autilaini? [be-CN tsa. 39 mpaka 41]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi kachisi amene “anam’manga zaka 46 ndi uti”? (Yoh. 2:20) [w08-CN 4/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Yohane”]
12. Kodi ndani amene ‘amachoka ku imfa kuwolokera ku moyo’? (Yoh. 5:24, 25) [w08-CN 4/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Yohane”]
13. Kodi n’chiyani chimene chinali chatsopano m’lamulo la pa Yohane 13:34? [Onani w90-CN 2/1 tsa. 21 ndime 5 ndi 6]
14. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anauza Mariya Mmagadala kuti asamukangamire? (Yoh. 20:17) [w08-CN 4/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Yohane”]
15. Kodi mawu akuti Yesu adzabwera “m’njira yofanana” ndi imene anakwerera kumwamba, amatanthauza chiyani? (Mac. 1:9-11) [rs-CN tsa. 163 ndime 3]