Zimene Tingachite Tikapeza Mwininyumba Wolankhula Chinenero China
1. N’chifukwa chiyani m’pofunika kuchita zinthu mwadongosolo polalikira m’magawo ena?
1 Nthawi zambiri, ofalitsa Ufumu padziko lonse amapeza anthu achidwi amene amalankhula chinenero chomwe si cha mpingo wawo. Pofuna kuthandiza anthu amenewa mwauzimu, maofesi ambiri anthambi aona kuti ndi bwino kukhazikitsa magulu ndiponso mipingo ya zinenero zina. Popeza kuti m’dera limodzi mungathe kumalankhulidwa zinenero zingapo, mipingo ya zinenero zosiyanasiyana ingathe kumalalikira m’gawo limodzi. Kodi mipingo yotereyi ingatani pofuna kuonetsetsa kuti ntchito yolalikira ikuchitika mwadongosolo?—1 Akor. 14:33.
2. Tikamalalikira nyumba ndi nyumba, kodi tingagwire bwanji ntchitoyo mogwirizana ndi gulu kapena mpingo wa chinenero china?
2 M’pofunika Kugwirizana: Pochita ulaliki wa mumsewu kapena polalikira mwamwayi, ofalitsa ali ndi ufulu wolalikira munthu aliyense ngakhale wolankhula chinenero china, ndipo angagawire mabuku a chinenero chimene munthuyo angakonde. Komabe, tikamalalikira nyumba ndi nyumba m’gawo limene gulu kapena mpingo wa chinenero china umalalikira, tiyenera kulalikira makamaka anthu amene amalankhula chinenero cha mpingo wathu. Ngati mipingo ingapo imalalikira m’gawo limodzi, m’pofunika kuchita zinthu mwadongosolo. Oyang’anira utumiki a mipingo imeneyi ayenera kukambirana ndi kugwirizana za mmene angamagwirire ntchito yolalikira m’gawolo. (Miy. 11:14) Komabe, ngati polalikira nyumba ndi nyumba tapeza munthu wolankhula chinenero china ndipo palibe mpingo wapafupi wa chinenero chimenecho, tiyenera kuyesetsabe kumulalikira ndi kumuthandiza mwauzimu.
3. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati takumana ndi gulu kapena mpingo wa chinenero china m’dera limene tikulalikira?
3 Ntchito Yathu ndi Yofanana: Kodi m’pofunika kuchita chiyani ngati mipingo yolankhula zinenero zosiyana ikulalikira m’dera limodzi panthawi yofanana? Pamenepa, chikondi chachikhristu chingathandize anthu amene akulalikirawo kuchita zinthu zothandiza anthu a m’deralo, m’malo moganizira za kusiyana kwa zinenero. (Yoh. 13:34, 35) Motero, amene akutsogolera maguluwo ayenera kuchita zinthu mololerana ndiponso mwachikondi pogwirizana zoti gulu limodzi lichoke m’deralo n’kukalalikira kwina.—Yak. 3:17, 18.
4. Kodi ndi ulosi wotani umene ukukwaniritsidwa masiku ano?
4 Baibulo linalosera kuti anthu a zinenero zosiyanasiyana adzamva uthenga wabwino. (Chiv. 14:6, 7) Kuchita zinthu mogwirizana kungatithandize kuti tisalalikire m’dera limodzi panthawi yofanana. Zimenezi zingathandize kuti anthu ambiri kuphatikizapo anthu olankhula chinenero china amve uthenga wabwino.—Aef. 4:16.