Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda June 1
“Kodi mukuganiza kuti Mulungu amavomereza zipembedzo zonse? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Mulungu ananena Aisiraeli atatengera miyambo ya zipembedzo za mitundu ina. [Werengani Ezekieli 6:6.] Nkhani iyi ikuyankha funso lakuti: ‘Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kulikonse?’” M’sonyezeni nkhani yomwe yayambira patsamba 9.
Galamukani! June
“Mosakayikira, mungavomereze kuti zimakhala zovuta kwa mwana ndiponso makolo ake, makamaka mwanayo akamasinkhuka. Kodi mukuganiza kuti malangizo awa angathandize makolo kulera bwino ana awo? [Werengani Yakobe 1:19. Ndiyeno, yembekezani ayankhe.] Musangalala kwambiri ndi mfundo zabwino zochokera m’Baibulo zomwe zili m’magazini iyi.”
Nsanja ya Olonda July 1
“Tonsefe tinavutikapo ndi chisoni munthu amene tinali kumukonda atamwalira. Panthawi yotereyi, kodi mukuganiza kuti Baibulo lingatithandize? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Salmo 55:22.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingatilimbikitse.”
Galamukani! July
“Anthu a pabanja akukumana ndi mavuto ochuluka ndipo ambiri akumasudzulana. Kodi mukuganiza kuti kutsatira malangizo awa kungathandize kuti ukwati uziyenda bwino? [Werengani Miyambo 12:18. Kenako, yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ili ndi mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize anthu a pabanja kuti akhale ndi ukwati wolimba.”